Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakopeke Ndi Zochita za Anzanga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakopeke Ndi Zochita za Anzanga?

Mutu 9

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakopeke Ndi Zochita za Anzanga?

Karen wangofika kumene kuphwando ndipo akuona anyamata awiri akubwera ndi zimajumbo zikuluzikulu ziwiri. Iye wadziwiratu zimene zili m’majumbomo chifukwa nthawi inayake anamva anyamatawo akukambirana kuti kuphwandoko kukakhala mowa wochita kusamba.

Kenako Karen akumva mnzake, dzina lake Jessica, akumufunsa kuti: “Kodi iwe wangoti ndwii pamenepo bwanji?” Pamene Karen akutembenuka akuona kuti mnzakeyo wanyamula mabotolo awiri a mowa ongotsegula kumene. Jessica akum’patsa Karen botolo limodzilo n’kumuuza kuti: “Eko imwa, kumanjoyako nthawi zina. Si zoti ‘Ine sindimwa.’”

Karen akufuna kukana koma akuona kuti n’zovuta. Jessica ndi mnzake komanso sakufuna kuti azimuona ngati samanjoyako nthawi zina. Komanso Karen amaona kuti Jessica ndi munthu wabwino. Ngati iyeyo akumwa ndiye kuti kumwa kulibe vuto lililonse. Karen akuganiza kuti: ‘Kumwa mowa kuli ndi vuto ngati? Ngati kuti ndikumwa mankhwala osokoneza bongo kapena ndikuchita uhule?’

MUNTHU ukakhala wamng’ono umayesedwa ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe zikhoza kukukopa ndipo nthawi zambiri ngati ndiwe mnyamata umayesedwa ndi atsikana pomwe atsikana amayesedwa ndi anyamata. Mnyamata wina wazaka 17, dzina lake Ramon, ananena kuti: “Atsikana akusukulu kwathu ndi okakamira kwambiri. Amakonda kukugwiragwira pongofuna kukuyesa ndipo ngati sungawaletse akhoza kukugwira posakhala bwino. Samakusiya ngakhale uwaletse.” Nayenso mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Deanna, amakumananso ndi vuto lomweli. Iye ananena kuti: “Mnyamata wina anabwera n’kundikolekera m’khosi. Ndinam’menya pamkono ndi mphamvu n’kumuuza kuti: ‘Tandisiye iwe, bwanji kodi?’”

N’kutheka kuti nanunso mumayesedwa ndi anzanu ndipo zimaoneka ngati kuyesedwako sikudzatha. Nthawi zina anthu amapitirizabe kukuyesa ngakhale utayesetsa kusonyeza kuti sukufuna kuchita zomwe akufunazo. Kodi inuyo mumayesedwa kawirikawiri? Kodi inuyo mumakopeka ndi zinthu zili m’munsizi?

□ Kusuta fodya

□ Kuonera zolaula

□ Kumwa mowa

□ Kufuna kugonana ndi munthu wina

□ Kumwa mankhwala ozunguza bongo

□ Zina ․․․․․

Ngati mwaika chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi kena kalikonse pamwambapa musaganize kuti n’zosatheka kukhala Mkhristu. Mukhoza kuphunzira kusatengeka ndi zochita za ena. Chimene chingakuthandizeni kuchita zimenezi ndi kuzindikira zimene zimachititsa kuti muzikopeka ndi zochita za ena. Tiyeni tione zinthu zitatu.

1. Ndife ochimwa. Munthu aliyense wochimwa amafuna kuchita zinthu zoipa. Ngakhale mtumwi Paulo, yemwe anali Mkhristu wolimba, anavomereza mfundo imeneyi ponena kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” (Aroma 7:21) Choncho, ngakhale munthu amene amayesetsa kuchita zinthu zabwino nthawi zina amalimbana ndi “chilakolako cha thupi,” komanso “chilakolako cha maso.” (1 Yohane 2:16) Koma ngozi imakhalapo ngati munthu akungoganizira zinthu zoipazo chifukwa Baibulo limati: “Chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.”​—Yakobo 1:15.

