Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kusamalira Thanzi Langa?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kusamalira Thanzi Langa?

Mutu 10

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kusamalira Thanzi Langa?

Ikani chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi komwe kali ndi cholinga chomwe mukufuna kukwaniritsa.

□ Ndichepetse nkhawa

□ Ndisamakwiye msanga

□ Ndisamadzikayikire

□ Ndizichita zinthu mochangamuka

□ Ndizikhala ndi mphamvu

□ Ndikhale ndi khungu looneka bwino

□ Nditsitse weti

PALI zinthu zina zimene simungasankhe pa moyo wanu. Mwachitsanzo, simungasankhe makolo, abale anu kapena malo amene mukukhala. Koma pa nkhani yokhudza thanzi lanu mukhoza kusankha zochita. Ngakhale kuti zinthu zina mumachita kutengera kwa makolo anu, koma thanzi lanu limayendera zimene mumachita komanso zimene simumachita. *

Anthu ena anganene kuti, ‘Ndidakali mwana, ndiye palibe chifukwa chodandaulira za thanzi langa.’ Ngati mumaganiza choncho, onaninso zimene zili patsamba 71 zija. Kodi inuyo mwasankha zolinga ziti? Dziwani kuti mukakhala ndi thanzi labwino mukhoza kukwaniritsa cholinga chilichonse chomwe chili pamenepo.

N’kutheka kuti mungakhale ndi maganizo amene mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Amber, anali nawo. Iye anati: “Sindingakwanitse kumangodya zakudya zopanda mafuta ambiri kapena zopanda shuga.” Ngati nanunso mukuganiza choncho musadandaule. Kukhala ndi thanzi labwino sikutanthauza kuti musiyiretu kudya maswiti komanso kuti muyambe kuthamanga wefuwefu mtunda wautali. Mungangofunika kusintha zinthu zina pa moyo wanu kuti muyambe kuoneka bwino, muzikhala ndi mphamvu komanso muzichita zinthu mwachangu. Tiyeni tione zimene achinyamata ena achita kuti akhale ndi thanzi labwino.

Muzidya Zakudya Zoyenera Kuti Muzioneka Bwino

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizichita zinthu mosapitirira malire. Lemba la Miyambo 23:20, limati: “Usakhale . . . pakati pa anthu odya nyama mosusuka.” Komatu nthawi zina kutsatira malangizo amenewa kumakhala kovuta.

“Ndimakhala ndi njala nthawi zonse ngati mmenenso zimakhalira ndi achinyamata ambiri. Makolo anga amandinena kuti ndikamadya zimangokhala ngati chakudyacho ndikuponyera m’dzenje lomwe silidzaza.”​—Anatero Andrew, wazaka 15.

“Ngakhale kuti ndimadziwa kuti zakudya zina zingandiyambitsire mavuto, sindingasiye kudya chifukwa mavutowo sanayambe kuonekera panopa.”​—Anatero Danielle, wazaka 19.

Kodi mumaona kuti mufunika kudziletsa pa nkhani ya zakudya? Onani zimene zinathandiza achinyamata ena kukwanitsa kuchita zimenezi.

Muzidziwa kuti mwakhuta. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Julia, ananena kuti: “Kale ndinkadya kwambiri ndipo ndinkangopewa zakudya zokhazo zomwe ndikudziwa kuti zimanenepetsa, koma masiku ano ndimasiya kudya ndikaona kuti ndakhuta.”

Muzipewa zakudya zosapatsa thanzi. Mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Peter, ananena kuti: “Nditasiya zakumwa zoziziritsa kukhosi ndinatsitsa weti yanga ndi makilogalama 5 m’mwezi umodzi wokha.”

Musamadye kwambiri. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Erin, ananena kuti: “Ndimayesetsa kuti ndisatengenso zakudya kachiwiri.”

Zomwe Zingakuthandizeni: Muzionetsetsa kuti mwadya chakudya cham’mawa, chamasana ndi chamadzulo. Mukadumpha chakudya china mumakhala ndi njala kwambiri, zomwe zingapangitse kuti mudye kwambiri.

Muzichita Masewera Olimbitsa Thupi Kuti Muzimva Bwino

Baibulo limati: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Komabe achinyamata ambiri samafuna kuchita masewera olimbitsa thupi.

“Ndili kusekondale, ana ambiri ankalephera kuchita masewera olimbitsa thupi. Komatu phunziro limeneli linali lophweka kwambiri. Panali pampunga penipeni.”​—Anatero Richard, wazaka 21.

“Ena amaganiza kuti, ‘N’kudzivutitsiranji kumakathamanga panja dzuwa lili phwee m’malo momakapanga masewera ngati omwewo pakompyuta.’”​—Anatero Ruth, wazaka 22.

Kodi mumagwa ulesi mukangomva za kupanga masewero olimbitsa thupi? Ngati ndi choncho, onani zinthu zitatu zimene mungapeze ngati mumachita masewera olimbitsa thupi.

Choyamba. Thupi lanu limakhala lamphamvu. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Rachel, ananena kuti: “Bambo anga ankakonda kundiuza kuti, ‘Ngati ulibe nthawi yochita masewera olimbitsa thupi, ndiye ukonzekere kupeza nthawi yodwala.’”

Chachiwiri. Maganizo anu amakhala m’malo. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Emily, ananena kuti: “Kuthamanga kumandithandiza kwambiri ndikakhala kuti ndikuganiza zinthu zambirimbiri. Ndimakhala ndi mphamvu komanso maganizo anga amakhala m’malo.”

