Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 5

Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?

Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?

Anthu ambiri m’nthawi ya Nowa ankachita zinthu zoipa. Genesis 6:5

Adamu ndi Hava anabereka ana, ndipo anthu anachuluka padziko lapansi. Patapita nthawi, angelo ena anagwirizana ndi Satana n’kugalukira Mulungu.

Angelowo anabwera padziko lapansi n’kuvala matupi a anthu n’cholinga choti akwatire akazi. Akaziwo anabereka ana achilendo amene anali oopsa ndiponso amphamvu.

Dziko linadzaza ndi anthu ochita zoipa. Baibulo limati, ‘kuipa kwa anthu kunachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.’

Nowa anamvera Mulungu ndipo anapanga chingalawa. Genesis 6:13, 14, 18, 19, 22

Nowa anali munthu wabwino ndipo Yehova anamuuza kuti awononga anthu oipa ndi chigumula.

Mulungu anauzanso Nowa kuti apange chingalawa chachikulu kuti iye ndi banja lake pamodzi ndi nyama za mtundu uliwonse alowemo.

Nowa anachenjeza anthu kuti kukubwera Chigumula, koma anthuwo sanamvere. Ena ankamuseka ndipo ena ankadana naye.

Nowa atamaliza kupanga chingalawacho, analowetsamo nyama.