2. Anzanu komanso zinthu zina. Munthu ukhoza kukopeka kuchita zinthu zoipa kwina kulikonse. Mtsikana wina, dzina lake Trudy, ananena kuti: “Anthu amangokhalira kukamba nkhani zogonana, kaya ndi kusukulu ndiponso kuntchito. Ndipo akamazionetsa pa TV komanso m’mafilimu amazionetsa ngati ndi zinthu zosangalatsa kwambiri. Moti nthawi zambiri saonetsa mavuto amene munthu angakumane nawo.” Zimene zinachitikira Trudy zinamuthandiza kuzindikira kuti zochita za anthu ena komanso zimene timaonera, zikhoza kutikopa n’kuchita zoipa. Iye ananena kuti: “Ndili ndi zaka 16 ndinayamba chibwenzi ndi mnyamata wina ndipo ndinkaona kuti timakondana kwambiri. Mayi anga anandilangiza kuti ngati sindithetsa chibwenzicho nditenga mimba. Ndinadabwa kwambiri ndi zimene ananenazi. Koma patangotha miyezi iwiri, ndinapezeka kuti ndilidi ndi mimba.”

3. “Zilakolako zaunyamata.” (2 Timoteyo 2:22) Zilakolako zaunyamata zingaphatikizepo chilichonse chomwe achinyamata amafuna monga kufuna kuti azikondedwa ndi anthu ena komanso kuti anthu ena aziwaona kuti ndi munthu wamkulu. Sikulakwa kufuna zinthu zimenezi koma ngati munthu sangasamale zikhoza kuchititsa kuti akopeke mosavuta. Mwachitsanzo, ngati mukufunitsitsa kuti anthu ena azikuonani kuti ndinu munthu wamkulu mukhoza kuyamba kunyalanyaza malangizo a makolo anu. Ndi zimene zinachitikira Steve ali ndi zaka 17. Iye ananena kuti: “Ndinasiya kutsatira malangizo a makolo anga ndipo ndinayamba kuchita zinthu zimene ankandiletsa. Ndinachita zonsezi nditangobatizidwa kumene.”

Mmene Mungapewere Kuchita Zoipa

Zinthu zitatu zimene tazitchula pamwambazi zimachititsa kuti anthu ambiri azikopeka kuchita zoipa. Komabe, n’zotheka kupewa kuchita zinthu zoipa. Kodi mungazipewe bwanji?

● Choyamba, zindikirani chinthu chimene chimakukopani kwambiri. (Mwina mwasankha kale pamwambapa.)

● Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakopeka kwambiri ndikakhala ndili kuti?’ Ikani chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi kamene kakusonyeza kumene mumakopeka kwambiri:

□ Kusukulu

□ Ndikakhala ndekha

□ Kuntchito

□ Malo ena ․․․․․

Kudziwa malo amene mungakopeke mosavuta kungakuthandizeninso kupewa kuchita zoipa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene tafotokoza kumayambiriro kwa nkhaniyi. Kodi n’chiyani chikanamuthandiza Karen kudziwa kuti kuphwandoko kukhoza kuchitika zinazake zoipa?

․․․․․

Kodi Karen akanatani kuti asakopeke?

․․․․․

● Popeza mwazindikira zinthu zimene zikhoza kukukopani komanso nthawi imene mungakopeke, tsopano mukhoza kupeza njira yopewera vutolo. Chinthu choyamba chimene mungachite ndi kuganizira zimene mungachite kuti musamakopeke kwambiri kapenanso musamakopeke n’komwe. Lembani m’munsimu zimene mungachite.

․․․․․

(Zitsanzo: Ngati nthawi zambiri anzanu a kusukulu amakukopani kuti musute fodya mukaweruka, mwina mungasinthe njira imene mumadutsa kuti musamakumane nawo. Ngati muli ndi foni ya intaneti ndipo mumalandira zithunzi zolaula, mwina mungaikemo mapulogalamu oti azitsekereza kuti zinthu zimenezo zisamabwere. Komanso mukamafufuza zinthu pa intaneti muzilemba zinthu zomwe mukufunazo momveka bwino.)

N’zoona kuti simungapeweretu zinthu zonse zoipa. Mwina mukhoza kukumana ndi zinthu zokopa kwambiri pa nthawi imene simukuyembekezera. Kodi mungatani kuti musadzakopeke?

