Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndine Wokonzeka Kusamuka N’kumakakhala Ndekha?

Kodi Ndine Wokonzeka Kusamuka N’kumakakhala Ndekha?

Mutu 7

Kodi Ndine Wokonzeka Kusamuka N’kumakakhala Ndekha?

“Nthawi zina ndimaganiza kuti anthu amandiderera chifukwa chakuti ndili ndi zaka 19 koma ndikukhalabe ndi makolo anga. Ndikuona kuti adzayamba kundiona kuti ndine wamkulu ndikadzayamba kukhala pandekha.”​—Anatero Katie.

“Ndili ndi zaka pafupifupi 20 koma ndilibe ufulu wochita zimene ndimafuna chifukwa choti ndidakali pakhomo pa makolo anga. Moti nthawi ina ndinaganizapo zokakhala pandekha.”​—Anatero Fiona.

N’KUTHEKA kuti panopo mumafuna kuchita zinthu panokha ngakhale kuti mudakali pakhomo pa makolo anu. Mwachibadwa munthu aliyense amafuna kuchita zinthu zina payekha. Ndipotu Mutu 3, unafotokoza kuti cholinga cha Mulungu n’choti ana akule kenako achoke pakhomo pa makolo awo n’kukayamba banja lawo. (Genesis 2:23, 24; Maliko 10:7, 8) Koma kodi mungadziwe bwanji kuti muli wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu? Tiyeni tikambirane mafunso atatu omwe mufunika kuwaganizira. Loyamba ndi lakuti . . .

Kodi Cholinga Changa N’chiyani?

Onani mayankho ali m’munsiwa ndipo muwaike manambala potengera zifukwa zomwe mukufuna kuchokera pakhomo.

․․․․․ Ndikufuna kuthawa mavuto amene ali pakhomopo

․․․․․ Ndikufuna ndizikhala ndi ufulu wopanga zomwe ndikufuna

․․․․․ Ndikufuna kuti anzanga azindipatsa ulemu

․․․․․ Ndikufuna ndimuthandize mnzanga yemwe akusowa wokhala naye

․․․․․ Ndikufuna ndipite kwinakwake kuti ndikagwire ntchito yongodzipereka

․․․․․ Ndikufuna ndiphunzire kukhala pandekha

․․․․․ Ndikufuna kuti makolo anga apume kundisamalalira

․․․․․ Zina ․․․․․

Zifukwa zimene zili pamwambazi sizolakwika kwenikweni. Koma nkhani ndi yakuti, Kodi cholinga chanu n’chiyani? Mwachitsanzo, ngati mukufuna kuchoka kuti muzikangochita zilizonse zomwe mukufuna, mukadabwa kwambiri ndi zimene mukakumane nazo.

Mtsikana wina, dzina lake Danielle, anachoka pakhomo pa makolo ake ali ndi zaka 20 koma kenako anabwereranso. Iye anaphunzirapo kanthu pa zimene anakumana nazo ndipo ananena kuti: “N’zosatheka kuti munthu uzichita chilichonse chomwe ukufuna. Ukamakhala pawekha ntchito imene umagwira komanso kuchepa kwa ndalama zimene umapeza kumapangitsa kuti uzilephera kuchita zinthu zina.” Mtsikana wina, dzina lake Carmen, yemwe anapita kukakhala kudziko lina kwa miyezi 6 anati: “Ndinkasangalala kukhala pandekha komabe nthawi zambiri ndinkapanikizika. Ndinkakhala ndi ntchito zambiri zapakhomo monga kukonza m’nyumba, kukonza zinthu zomwe zawonongeka, kukonza panja, kuchapa zovala komanso ntchito zina zambiri.”

Musamapupulume kusamuka chifukwa cha zimene anthu ena akunena. (Miyambo 29:20) Ngakhale patakhala zifukwa zomveka zochokera pakhomo pa makolo anu ndi bwino kudikira kaye mpaka mutaphunzira zinthu zimene zingakuthandizeni kukakhala panokha bwinobwino. Zimenezi zikutifikitsa pa funso lachiwiri lakuti . . .

Kodi Ndine Wokonzeka Kukakhala Pandekha?

