Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

Mutu 13

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?

“Nthawi zonse anzanga akakhala ndi mavuto ndimawathandiza. Koma ineyo ndikakumana ndi mavuto omwewo ndimangodzitsekera m’nyumba n’kumangolira ndipo anthu ambiri sadziwa zimenezi.”​—Anatero Kellie.

“Ndikakhumudwa ndimakonda kukhala ndekha. Ndikaitanidwa kuti ndipite kwinakwake ndimapeza chifukwa chokanira. Ndimayesetsa kuti ngakhale abale anga asadziwe kuti ndakhumudwa. Amangoganiza kuti ndili bwinobwino.”​—Anatero Rick.

KODI inunso mumachita zimene Kellie ndi Rick amachita? Ngati mwayankha kuti inde, musafulumire kuganiza kuti muli ndi vuto. Tikutero chifukwa aliyense amakhumudwa nthawi zina. Ngakhale anthu okhulupirika amene anatchulidwa m’Baibulo anakhumudwapo.​—1 Samueli 1:6-8; Salimo 35:14.

Nthawi zina mukhoza kudziwa chimene chakuchititsani kuti mukhumudwe koma nthawi zina simungadziwe. Mtsikana wina wazaka  19, dzina lake Anna, ananena kuti: “Nthawi zina munthu umangokhumudwa ngakhale kuti palibe chimene chachitika. Sungazimvetse koma zimachitika.”

Kaya pali chimene chachititsa kapena palibe, kodi mungatani kuti musakhale okhumudwa? Yesani kuchita izi:

1. Muzifotokozera munthu wina. Atapanikizika ndi mavuto, Yobu ananena kuti: “Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.”​—Yobu 10:1.

“Ndimamva bwino kwambiri ndikafotokozerako munthu wina mmene ndikumvera. Zimakhala ngati ndagwera m’chidzenje chakuya ndipo munthuyo wadziwa zimenezi moti akhoza kundiponyera chingwe n’kundipulumutsa.​—Anatero Kellie.

Tayesani izi: Lembani dzina la munthu amene mungamufotokozere mmene mukumvera ngati mwakhumudwa.

․․․․․

2. Lembani mmene mukumvera. Mukasokonezeka maganizo chifukwa chokhumudwa, mungachite bwino kulemba mmene mukumvera. Davide, yemwe anauziridwa kulemba masalimo, analembanso mawu osonyeza kuti nthawi ina anakhala wokhumudwa kwambiri. (Salimo 6:6) Kulemba mmene mukumvera kukhoza kukuthandizani kuti ‘musunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.’​—Miyambo 3:21.

“Ndikakhumudwa, ndimasokonezeka maganizo kwambiri. Koma ndikalemba mmene ndikumvera, maganizo anga amakhazikika. Kulemba kumathandizanso kuti udziwe chimene chachititsa kuti ukhumudwe ndipo ukadziwa vutolo limachepa.”​—Anatero Heather.

Tayesani izi: Gwiritsani ntchito tchati chimene chili patsamba 93 kuti mupeze njira zimene zingakuthandizeni mukakumana ndi zinthu zokhumudwitsa. Tchati chimenechi chingakuthandizeni kuti mukakumana ndi zinthu zokhumudwitsa, musamakhumudwe kwambiri.

3. Muzipemphera. Baibulo limanena kuti mukapempherera nkhawa zanu, “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”​—Afilipi 4:6, 7.

“Ndinayesetsa kufufuza kuti ndidziwe chimene chinkandichititsa kukhumudwa koma ndinalephera. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala wosangalala. Ndinatopa ndi kumangokhumudwa popanda chifukwa. Koma kenako ndinasiya kumangokhumudwakhumudwa. Musamakayikire, pemphero limathandiza kwambiri.”​—Anatero Esther.

Tayesani izi: Werengani Salimo 139:23, 24 kenako popemphera kwa Yehova, tsatirani mmene wamasalimoyu anapempherera. Popemphera fotokozani mmene mukumvera mumtima mwanu ndipo pemphani kuti akuthandizeni kudziwa chimene chikukuchititsani kuti muzikhumudwa.

Kuwonjezera pa mfundo zimenezi, muziwerenga Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Kuganizira kwambiri mfundo zolimbikitsa zopezeka m’Baibulo kungakuthandizeni kuti muzikhala osangalala. (Salimo 1:1-3) Mukhoza kupeza mfundo za m’Baibulo zothandiza m’masamba amene ali ndi kamutu kakuti “Chitsanzo Chabwino” m’buku lino komanso Buku Lachiwiri. M’Buku Lachiwiri patsamba 227, mupezapo mfundo zomwe zinathandiza mtumwi Paulo, yemwe nthawi zina ankakhumudwa chifukwa cholakwitsa zinthu zina.