Konzekerani

Pamene Yesu ‘ankayesedwa ndi Satana’ anamuyankha mwamphamvu nthawi yomweyo. (Maliko 1:13) Anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kale zimene ankayenera kuchita pa nkhaniyo komanso chifukwa chakuti anali atatsimikiza kale mumtima mwake kuti azimvera Atate wake nthawi zonse. (Yohane 8:28, 29) Yesu ananena kuchokera pansi pa mtima kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.”​—Yohane 6:38.

Patsamba lotsatirali, lembani zifukwa ziwiri zokuchititsani kupewa chinthu chomwe chimakukopani nthawi zambiri. Lembaninso zinthu ziwiri zimene zingakuthandizeni kuti muzipewa chimene chimakukopanicho.

Zifukwa:

1 ․․․․․

2 ․․․․․

Zimene zingakuthandizeni:

1 ․․․․․

2 ․․․․․

Muzikumbukira kuti nthawi iliyonse imene mwalolera kuchita zinthu zoipa, mumakhala kapolo wa mtima wanu. (Tito 3:3) Si bwino kulola kuti mtima wanu uzikulamulirani. Inuyo ndi amene muyenera kulamulira mtima wanuwo. (Akolose 3:5) Ndipo muziipempherera nkhani imeneyi.​—Mateyu 6:13. *

WERENGANI ZAMBIRI PA NKHANIYI M’MUTU 15 M’BUKU LACHIWIRI

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mukumalephera kuchita zinthu mwachangu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukhale ndi mphamvu komanso thanzi labwino

[Mawu a M’munsi]

LEMBA

“Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”​—1 Akorinto 10:13.

MFUNDO YOTHANDIZA

Onani bokosi limene lili patsamba 132 ndi 133, lomwe lili ndi mutu wakuti “Mmene mungakonzekerere” m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Bokosili lingakuthandizeni kudziwa komanso kukonzekereratu zimene munganene ngati munthu wina atakunyengererani kuti muchite zoipa.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Mulungu ananeneratu kuti Yesu adzakhala wokhulupirika, koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu analengedwa ngati loboti yomwe imangochita zinthu osaganiza. Yesu anali ndi ufulu wosankha zoyenera kuchita moti anakhala munthu wokhulupirika chifukwa choti anachita kusankha yekha osati chifukwa chakuti anam’panga kuti adzakhale wokhulupirika. N’chifukwa chake ankachita kupemphera akamayesedwa.​—Aheberi 5:7.

ZOTI NDICHITE

Ndizichita zotsatirazi kuti ndizilimba mtima kupewa kuchita zinthu zoipa: ․․․․․

Malo, anthu komanso zochitika zimene ndiyenera kuzipewa: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi zolengedwa zopanda uchimo zikhoza kukopedwa kuti zichite zinthu zoipa?​—Genesis 6:1-3; Yohane 8:44.

● Kodi anthu ena amakhudzidwa bwanji ngati simunakopeke kuti muchite zoipa?​—Miyambo 27:11; 1 Timoteyo 4:12.

[Mawu Otsindika patsamba 68]

“Chimene chimandithandiza kwambiri ndi kudziwa kuti Mulungu, yemwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonsechi, ndi wokonzeka kundithandiza ndipo ndikhoza kumupempha nthawi iliyonse kuti andithandize.”​—Anatero Christopher

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 67]

Ganizirani Izi

Nthawi zonse muvi wa kampasi umaloza kumpoto. Koma ngati kampasiyo itayandikana ndi maginito, muviwo sumalozanso kumpoto. M’malomwake umaloza mbali imene kuli maginitowo.

Chikumbumtima chanu chili ngati kampasi. Ngati munachiphunzitsa bwino chimakuthandizani kusankha zinthu mwanzeru. Koma kucheza ndi anthu oipa, n’kwamphamvu ngati maginito chifukwa kungakusokonezeni maganizo n’kuyamba kuchita zinthu zolakwika. Choncho, ndi bwino kuti muzipewa kukhala malo olakwika komanso kucheza ndi anthu omwe angakuchititseni kuti musamasankhe zinthu mwanzeru.—Miyambo 13:20.

[Chithunzi patsamba 69]

Mukalolera kuchita zinthu zoipa mumakhala kapolo wa mtima wanu