Kuchoka pakhomo pa makolo anu kuli ngati kupita kuchipululu nokhanokha. Kodi mungayende m’dera loterolo musakudziwa kukunga tenti, kuyatsa moto, kuphika kapena kudziwa kugwiritsa ntchito mapu? N’zokayikitsa. Komatu achinyamata ambiri amachoka pakhomo pa makolo awo atangophunzira zinthu zochepa zowathandiza kukhala paokha.

Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Kuti mudziwe ngati muli wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu, ganizirani mfundo zotsatirazi. Ikani chizindikiro ichi pa luso lomwe mwaphunzira kale ndipo ikani chizindikiro ichi X pa luso lomwe mukufunika kuphunzira.

Kusunga ndalama: Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Serena, ananena kuti: “Chiyambire, makolo anga akhala akundilipilira chilichonse. Ndimaopa kuchoka pakhomo pa makolo anga chifukwa sindidziwa kupanga bajeti.” Kodi mungaphunzire bwanji kugwiritsa ntchito ndalama mwanzeru?

Baibulo limati: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.” (Miyambo 1:5) Mungachite bwino kufunsa makolo anu kuti akufotokozereni ndalama zimene munthu mmodzi angawononge pa mwezi polipirira lendi, kugula chakudya, kulipirira thiransipoti kapena zinthu zina. Ndiyeno pemphani makolo anuwo kuti akuphunzitseni kupanga bajeti komanso kulipira zina ndi zina. *

Ntchito zapakhomo: Mnyamata wina wazaka 17, dzina lake Brian, ananena kuti amaopa kuchoka pakhomo pa makolo ake chifukwa safuna kuti azikachapa yekha. Kodi mungadziwe bwanji kuti mungathe kukhala nokha bwinobwino? Mnyamata wina wazaka 20, dzina lake Aron, ananena mfundo yomwe akuiona kuti ndi yothandiza. Iye anati: “Yesani kuchita zinthu zonse panokha kwa mlungu umodzi. Muzidya zakudya zomwe mwagula ndi ndalama zanu komanso zoti mwaphika nokha. Muzivala zovala zomwe mwachapa komanso kusita nokha. Muzigwira ntchito zonse zapakhomo. Ngati mukufuna kupita kwinakwake yendani nokha ndipo musapemphe ndalama ya thiransipoti.” Kutsatira mfundo zimenezi kungakuthandizeni kuti: (1) mukhale ndi maluso ofunikira komanso (2) muziyamikira kwambiri zimene makolo anu amakuchitirani.

Muzikhala bwino ndi anthu ena: Kodi mumakhala bwinobwino ndi makolo komanso abale anu? Ngati zimavuta kukhala nawo bwinobwino mwina mungaone kuti zingakhale bwino mutangosamuka n’kumakakhala ndi anzanu. Koma taganizirani zimene mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Eve ananena. Iye anati: “Anzanga ena awiri omwe ankagwirizana kwambiri anayamba kukhala nyumba imodzi. Koma anali osiyana chifukwa wina ankachita zinthu mwadongosolo pomwe winayo anali wauve. Wina ankakonda kwambiri zinthu zauzimu pomwe winayo sankazikonda, moti sanapitirize kukhalira limodzi.”

Ndiye mungatani kuti muzikhala bwino ndi anthu ena? Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Erin, ananena kuti: “Mukhoza kuphunzira mmene mungakhalire ndi anthu ena mukadali pakhomo pa makolo anu. Mumaphunzira mmene mungathetsere mavuto komanso kukhala wololera. Ndimaona kuti anthu amene amachoka pakhomo pa makolo awo chifukwa chakuti akufuna kupewa kukangana ndi makolo awo, saphunzira kuthetsa mavuto.”

Kuchita zinthu zauzimu: Achinyamata ena amachoka pakhomo pa makolo awo n’cholinga chofuna kupewa kuchita zinthu zauzimu ngati mmene makolo awo amachitira. Ena amakhala ndi cholinga choti azikapitiriza kuphunzira Baibulo paokha komanso kuchita zinthu zina zauzimu koma kenako amayamba makhalidwe oipa. Kodi inuyo mungatani kuti ‘chikhulupiriro chanu chisasweke ngati ngalawa’? *​—1 Timoteyo 1:19.

