Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAO 3

Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?

Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?

Yehova anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zabwino zambili. Genesis 1:28

Yehova anapanga Hava, mkazi woyamba, ndipo anamupeleka kwa Adamu kuti akhale mkazi wake.—Genesis 2:21, 22.

Yehova anawalenga ndi maganizo ndi matupi angwilo, opanda coipa ciliconse.

Mudzi wao unali munda wa Edeni, ndipo malo ake anali okongola. Munali mitsinje, mitengo ya zipatso, ndi nyama.

Yehova anali kukamba nao ndi kuwaphunzitsa. Ngati anamvetsela kwa iye, akanakhala ndi moyo wamuyaya m’Paladaiso padziko lapansi.

Mulungu anawaletsa kudya mtengo umodzi cabe. Genesis 2:16, 17

Yehova anaonetsa Adamu ndi Hava mtengo umodzi wa zipatso umene unali m’munda ndipo anawauza kuti ngati adzadya umenewo, adzafa.

Mngelo wina anapandukila Mulungu. Mngelo woipa ameneyo ni Satana Mdyelekezi.

Satana sanafune kuti Adamu ndi Hava amvele Yehova. Conco anaseŵenzetsa cinjoka kuuza Hava kuti akadya cipatso ca mtengo umenewo, sadzafa, koma adzakhala ngati Mulungu. Ili linali bodza.—Genesis 3:1-5.