Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Bwanji Ndingodzipha?

Bwanji Ndingodzipha?

Mutu 14

Bwanji Ndingodzipha?

“KULI bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.” Kodi mukudziwa amene ananena mawu amenewa? Mwina mungaganize kuti anali munthu amene sankakhulupirira Mulungu kapena amene anali atasiya kukhulupirira Mulungu. Koma amene ananena mawu amenewa ndi munthu amene anali wokhulupirika kwa Mulungu kungoti anali atakhumudwa kwambiri. Dzina lake anali Yona.​—Yona 4:3.

Baibulo silinena kuti Yona ankafuna kudzipha. Koma zimene ananenazi zikusonyeza kuti nthawi zina ngakhale atumiki a Mulungu amavutika mumtima.​—Salimo 34:19.

Achinyamata ena amavutika maganizo ndipo amaona kuti ndibwino kuti angofa. Ena angamve ngati mmene Laura wazaka 16 anamvera. Iye anati: “Ndakhala ndikudwala matenda ovutika maganizo kwa zaka zambiri ndipo nthawi zambiri ndimaganiza zongodzipha.” Kodi mungamuthandize bwanji mnzanu amene ali ndi maganizo amenewa, kapena inuyo mungatani ngati muli ndi maganizo amenewa? Choyamba tiyeni tione zimene zimachititsa munthu kukhala ndi maganizo ofuna kudzipha.

Zimene Zimachititsa Munthu Kukhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha

Pali zifukwa zambiri zimene zimachititsa munthu kuganiza zoti angodzipha. Chifukwa choyamba n’chakuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza,’ yomwe ndi “nthawi yapadera komanso yovuta” ndipo achinyamata ambiri akukumana ndi zinthu zimene zikuwapanikiza pa moyo wawo. (2 Timoteyo 3:1) Chifukwa chinanso n’chakuti, uchimo umachititsa kuti anthu ena azidziona kuti ndi osafunika komanso umachititsa kuti aziganiza zoti anthu ena amawaona ngati osafunika. (Aroma 7:22-24) Nthawi zina zimenezi zimachitika ngati munthu wakumana ndi zinthu zopanda chilungamo. Komanso ena angafune kudzipha chifukwa chakuti akuvutika ndi matenda. Ndipotu m’dziko lina zikuoneka kuti pa anthu 100 alionse amene amadzipha, anthu 90 amadwala matenda enaake amaganizo. *

N’zoona kuti aliyense amakumana ndi mavuto. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa.” (Aroma 8:22) Enanso amene akukumana ndi mavutowa ndi achinyamata. Ndipotu achinyamata amavutika kwambiri maganizo chifukwa cha zinthu monga:

Imfa ya mnzawo, wachibale kapena chiweto

Mavuto a m’banja

Kulephera mayeso

Kutha kwa chibwenzi

Kuchitidwa chipongwe (ngati kumenyedwa kapena kugwiriridwa)

N’zoona kuti wachinyamata aliyense panopa kapena m’tsogolo adzakumanapo ndi ena mwa mavuto amene ali pamwambawa. Koma kodi n’chiyani chimachititsa kuti achinyamata ena azitha kupirira mavutowo kuposa anzawo? Akatswiri ena ananena kuti achinyamata amene amafuna kudzipha amaganiza kuti palibe amene angawathandize ndiponso palibe njira yothetsera mavuto awowo. Amakhala alibe chiyembekezo. Si kuti kwenikweni amafuna kudzipha, koma amangofuna kuthetsa mavutowo.

Kodi Pali Zimene Mungachite?

Kodi mukudziwa munthu wina amene akufuna kudzipha poganiza kuti imeneyi ndi njira yabwino yothetsera mavuto ake? Kodi mungamuthandize bwanji?

Ngati mnzanu wakhala akuvutika maganizo kwambiri moti akuganiza zodzipha mulimbikitseni kuti apeze thandizo. Kaya mnzanuyo akufuna kuti anthu ena adziwe za nkhaniyi kapena ayi, uzani munthu wina wachikulire. Musaganize kuti kuchita zimenezi kusokoneza ubwenzi wanu. Kuuza munthu wachikulire za nkhaniyi kungapulumutse moyo wa mnzanuyo.

Koma bwanji ngati ndi inuyo amene muli ndi maganizo amenewo? Musangosunga nkhaniyi mumtima, koma fotokozerani makolo anu, mnzanu kapena munthu wina aliyense amene amachita zinthu mokuganizirani ndipo akhoza kumvetsa nkhawa zanu. Mukachita zimenezi zinthu zidzakuyenderani bwino. *

N’zoona kuti mavuto anu sangatheretu chifukwa chakuti mwauza munthu wina. Koma zimenezi zingakuthandizeni kuti muyambenso kuona zinthu bwinobwino. Zingakuthandizeninso kuti mupeze njira yothetsera mavutowo.

Zinthu Zimasintha

Mukamakumana ndi vuto linalake muzikumbukira kuti: Ngakhale vutolo likule bwanji, m’kupita kwa nthawi zinthu zimasintha. Pa nthawi ina Davide anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mwasintha kulira kwanga kuti kukhale kuvina.”—Salimo 30:11.

