CHIGAWO 4 Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana? YAMBANI Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana? Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, choncho anafa. Genesis 3:6, 23 Hava anamvera njoka ndipo anadya chipatso cha mtengo woletsedwawo. Atatero, anatengako chipatso china n’kukapatsa mwamuna wake Adamu, ndipo iyenso anadya. Zimene anachitazo zinali zolakwika chifukwa linali tchimo. Zitatero Mulungu anawathamangitsa m’Paradaiso mmene iwo ankakhala. Iwo pamodzi ndi ana awo anayamba kukhala moyo wovutika kwambiri. Kenako, iwo anakalamba n’kufa. Iwo atafa, sanapite kudziko lamizimu ayi, chifukwa mwa munthu mulibe chilichonse chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira. Munthu akafa amangokhala ngati fumbi. Genesis 3:19 Tonsefe timafa chifukwa ndife ana a Adamu ndi Hava. Anthu akufa sangathe kuchita chilichonse monga kumva kapena kuona.—Mlaliki 9:5, 10 Sichinali cholinga cha Yehova kuti anthu azifa. Choncho, posachedwapa iye adzaukitsa anthu onse amene anamwalira. Anthu amenewo akadzamvera Mulungu, adzakhala ndi moyo wosatha. Yam'mbuyo Yotsatira Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira? Baibulo limanena kuti kutsogoloku anthu ambiri adzaukitsidwa ngati mmene zinakhalira ndi Lazaro. ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? Anthu ambiri amafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri. Baibulo limapereka yankho logwira mtima pa nkhaniyi. KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI? Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso Mulungu atapereka chilango kwa Adamu ndi Hava chifukwa cha kusamvera kwawo, kodi anatani kuti apatse anthu chiyembekezo? Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana? MVERANI MULUNGU KUTI MUDZAPEZE MOYO WOSATHA Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana? Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana? https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/e781f8601f/images/syn_placeholder_sqr.png