Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere?

Mutu 12

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere?

Inde Ayi

Kodi mukadziyang’ana pagalasi □ □

mumasangalala ndi mmene mukuonekera?

Kodi mumaona kuti muli ndi luso □ □

linalake limene anzanu amasirira?

Kodi anzanu atakunyengererani kuti □ □

muchite zinthu zoipa zimene iwowo

akufuna, mukhoza kukana?

Kodi mumavomereza mfundo zomveka □ □

zimene munthu wina wanena

zotsutsana ndi mfundo zanu?

Kodi mumatani anthu ena □ □

akamanena zinthu zoipa za inuyo?

Kodi mumaona kuti anthu □ □

amakukondani?

Kodi mumayesetsa kuti mukhale ndi □ □

thanzi labwino?

Kodi mumasangalala anthu ena □ □

zikamawayendera bwino?

Kodi mumaona kuti nthawi □ □

zambiri mukachita zinthu,

zimakuyenderani bwino?

Ngati mwayankha kuti ayi pa mafunso ambiri m’mwambamu, mwina muli ndi vuto lodziderera moti simuona zimene mumachita bwino. Mutu uno wakonzedwa n’cholinga chokuthandizani kuti muone zimene mumachita bwino.

ACHINYAMATA ambiri amavutika chifukwa cha mmene amaonekera, luso limene ali nalo ndiponso mmene anzawo amawaonera. Kodi inunso mumamva choncho nthawi zina? Dziwani kuti siinu nokha amene mumamva choncho.

“Nthawi zambiri zimene ndimalakwitsa zimandichititsa kukhala wokhumudwa ndipo ndimakhalira kudziimba mlandu.”​—Anatero Leticia.

“Ngakhale utakhala wokongola bwanji, nthawi zonse umakumanabe ndi anthu ena okongola kwambiri kuposa iweyo.”​—Anatero Haley.

“Ndimada nkhawa kwambiri ndikakhala ndi anthu ena chifukwa ndimangoganiza kuti aliyense azindiona ngati ndine munthu wachabechabe.”​—Anatero Rachel.

Ngati mukugwirizana ndi mfundo zili pamwambazi, musadandaule chifukwa thandizo lilipo. Tiyeni tikambirane mfundo zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti musamadziderere komanso kuti muzitha kuona zabwino zimene mumachita.

Muzichitira Anthu Ena Zinthu Zabwino

Lemba lothandiza. “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Tanthauzo lake. Mukamachitira anthu ena zinthu zabwino ndiye kuti mukudzichitiranso zinthu zabwino. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Baibulo limati: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto, ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.” (Miyambo 11:25) Palibe amene angatsutse kuti munthu ukachitira anthu ena zinthu zabwino umakhala wosangalala. *

“Nthawi zambiri ndimaganizira zimene ndingachite kuti ndithandize munthu wina mu mpingo mwathu ndipo ndimayesetsa kuchita zimene ndaganizazo. Ndimasangalala kwambiri ndikamachita zinthu zosonyeza kuti ndimakonda anthu ena.”​—Anatero Breanna.

“Ntchito yolalikira ndi yothandiza kwambiri chifukwa imakuchititsa kuti usamangoganizira za iwe wekha koma uziganiziranso anthu ena.”​—Anatero Javon.

Chenjezo: Musamathandize anthu ena n’cholinga choti mupezepo kenakake. (Mateyu 6:2-4) Kuthandiza anthu ndi zolinga zolakwika n’kopanda phindu chifukwa nthawi zambiri anthu amatulukira kuti muli ndi zolinga zolakwika.​—1 Atesalonika 2:5, 6.

Chitani izi. Ganizirani munthu amene munamuthandizapo. Kodi dzina lake ndani ndipo munamuthandiza bwanji?

․․․․․

Kodi mutamuthandiza munamva bwanji?

․․․․․

Ganizirani munthu winanso amene mungamuthandize ndipo lembani mmene mungamuthandizire.

․․․․․

Yesetsani Kupeza Anzanu Abwino

Lemba lothandiza. “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.

Tanthauzo lake. Mnzako weniweni amakuthandiza pakagwa mavuto. (1 Samueli 18:1; 19:2) Ndipotu kungodziwa kuti winawake amakuganizira n’zolimbikitsa kwambiri. (1 Akorinto 16:17, 18) Choncho, yesetsani kupeza anzanu omwe angakuthandizeni.

“Mnzako weniweni amakulimbikitsa.”​—Anatero Donnell.

“Nthawi zina umasangalala kungodziwa kuti winawake amakuganizira. Zimakupangitsa kuona kuti ndiwe wofunika.”​—Anatero Heather.

Chenjezo: Musamachite zinthu n’cholinga chongofuna kuti mufanane ndi gulu linalake la anthu kuti akhale anzanu. (Miyambo 13:20; 18:24; 1 Akorinto 15:33) Kuyamba khalidwe loipa n’cholinga choti anzanu azikugomerani n’kosathandiza ndipo kungakuchotsereni ulemu wanu komanso mungamadzione kuti ndinu wachabechabe.​—Aroma 6:21.

