Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAO 2

Kodi Mulungu Woona Ndani?

Kodi Mulungu Woona Ndani?

Pali Mulungu woona mmodzi cabe, ndipo dzina lake ni Yehova. (Salimo 83:18) Iye ni Mzimu, sitingamuone. Amatikonda ndipo amafuna kuti ife tizimukonda. Amafunanso kuti tizikonda anthu anzathu. (Mateyu 22:35-40) Iye ni Wamphamvuyonse, ni Mlengi wa zinthu zonse.

Pa zolengedwa zake zonse, Mulungu anayambilila kulenga mngelo mmodzi wamphamvu. Mngelo ameneyo ndiye anabwela kukhala Yesu Kristu. Pambuyo pake Yehova analenga angelo ena.

Yehova analenga zinthu zonse za kumwamba . . . ndi za padziko lapansi. Chivumbulutso 4:11

Yehova analenga nyenyezi, dziko lapansi, ndi zonse za padziko.—Genesis 1:1.

Anaumba Adamu, munthu woyamba, ndi dothi lapansi.—Genesis 2:7.