Davide sanayembekezere kuti azingovina mpaka kalekale. Iye ankadziwa kuti mavuto amabwera ndipo amatha. Kodi inunso mukuvomereza mfundo imeneyi? Mavuto ena amaoneka kuti ndi aakulu kwambiri moti mungaganize kuti sangathe. Koma musade nkhawa, m’kupita kwa nthawi zinthu zidzasintha n’kuyamba kuyenda bwino. Nthawi zina mavuto amachepa m’njira imene simumaiganizira n’komwe. Komanso mukhoza kupeza njira yomwe simunaiganizirepo yopiririra vutolo. Pamenepatu mfundo ndi yakuti, kaya mukumane ndi mavuto aakulu bwanji, koma m’kupita kwa nthawi zinthu zidzasintha.—2 Akorinto 4:17.

Pemphero Limathandiza

Mukamakumana ndi mavuto, chinthu chofunika kwambiri ndi kupemphera. Mukhoza kupemphera ngati mmene Davide anapempherera kuti: “Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere, ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa, ndipo munditsogolere m’njira yamuyaya.”​—Salimo 139:23, 24.

Pemphero silimangotithandiza kupirira mavuto amene tikukumana nawo, koma ndi njira imene timalankhulira ndi Atate wathu wakumwamba. Iye amafuna kuti ‘tizimukhuthulira za mumtima mwathu.’ (Salimo 62:8) Taonani zifukwa zina zimene zingatichititse kuti tizikhuthulira Mulungu nkhawa zathu.

Iye amadziwa bwino zimene zimatichititsa kuti tizikumana ndi mavuto.​—Salimo 103:14.

Amatidziwa bwino kuposa mmene eniakefe timadzidziwira.​—1 Yohane 3:20.

“Amatidera nkhawa.”​—1 Petulo 5:7.

M’dziko latsopano, Mulungu “adzapukuta misozi yonse” m’maso mwathu.​—Chivumbulutso 21:4.

Ngati Muli ndi Vuto la Matenda

Monga tanenera kale, anthu ena amakhala ndi maganizo ofuna kudzipha chifukwa cha matenda enaake amaganizo. Ngati inunso muli ndi vuto limeneli musachite manyazi kupempha munthu wina kuti akuthandizeni. Ngakhale Yesu anavomereza mfundo yakuti anthu amene akudwala ndi amene amafuna dokotala. (Mateyu 9:12) Mfundo yolimbikitsa ndi yakuti matenda ambiri ali ndi mankhwala amene angakuthandizeni kupezako bwino. *

M’Baibulo muli lonjezo lolimbikitsa kwambiri. Lonjezo lake n’lakuti m’dziko lapansi latsopano palibe amene adzanene kuti: “Ndikudwala.” (Yesaya 33:24) Mulungu walonjeza kuti pa nthawi imeneyo, “zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” (Yesaya 65:17) Koma padakali pano, yesetsani kupirira mavuto amene mukukumana nawo pa moyo wanu. Muzikhulupiriranso kuti pa nthawi yake Mulungu adzathetsa matenda ovutika maganizo.​—Chivumbulutso 21:1-4.

WERENGANI ZAMBIRI PA NKHANIYI M’MUTU 9 M’BUKU LACHIWIRI

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani ngati makolo anu amafuna kudziwa china chilichonse chomwe mukuchita pa moyo wanu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Dziwani kuti achinyamata ambiri amene amadwala matenda amaganizo samadzipha.

^ ndime 18 Akhristu amene akuvutika maganizo angapemphenso thandizo kwa akulu mumpingo.​—Yakobo 5:14, 15.

^ ndime 31 Kuti mudziwe zambiri, werengani Mutu 13.

LEMBA

“Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”​—Afilipi 4:6, 7.

MFUNDO YOTHANDIZA

Mukakhumudwa ndibwino kupita kokayenda. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mtima wanu ukhale m’malo komanso kuti mumveko bwino.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Munthu akadzipha amavutitsanso anthu ena.

ZOTI NDICHITE

Ndikamaona ngati kuti anthu sakundikonda komanso ndikamadziona ngati ndine wosafunika, ndidzapita kwa (lembani dzina la munthu amene mudzamuuze mavuto anu) ․․․․․

Chinthu chimodzi chimene ndimayamikira pa moyo wanga ndi ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kukumbukira mfundo yakuti ngakhale mavuto atakula bwanji adzatha, kungakuthandizeni bwanji mukamakumana ndi mavuto?

● Kodi anthu ena amavutika bwanji munthu akadzipha?

[Mawu Otsindika patsamba 104]

“Nthawi zina ndinkavutika kwambiri maganizo moti ndinkangofuna kufa. Koma panopa zinthu zikuyenda bwino chifukwa cholimbikira kupemphera komanso chifukwa chothandizidwa kuchipatala.”​—Anatero Heidi

[Bokosi patsamba 100]

Ngati Mukuvutika Kwambiri Maganizo

Nthawi zina anthu ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankathedwa nzeru chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo pa moyo wawo. Taonani zitsanzo izi:

Rabeka: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, ndiye ndi bwino ndingofa.”​—Genesis 25:22.

Mose: “Chonde, ingondiphani kuti tsokali lindichoke.”​—Numeri 11:15.

Eliya: “Chotsani moyo wanga Yehova, pakuti sindine woposa makolo anga.”​—1 Mafumu 19:4.

Yobu: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda, . . . mukanati mundiikire nthawi n’kudzandikumbukira.”​—Yobu 14:13.

Patapita nthawi, moyo wa munthu aliyense amene tamutchula pamwambapa unayamba kuyendanso bwino mosiyana ndi mmene ankaganizira. Inunso mukakumana ndi mavuto, dziwani kuti zinthu zikhoza kuyambanso kuyenda bwino pa moyo wanu.

[Chithunzi patsamba 102]

Maganizo ofuna kudzipha ali ngati mitambo ya mvula yomwe imakhalapo kwa nthawi yochepa