Chitani izi. Lembani dzina la mnzanu amene angakulimbikitseni pa zinthu zabwino.

․․․․․

Mungachite bwino kupeza nthawi yocheza ndi munthu amene mwatchulayu.​—Dziwani izi: Munthu ameneyu akhoza kukhala wamkulu kapena wamng’ono kwa inuyo.

Musataye Mtima

Lemba lothandiza. “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.”​—Aroma 3:23.

Tanthauzo lake. Tonse tinabadwa ochimwa. Izi zikusonyeza kuti nthawi zina tikhoza kulankhula kapena kuchita zinthu zolakwika. (Aroma 7:21-23; Yakobo 3:2) N’zoona kuti simungapeweretu kulakwitsa zinthu zina, koma mukhoza kuyesetsa kuti musamakhumudwe kwambiri mukalakwitsa zinthu. Baibulo limati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.”​—Miyambo 24:16.

“Nthawi zina timayamba kudziderera chifukwa choti tikalakwitsa zinthu timadziyerekezera ndi munthu yemwe amachita bwino zinthuzo.”​—Anatero Kevin.

“Aliyense amakhala ndi makhalidwe abwino komanso ena oipa. Tiyenera kusangalala kuti tili ndi makhalidwe abwino komanso kuyesetsa kusintha makhalidwe oipawo.”​—Anatero Lauren.

Chenjezo: Musamachite zinthu zoipa mwadala chifukwa chakuti ndinu wochimwa. (Agalatiya 5:13) Kuchita dala zinthu zoipa kungachititse kuti musokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova Mulungu, womwe ndi wofunika kwambiri.​—Aheberi 10:26, 27.

Chitani izi. Lembani khalidwe loipa limene mukufuna kuti mulisiye.

․․․․․

Lembani deti lalero pambali pa khalidweli. Fufuzani mfundo zimene zingakuthandizeni kusintha khalidweli ndiyeno pambuyo pa mwezi umodzi muone ngati mwasintha.

Ndinu Munthu Wofunika

Baibulo limanena kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (1 Yohane 3:20) Izi zikutanthauza kuti Mulungu amaona kuti ndinu wofunika ngakhale mutakhala kuti eniakenu simudziona choncho. Koma kodi tikachimwa Mulungu amasintha mmene amationera? Tiyerekeze kuti muli ndi ndalama ya pepala ndiye yang’ambika pang’ono. Kodi zimenezi zingachititse kuti muitaye kapena kuyamba kuiona kuti ndi yosafunika? Ayi. Ndalama sisintha mphamvu chifukwa choti ndi yong’ambika.

Ndi mmenenso Mulungu amakuonerani. Iye amakuonanibe kuti ndinu ofunika ngakhale kuti nthawi zina mumalakwitsa zinthu zina. Amaona komanso saiwala zimene mumayesetsa kuchita kuti mumusangalatse ngakhale zitakhala zochepa bwanji. N’chifukwa chake Baibulo limakutsimikizirani kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”​—Aheberi 6:10.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi nthawi zina mumangokhala wokhumudwa? Kodi mungatani ngati zimenezi zimakuchitikirani?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, mungasangalale kwambiri chifukwa chouzako ena uthenga wabwino wa Ufumu.​—Yesaya 52:7.

LEMBA

“Koma aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”​—Agalatiya 6:4.

MFUNDO YOTHANDIZA

Musamakonde kunena kuti ‘Nthawi zonse ndimalephera’ kapena kuti ‘Palibe chimene ndimachita bwino.’ Maganizo amenewa si abwino chifukwa akhoza kukufooketsani ndipo ndi okokomeza. M’malomwake dziwani zimene mumalephera komanso zimene mumachita bwino.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Mmene anthu ena amakuonerani komanso mmene amachitira nanu zinthu zimadalira mmene inuyo mumadzionera.

ZOTI NDICHITE

Anzanga akadzandikhumudwitsa ndidzachita zotsatirazi: ․․․․․

Ndikazindikira kuti ndikungoganizira zomwe ndimalephera, ndidzachita zotsatirazi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi: ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chiyani chimapangitsa achinyamata ambiri kuti azidziderera?

● N’chifukwa chiyani ndi bwino kumachita zinthu modzidalira?

[Mawu Otsindika patsamba 88]

“Munthu wina akhoza kukhala wooneka bwino koma n’kumadziona ngati wosakongola. Komanso pakhoza kukhala munthu wina yemwe si wokongola kwenikweni koma iyeyo n’kumadziona ngati ndi wokongola kwambiri. Nkhani yagona pa mmene munthuyo amadzionera.”​—Anatero Alyssa

[Chithunzi patsamba 90]

Ndalama sisintha mphamvu chifukwa choti ndi yong’ambika. Mulungu amationabe kuti ndife ofunika ngakhale kuti nthawi zina timalakwitsa zinthu zina