Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

Mutu 1

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

“Nkhani inayake itachitika, ndinayesetsa kwambiri kufotokozera makolo anga mmene ndinkamvera, koma ankangondidula mawu. Zinali zovuta kwambiri kuti ndilimbe mtima n’kuwauza mmene ndinkamvera, koma ngakhale kuti ndinayesetsa sizinathandize ngakhale pang’ono.”​—Anatero Rosa.

N’KUTHEKA kuti muli mwana munkakonda kufunsa zinthu kwa makolo anu. Munkawauza chilichonse, ndi nkhani yaing’ono yomwe. Munkawafotokozera momasuka zakukhosi kwanu ndipo munkaona kuti malangizo awo ndi othandiza.

Koma mwina masiku ano mumaona kuti makolo anu samakumvetsetsani. Mtsikana wina, dzina lake Edie, anati: “Tsiku lina tikudya chakudya chamadzulo ndinayamba kufotokoza mmene ndikumvera kwinaku ndikulira. Makolo anga ankamvetsera koma ankaoneka kuti sankandimvetsetsa.” Kenako mtsikanayu anafotokoza kuti: “Ndinangopita kuchipinda kwanga n’kukapitiriza kulira.”

Achinyamata ambiri amaonanso kuti ndi bwino kubisira makolo awo nkhani zina. Mnyamata wina, dzina lake Christopher, anati: “Ndimauza makolo anga nkhani zambiri, koma pali nkhani zina zimene sindimawauza.”

Kodi n’kulakwa kubisira makolo anu nkhani zina? Nthawi zina sikulakwa, bola ngati simukuchita zachiphamaso. (Miyambo 3:32) Komabe, kaya makolo anu amaoneka kuti sakumvetsetsani kapena inuyo simufuna kuwauza zinthu zina, dziwani mfundo iyi: Mwana amafunika aziuza makolo ake mmene akumvera ndipo makolo ayenera kumvetsera mwanayo akamalankhula.

Musaleke Kulankhula Nawo

Kulankhula ndi makolo anu tingakuyerekezere ndi kuyendetsa galimoto ndipo mavuto amene amalepheretsa kulankhulana tingawayerekezere ndi chikwangwani chosonyeza kuti msewu watsekedwa. Ngati mutapeza chikwangwani chosonyeza kuti msewu watsekedwa, simungabwerere koma mukhoza kungodzera msewu wina. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi:

VUTO LOYAMBA Inuyo mukufuna kulankhula ndi makolo anu, koma akuoneka ngati sakumvetsera. Mtsikana wina, dzina lake Leah, anati: “Zimandivuta kulankhulana ndi bambo anga. Nthawi zina ndimatha kuwafotokozera zinthu zambiri, koma kenako amanena kuti, ‘Pepa, kodi umalankhula ndi ine?’”

FUNSO: Kodi Leah angatani ngati akufuna kuuza bambo ake vuto linalake? Pali njira zitatu zomwe angatsatire.

Njira Yoyamba

Akhoza kuwalusira bambo ake. Leah akulankhula mokalipa kuti: “Tamvetserani zimene ndikufuna ndikuuzenizi! Nkhani yake ndi yofunikatu!”

Njira Yachiwiri

Akhoza kusiya kulankhula nawo. Leah akusiya kulankhula ndi bambo ake.

Njira Yachitatu

Akhoza kudikira kuti alankhule ndi bambo akewo nthawi ina. Leah akudikira kaye kuti alankhule ndi bambo akewo nthawi ina kapena akuwalembera kalata yofotokoza vuto lakelo.

Kodi inuyo mukuganiza kuti Leah asankhe njira iti? ․․․․․

Tiyeni tikambirane njira iliyonse kuti tione zotsatira zake.

