Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 8

Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani bwanji?

Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani bwanji?

Yesu anafa kuti ife tikhale ndi moyo. Yohane 3:16

Patapita masiku atatu Yesu atamwalira, amayi ena anapita kumanda ake ndipo sanapezeko kanthu. Yehova anali ataukitsa Yesu.

Kenako Yesu anaonekera kwa atumwi ake.

Inde, Yehova anaukitsa Yesu kuti akhale mngelo wamphamvu ndipo anam’patsa moyo umene sungafe. Ophunzira a Yesu anamuona pamene iye ankapita kumwamba.

Mulungu anaukitsa Yesu ndipo anamuika kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Danieli 7:13, 14

Yesu anapereka moyo wake dipo kuti awombole anthu. (Mateyu 20:28) Kudzera mu dipo limenelo, Mulungu wakonza zoti tidzakhale ndi moyo wosatha.

Yehova anasankha Yesu kukhala Mfumu kuti alamulire dziko lapansi. Iye adzalamulira limodzi ndi anthu okhulupirika okwanira 144,000 amene amaukitsidwa kuchokera padziko lapansi kupita kumwamba. Yesu pamodzi ndi anthu 144,000 amenewo adzalamulira m’boma lakumwamba, kapena kuti, Ufumu wa Mulungu.​—Chivumbulutso 14:1-3.

Ufumu wa Mulungu udzabweretsa paradaiso padziko lapansi. Ndipo sipadzakhalanso nkhondo, chiwawa, umphawi ndiponso njala. Anthu adzakhala osangalala kwambiri.—Salimo 145:16.