Yehova Mulungu amafuna kuti aliyense azichita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira. (Aroma 12:1, 2) Khalani ndi chizolowezi chochita zinthu zauzimu komanso kuphunzira Baibulo ndipo muziyesetsa kuchita zimenezi nthawi zonse. Lembani pakalendala zinthu zauzimu zimene muyenera kuchita ndipo onani ngati mungakwanitse kutsatira zimene mwalembazo kwa mwezi umodzi popanda makolo anu kukukumbutsani.

Funso lachitatu komanso lomaliza limene muyenera kuliganizira ndi lakuti . . .

Kodi Ndikufuna Kudzachita Chiyani pa Moyo Wanga?

Kodi mukufuna kuchoka pakhomo pa makolo anu kuti muthawe mavuto? Kapena kuti makolo anu asamangokuuzani zochita? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mukungothawa mavuto koma simukuganizira za tsogolo lanu. Kuchita zimenezi n’chimodzimodzi kuyendetsa njinga n’kumangoyang’ana kumbuyo. Munthu wochita zimenezi akhoza kuchita ngozi chifukwa sakuona zimene zili kutsogolo kwake. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati mukufuna kuchoka pakhomo pa makolo anu muziganizira kwambiri zolinga zimene mukufuna kuchita pa moyo wanu.

Achinyamata ena a Mboni za Yehova amasamukira kudera lina kapena kudziko lina n’cholinga choti azikalalikira. Ena amasamuka kuti akathandize nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu kapena azikagwira ntchito ku maofesi a Mboni za Yehova. Koma ena amachoka pakhomo pa makolo awo n’kukhala kaye okha kwa kanthawi asanakwatire. *

Ndiye kaya inuyo mukufuna kusamuka pa zifukwa ziti, mukufunika kuiganizira nkhani imeneyi mofatsa. Baibulo limanena kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Muzimvera malangizo a makolo anu. (Miyambo 23:22) Muziipempherera nkhani imeneyi ndipo mukamasankha zochita muziganizira mfundo za m’Baibulo zimene takambirana m’mutu uno.

Choncho funso lofunika kuliganizira n’lakuti, kodi ndikhoza kukwanitsa kukhala pandekha? Ngati mungayankhe kuti inde ndiye kuti ndinu wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 23 Kuti mudziwe zambiri werengani Mutu 19 m’Buku Lachiwiri.

^ ndime 27 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 34 ndi 35 m’Buku Lachiwiri.

^ ndime 32 Anthu a zikhalidwe zina amaona kuti ndi bwino kuti mwana makamaka mtsikana azikhalabe ndi makolo ake mpaka atakwatiwa. Baibulo silinena chilichonse pa nkhani imeneyi.

LEMBA

“Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake.”​—Mateyu 19:5.

MFUNDO YOTHANDIZA

Kwa miyezi ingapo perekani kwa makolo anu ndalama zomwe amawononga pogulira chakudya chanu, kulipira lendi ndi zinthu zina. Ngati simukufuna kapena ngati simungakwanitse kuchita zimenezi, ndiye kuti simunakonzeke kukakhala panokha.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Cholinga chanu chochokera pakhomo chingapangitse kuti muzikakhala osangalala kumene mukupitako kapena ayi.

ZOTI NDICHITE

Cholinga changa ndikadzayamba kukhala pandekha ndi ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi: ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Ngakhale kuti mumakhala mopanikizika pakhomo pa makolo anu, n’chifukwa chiyani ndi bwino kukhalabe pakhomopo kwa kanthawi?

● Pamene mudakali pakhomo pa makolo anu, kodi mungatani kuti muthandize banja lanu komanso kuti mukonzekere kukakhala panokha?

[Mawu Otsindika patsamba 52]

“Mwachibadwa munthu aliyense amafuna kuchita zinthu zina payekha. Koma ngati munthu akuchoka pakhomo pa makolo ake pongofuna kuthawa malamulo amene ali pakhomopo ndiye kuti sanakonzeke kukakhala payekha.”​—Anatero Aron

[Chithunzi patsamba 50, 51]

Kuchoka pakhomo pa makolo anu kuli ngati kupita kuchipululu nokhanokha. Musananyamuke muyenera kuphunzira zinthu zomwe zingakuthandizeni kukhala panokha