Ngati Mukupitirizabe Kukhala Wokhumudwa

Mnyamata wina, dzina lake Ryan, ananena kuti: “Nthawi zina sindifuna kudzuka pofuna kupewa zinthu zokhumudwitsa.” Ryan amadwala matenda ovutika maganizo ndipo pali anthu enanso omwe ali ndi matenda amenewa. Ochita kafukufuku ena anapeza kuti wachinyamata mmodzi pa achinyamata 4 alionse amadwala matenda ovutika maganizo asanakule.

Kodi mungadziwe bwanji ngati mukudwala matenda ovutika maganizo? Zizindikiro zina za matendawa ndi kukhumudwa pafupipafupi, kufuna kukhala pawekha, kusafuna kuchita chilichonse, kuvutika kudya ndiponso kugona, kudziimba mlandu komanso kudziona kuti ndiwe wosafunika.

N’zoona kuti nthawi zina aliyense akhoza kukhala ndi zina mwa zizindikiro zimenezi. Koma ngati zizindikirozi zitapitirira kwa milungu ingapo, mungachite bwino kufotokozera makolo anu kuti mukaonane ndi adokotala. Adokotala akhoza kudziwa ngati muli ndi matenda ovutika maganizo. *

Ngati mukudwala matenda ovutika maganizo musachite manyazi. Anthu ambiri amene amadwala matendawa akalandira thandizo amayamba kupeza bwino. Kaya mwakhumudwa chifukwa chovutika maganizo kapena ayi, muzikumbukira mawu olimbikitsa opezeka pa Salimo 34:18. Lembali limati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani ngati mumakhumudwa kwambiri moti nthawi zina mumafuna kungodzipha?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 Achinyamata ena akavutika maganizo kwa nthawi yaitali amafuna kungodzipha. Ngati munakhalapo ndi maganizo amenewa, fotokozerani munthu wina wamkulu amene mumam’khulupirira.​—Kuti mudziwe zambiri, onani Mutu 14.

LEMBA

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—Salimo 34:18.

MFUNDO YOTHANDIZA

Lembani mmene mumamvera mukakhumudwa komanso zimene mukuganiza kuti zimachititsa kuti mukhumudwe. Pakapita mwezi umodzi, werenganinso zimene munalembazo. Kodi maganizo anu asintha? Ngati mukuyankha kuti inde, lembani zimene zakuthandizani.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Nthawi zina ndi bwino kulira ngakhale mutakhala munthu wa mwamuna. Pa nthawi ina Mfumu Davide inanena kuti: “Usiku wonse ndimanyowetsa  . . . bedi langa ndi misozi.”​—Salimo 6:6.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndizikhala wosangalala ndizichita zinthu izi: ․․․․․

Kuti ndichepetseko nkhawa ndikakhumudwa, ndizicheza ndi anthu awa: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kulira n’kothandiza?

● Kodi kucheza ndi anthu ena kungakuthandizeni bwanji mukakhumudwa?

[Mawu Otsindika patsamba 96]

“Ndikakhumudwa ndimafuna kukhala pandekha kuti ndiyambirenso kuganiza bwinobwino komanso kuti ndilire. Koma zimenezi zikachitika ndimafunikanso kukhala ndi anthu ena kuti ndisaganizirenso zomwe zinandikhumudwitsazo.”​—Anatero Christine

[Tchati/​Zithunzi patsamba 93]

Zoti Muchite

Kuti Musamakhumudwe Kwambiri Malizitsani kulemba m’munsimu

Zimene zachitika Zosayenera kuchita Zoyenera kuchita

Aphunzitsi Sindizilimbikiranso Chimene chingathandize:

akandichititsa manyazi m’kalasi Werengani Mutu 20

Ngati mnzanga wasiya → Ndiziuza anthu ena nkhani → Chimene chingathandize:

kucheza nanenso zoipa za iyeyu Werengani Mutu 10 m’Buku Lachiwiri

Ngati makolo anga → Ndikwiyira makolo anga → Chimene chingathandize:

akufuna kuthetsa onse kapena kholo limodzi Werengani Mutu 4

banja lawo

․․․․․ ․․․․․ ․․․․․

․․․․․ ․․․․․ ․․․․․

[Chithunzi patsamba 95]

Munthu akakhala wokhumudwa amakhala ngati wagwera m’dzenje. Koma akachita khama ndiponso kuthandizidwa akhoza kutulukamo