Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAO 8

Kodi Tingapindule Bwanji Ndi Imfa ya Yesu?

Kodi Tingapindule Bwanji Ndi Imfa ya Yesu?

Yesu anafa kuti tikapeze moyo. Yohane 3:16

Patapita masiku atatu kucokela pamene Yesu anafa, akazi ena anapita kumanda amene anamuikamo ndipo anapeza mulibe. Iwo anapeza kuti Yehova waukitsa Yesu kwa akufa.

Pambuyo pake Yesu anaonekela kwa atumwi ake.

Inde, Yehova anaukitsa Yesu kukhala mngelo wamphamvu, amene sakhoza kufa. Ophunzila ake anamuona akupita kumwamba.

Mulungu anaukitsa Yesu ndi kumuika kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Danieli 7:13, 14

Yesu anapeleka moyo wake kukhala dipo la anthu onse. (Mateyu 20:28) Cifukwa ca dipo limenelo, Mulungu watipatsa mwai wakuti tikhale ndi moyo wamuyaya.

Yehova anasankha Yesu kukhala Mfumu ya dziko lapansi. Iye adzalamulila pamodzi ndi anthu okhulupilika okwanila 144,000 amene amaukitsidwa kucoka padziko kupita kumwamba. Yesu ndi a 144,000 amapanga boma la kumwamba lolungama—Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 14:1-3.

Ufumu wa Mulungu udzasandutsa dziko lapansi kukhala paladaiso. Nkhondo, upandu, kusauka, ndi njala zidzatha. Anthu adzakondwela kwambili.—Salimo 145:16.