Bambo a Leah atanganidwa ndi zinthu zina zomwe zachititsa kuti asadziwe zoti mwana wawoyo wakhumudwa. Choncho ngati Leah atasankha Njira Yoyamba, bambo akewo sangamvetse zimene zachititsa kuti mwana wawoyo aluse. Ndipo kuchita zimenezi sikungapangitse kuti bambo akewo amumvetsere komanso zingasonyeze kuti samawalemekeza. (Aefeso 6:2) Choncho, njira imeneyi singathandize ngakhale pang’ono.

Njira Yachiwiri ingakhale yosavuta koma si yothandiza. Tikutero chifukwa chakuti “zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.” (Miyambo 15:22) Kuti athetse vuto lakelo Leah akufunika kulankhulana ndi bambo ake koma n’zovuta kuti bambo akewo amuthandize ngati sakudziwa zimene zikumuchitikira. Choncho, kusiya kulankhula nawo n’kosathandiza.

Njira Yachitatu, Leah sanasankhe kungosiya kulankhula ndi bambo ake chifukwa chakuti sakumumvetsera. M’malomwake iye waona kuti ndi bwino kuti alankhule nawo nthawi ina. Ndipo kulembera kalata bambo akewo kungamuthandize kumvako bwino, ngakhale asanamuyankhe. Komanso kulemba kalata kungamuthandize kuti afotokoze bwino vuto lakelo komanso mwaulemu. Bambo ake akawerenga kalatayo akhoza kudziwa zimene mwana wawo akufuna kuwafotokozera, zomwe zingawathandize kumvetsa vuto lakelo. Choncho njira yachitatuyi ingathandize Leah komanso bambo ake.

Kodi pali njira zinanso zimene Leah angatsatire? Ganizirani njira imodzi ndipo ilembeni m’munsimu. Kenako lembani zimene zingachitike atatsatira njira imeneyi.

․․․․․

VUTO LACHIWIRI Makolo anu akufuna kulankhula nanu koma inuyo simukufuna. Mtsikana wina, dzina lake Sarah, anati: “Palibe chimandikwana kwambiri ngati kufunsidwa mafunso ambirimbiri pambuyo poti ndatopa ndi za kusukulu. Ndimafuna kuiwalako za kusukulu koma nthawi yomweyo makolo amandifunsa kuti, ‘Waswera bwanji? Kusukulu kunali bwanji?’” Makolo a Sarah ayenera kuti amafunsa mafunso amenewa chifukwa choti amamukonda. Koma iye amadandaula kuti, “Sindimafuna kulankhula za kusukulu ndikatopa.”

FUNSO: Kodi Sarah angatani? Mofanana ndi chitsanzo choyamba chija, pali njira zitatu zimene angatsatire.

Njira Yoyamba

Asalankhule nawo. Sarah anene kuti: “Ndisiyeni, sindikufuna zolankhula.”

Njira Yachiwiri

Alankhulebe nawo ngakhale asakufuna. Ngakhale kuti wakhumudwa, Sarah akuyankhabe zimene makolo akewo afunsa koma monyinyirika.

Njira Yachitatu

Asinthe nkhani, m’malo mokamba za kusukulu ayambitse nkhani ina. Sarah waona kuti ndi bwino kusiya kaye nkhani za kusukulu kuti adzakambirane nthawi ina maganizo ake atakhala m’malo. Kenako akunena kuti: “Ndaswera. Kaya inuyo tsiku lanu linali bwanji?”

Kodi inuyo mukuganiza kuti Sarah asankhe njira iti? ․․․․․

Tiyeni tikambiranenso njira iliyonse kuti tione zotsatira zake.

Sarah watopa ndipo sakufuna zolankhula. Ndiye ngati atasankha Njira Yoyamba, sizingasinthe chilichonse chifukwa angakhalebe wotopa komanso angamadziimbe mlandu chifukwa choti anawalusira makolo akewo.​—Miyambo 29:11.