Chachitatu. Mumakhala wosangalala. Mtsikana wina wazaka 22, dzina lake Ruth, ananena kuti: “Ndimakonda kukaona malo, n’chifukwa chake ndimakonda kukwera mapiri, kusambira ndiponso kupalasa njinga.”

Zomwe Zingakuthandizeni: Muziyesetsa kuchita masewera olimbitsa thupi omwe mumawakonda kwambiri kwa mphindi 20 zokha, katatu pa mlungu.

Mukamagona Mokwanira Mumachita Zinthu Mwamphamvu

Baibulo limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Ngati simugona mokwanira simukhala ndi mphamvu zokwanira zochitira zinthu.

“Ndikapanda kugona mokwanira ndimalephera kuganiza komanso kuchita zinthu bwinobwino.”​—Anatero Rachel, wazaka 19.

“Ngati sindinagone mokwanira, ikamafika 2 koloko masana ndimakhala nditatopa kwambiri moti ndimatha kugona ndikucheza.”​—Anatero Kristine, wazaka 19.

Kodi simugona mokwanira? Taonani zimene achinyamata anzanu amachita kuti azigona mokwanira.

Musamagone mochedwa. Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Catherine, ananena kuti: “Ndimayesetsa kuti ndizigona nthawi yabwino.”

Musamacheze mpaka usiku kwambiri. Mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Richard, ananena kuti: “Nthawi zina anzanga amandiimbira foni kapena kunditumizira mameseji usiku kwambiri. Koma panopa ndapeza njira yosiyira kucheza nawo usikuwo kuti ndizigona.”

Musamasinthesinthe. Mtsikana wina wazaka 20, dzina lake Jennifer, ananena kuti: “Panopa ndinakonza nthawi yogonera komanso kudzuka imene nthawi zonse ndimaitsatira.”

Zomwe Zingakuthandizeni: Muziyesetsa kugona maola osachepera 8 tsiku lililonse.

Ngati mutatsatira njira zosavuta zimenezi mukhoza kukhala ndi thanzi labwino kwambiri. Muzikumbukira kuti kukhala ndi thanzi labwino kungakuthandizeni kuti muzioneka bwino, muzikhala wosangalala komanso kuti muzigwira bwino ntchito. Zinthu zina pa moyo wanu simungathe kuzisintha koma thanzi lanu mukhoza kulisintha. Erin, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Ndi udindo wanu kusamalira thanzi lanu.”

M’MUTU WOTSATIRA

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite ngati simugwirizana ndi makolo anu pa nkhani ya zovala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 N’zoona kuti anthu ambiri amadwala matenda osiyanasiyana komanso ena ndi olumala ndipo palibe chimene angachite kuti athetse vuto lawolo. Mutu uno wakonzedwa n’cholinga chothandiza anthu oterewa kuti akhale ndi thanzi labwinoko malinga ndi zimene angathe.

LEMBA

“Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”​—1 Timoteyo 4:8.

MFUNDO YOTHANDIZA

Pezani munthu woti muzipanga naye masewera olimbitsa thupi. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzilimbikira chifukwa simungafune kukhumudwitsa mnzanuyo.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kuchita masewera olimbitsa thupi kumathandiza kuti ubongo wanu utulutse timadzi tinatake. Timadziti timathandiza kuchepetsa ululu komanso timathandiza kuti muzikhala wosangalala.

ZOTI NDICHITE

Cholinga chomwe ndili nacho pa nkhani ya zakudya n’chakuti ․․․․․

Cholinga chomwe ndili nacho pa nkhani ya masewera olimbitsa thupi n’chakuti ․․․․․

Mwezi ukubwerawu ndiziyesetsa kuti ndizigona maola pafupifupi tsiku lililonse. ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kusamalira thanzi lanu kungakuthandizeni bwanji kuti musamadzikayikire?

● Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuposa kusamalira thanzi lanu?​—1 Timoteyo 4:8.

[Mawu Otsindika patsamba 74]

“Ndimasangalala ndikamachita masewera olimbitsa thupi komanso ndikaona kuti thupi langa layamba kusintha chifukwa cha masewerawo.”​—Anatero Emily

[Bokosi patsamba 73]

“Ndinasintha Zinthu pa Moyo Wanga”

“Ndili mwana ndinali chiduntu ndipo zimenezi sizinkandisangalatsa. Ndinkayesetsa kupewa zakudya zina kuti ndiphwe koma sindinkachedwa kunenepanso. Ndiyeno ndili ndi zaka 15, ndinatsimikiza zoti ndisinthe zinthu zina pa moyo wanga. Ndinkafuna kupeza njira yabwino yochepetsera thupi komanso yoti ndikhoza kuitsatira kwa moyo wanga wonse. Ndinagula buku lomwe linkafotokoza za zakudya komanso masewera olimbitsa thupi oyenera ndipo ndinayamba kutsatira zimene bukulo linkanena. Ndinatsimikiza kuti sindidzasiya kutsatira mfundozo ngakhale chinachake chitandigwetsa ulesi. Patangopita chaka chimodzi ndinatsitsa weti ndi makilogalamu oposa 25. Ndipo kuyambira pamenepo sindinanenepenso. Poyamba ndinkaona ngati sindingakwanitse koma chimene chinandithandiza kwambiri n’chakuti ndinasintha zinthu pa moyo wanga.”​—Anatero Catherine, wazaka 18.

[Chithunzi patsamba 74]

Thanzi lanu lili ngati galimoto. Ngati simukuisamalira bwino imawonongeka