Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAO 6

Kodi Cigumula ca Nowa Cimatiphunzitsa Ciani?

Kodi Cigumula ca Nowa Cimatiphunzitsa Ciani?

Mulungu anaononga anthu oipa koma anapulumutsa Nowa ndi banja lake. Genesis 7:11, 12, 23

Kunagwa mvula masiku 40 usana ndi usiku, ndipo dziko lonse lapansi linamila. Anthu onse oipa anafa.

Angelo opanduka anasiya matupi awo aumunthu ndi kukhala viŵanda.

Anthu amene anali m’cingalawa anapulumuka. M’kupita kwa nthawi Nowa ndi banja lake anafa, koma Mulungu adzawaukitsa ndipo adzakhala ndi ciyembekezo ca moyo wamuyaya.

Mulungu adzaononganso anthu oipa ndi kupulumutsa abwino. Mateyu 24:37-39

Satana ndi viŵanda vake akali kusokoneza anthu.

Masiku ano, monga m’nthawi ya Nowa, anthu ambili amakana malangizo acikondi a Yehova. Posacedwa Yehova adzaononga anthu onse oipa.—2 Petulo 2:5, 6.

Anthu ena ali ngati Nowa. Iwo amamvetsela kwa Mulungu ndi kucita zimene iye amakamba; anthu amenewo ni Mboni za Yehova.