Makolo a Sarah sangasangalale ngati mwana wawo atasiya kulankhula nawo komanso akhoza kukhumudwa ngati atawalusira. Iwo akhoza kuganiza kuti pali chinachake chimene mwana wawoyo akuwabisira. Ndipo angayesetse kwambiri kukakamiza mwana wawoyo kuti afotokoze zimene zili kukhosi kwake, zomwe zingamuchititse kuti akhumudwe kwambiri. Choncho, njira imeneyi singathandize makolowo komanso mwanayo.

Njira Yachiwiri ndi yabwinoko poyerekeza ndi njira Yoyamba. Tikutero chifukwa onse akulankhulana. Komabe, kulankhulana kwawo n’kosathandiza chifukwa akungolankhula modzikakamiza.

Koma Njira Yachitatu ndi yothandiza kwa Sarah chifukwa akusintha nkhaniyo n’kuyambitsa nkhani ina. Ndipo makolo ake angasangalale kwambiri kuti wayesetsa kulankhula nawo. Njira imeneyi ingathandize kwambiri chifukwa aliyense akuyesetsa kutsatira mfundo ya pa Afilipi 2:4 yakuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”

Muzisamala Ndi Zimene Makolo Anu Angaganize

Dziwani kuti nthawi zina zimene makolo anu angamve zingakhale zosiyana ndi zimene inuyo mwanena. Mwachitsanzo, ngati makolo anu atakufunsani kuti mwakwiya chifukwa chiyani, mungayankhe kuti, “Sindikufuna kuti tikambirane nkhani imeneyi.” Makolo anu angaganize kuti mukutanthauza kuti: “Sindikukhulupirirani ndiye sindingakuuzeni. Kulibwino ndikauze anzanga m’malo mouza inuyo.” Lembani zimene mukuganiza m’munsimu. Yerekezani kuti mwakumana ndi vuto linalake ndipo makolo anu akufuna kukuthandizani.

Ngati mutayankha makolo anu kuti: “Musadandaule. Ndithana nalo ndekha vuto limeneli.”

Makolo anu angaganize kuti mukunena kuti: ․․․․․

Njira yabwino ndi kunena kuti: ․․․․․

Koma mfundo yofunika kwambiri yomwe muyenera kuikumbukira ndi yakuti: Muziyamba mwaganiza kaye musanalankhule ndipo muzilankhula mwaulemu. (Akolose 4:6) Muziona makolo anu ngati anzanu, osati ngati adani anu. Ndipotu mumafunika kukhala ndi anthu amene angakuthandizeni kuti muthane ndi mavuto onse amene mungakumane nawo.

M’MUTU WOTSATIRA

Koma bwanji ngati nthawi iliyonse mukamalankhula ndi makolo anu mumakangana?

LEMBA

“Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga, ndipo milomo yanga imanena nzeru moona mtima.”​—Yobu 33:3.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati mumaona kuti mumavutika kukambirana ndi makolo anu za vuto linalake mutakhala pansi, mukhoza kukambirana nawo poyenda, mukamapita kwinakwake pa galimoto kapena pokagula zinthu.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngati inuyo mumavutika kukambirana ndi makolo anu nkhani zinazake, dziwani kuti nawonso amavutika komanso samasuka kukambirana nanu nkhani zomwezo.

ZOTI NDICHITE

Ulendo wotsatira ndikadzakhala kuti sindikufuna kulankhula ndi makolo anga, ndidzachita izi: ․․․․․

Makolo anga akadzandikakamiza kulankhula nawo nkhani inayake imene siikundisangalatsa ndidzanena kuti: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi: ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kusankha nthawi yabwino yolankhulirana n’kofunika motani?​—Miyambo 25:11.

● N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kulankhula ndi makolo anu?​—Yobu 12:12.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

“Nthawi zina kulankhula ndi makolo kumakhala kovuta, koma ukamayesetsa kulankhulana nawo umamva kupepukidwa mumtima.”​—Anatero Devenye

[Chithunzi patsamba 8]

Msewu ukatsekedwa mukhoza kupeza njira ina imene mungadutse. N’zothekanso kupeza njira yolankhulirana ndi makolo anu