Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kulakwa Kufuna Kuchitako Zinthu Zina Pandekha?

Kodi N’kulakwa Kufuna Kuchitako Zinthu Zina Pandekha?

Mutu 15

Kodi N’kulakwa Kufuna Kuchitako Zinthu Zina Pandekha?

Ikani chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi kamene kakufotokoza zimene munganene:

1. Yerekezani kuti muli kuchipinda kwanu ndipo chitseko n’chotseka. Kenako m’bale wanu akungolowa osagogoda.

□ ‘Palibe vuto. Inenso ndimachita zomwezo ndikamalowa kuchipinda kwake.’

□ ‘Chipongwetu chimenechi. Nanga ndikanakhala kuti ndikuvala?’

2. Yerekezani kuti mwangofika kumene kunyumba ndipo makolo anu akuyamba kukufunsani mafunso ambirimbiri. “Unali kuti? Unali ndi ndani? Mumakatani?”

□ ‘Palibe vuto, chifukwa ndimawauza chilichonse.’

□ ‘Zimenezi sizimandisangalatsa. Akamandifunsa mafunso ambiri ndiye kuti sandikhulupirira.’

MULI wamng’ono simunkadandaula anthu akamadziwa chilichonse chimene mukuchita. M’bale wanu ankati akalowa kuchipinda kwanu osagogoda munkasangalala kuti mwapeza wosewera naye. Makolo anu ankati akamakufunsani mafunso munkangoyankha bwinobwino. Nthawi imeneyo simunkaona vuto lina lililonse. Koma panopa simufuna kuti anthu azidziwa chilichonse chimene mukuchita. Mnyamata wina wazaka 14, dzina lake Corey, ananena kuti: “Nthawi zina sindifuna kuti anthu azidziwa zimene ndikuchita.” Tiyeni tione mbali ziwiri zimene zimakhala zovuta kwambiri ngati mukufuna kuchita zinthu panokha.

Nthawi Imene Mukufuna Kukhala Panokha

Pali zifukwa zambiri zimene zingakuchititseni kufuna kukhala panokha. Nthawi zina mungafune ‘kupumula pang’ono.’ (Maliko 6:31) Kapena mungafune kupemphera potsatira zimene Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko ndipo pemphera kwa Atate wako.” (Mateyu 6:6; Maliko 1:35) Koma vuto lingakhale lakuti, mukadzitsekera kuchipinda kwanu (ngati muli ndi chipinda chanu) kuti mupemphere, makolo anu sangadziwe kuti mwadzitsekera chifukwa chakuti mukufuna kupemphera. Komanso abale anu sangamvetse zoti mukufuna kukhala panokha.

Zimene mungachite. M’malo mokangana ndi anthu ena chifukwa chakuti mukufuna kukhala panokha chitani zotsatirazi:

● Mukamachita zinthu ndi azibale anu, yesani kukhazikitsa malamulo oti ana nonse muzitsatira. Mwina mungapemphe makolo anu kuti akuthandizeni pokonza malamulowo. *

● Mukamachita zinthu ndi makolo anu, muziyesetsa kumvetsa maganizo awo. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Rebekah, ananena kuti: “Nthawi zina makolo anga amafuna kudziwa kuti zinthu zikuyenda bwanji pa moyo wanga. Koma kunena zoona, inenso ndikanakhala kuti ndili ndi mwana ndikanachita zomwezo, makamaka chifukwa choti achinyamata akukumana ndi mavuto ambiri masiku ano.” Mofanana ndi Rebekah, kodi mumamvetsa chifukwa chake makolo anu amakuderani nkhawa?​—Miyambo 19:11.

● Dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene ndakhala ndikuchita zimachititsa kuti makolo anga azindikayikira? Kodi ndakhala ndikubisa zinazake moti makolo anga amachita kundifufuza kuti adziwe zimene zikuchitika pa moyo wanga?’ Ngati mwayankha kuti ayi, koma makolo anu samakukhulupiriranibe, auzeni mwaulemu mmene mukumvera. Muzimvetsera akamalankhula ndipo onetsetsani kuti simukuchita chilichonse chomwe chingawonjezere vutolo.​—Yakobo 1:19.

Mukamafuna Kupeza Anzanu

Mukamakula n’zachibadwa kufuna kupeza anzanu oti muzicheza nawo. Komanso n’zachibadwa kuti makolo anu azifuna kudziwa anthu amene mumacheza nawo komanso zimene mumachita mukakhala ndi anzanuwo. Koma nthawi zina mungaganize kuti makolo anu amada nkhawa mopitirira malire. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Amy, ananena kuti: “Sindisangalala makolo anga akamafuna kudziwa munthu amene ndikulankhula naye, kuti aziona zimene ndikulemba pafoni kapena kuwerenga maimelo anga.”

Zimene mungachite. Musalole kuti kucheza ndi anzanu kuchititse kuti musamagwirizane ndi makolo anu. Yesani kuchita zotsatirazi:

● Makolo anu azidziwa anzanu amene mumacheza nawo. N’zoona kuti simungasangalale ngati mutadziwa kuti makolo anu akukufufuzani kuti adziwe anzanu amene mumacheza nawo. Koma n’zimene ayenera kuchita ngati inuyo mumawabisira anzanu amene mumacheza nawo. Muzikumbukiranso kuti makolo anu akamadziwa bwino anzanu, sangamade nkhawa kuti mukucheza ndi anthu olakwika.

● Dziwani vuto lenileni: Kodi vuto ndi lakuti makolo anu amafuna kudziwa chilichonse kapena inuyo mukubisa zinazake? Mtsikana wina wazaka 22, dzina lake Brittany, ananena kuti: “Ngati mukukhala ndi makolo anu ndipo akukuderani nkhawa, mungachite bwino kuganizira mfundo iyi: ‘Palibe chifukwa chobisira zomwe ndimachita ngati sindichita zoipa.’ Koma ngati mukubisa zinazake ndiye kuti pali vuto.”

Kodi Mukuyeneradi Kuchita Zinthu Panokha?

Tsopano ganizirani mofatsa zimene mungachite pa nkhani yofuna kuchita zinthu panokha. Lembani mayankho anu pamizere ili m’munsiyi:

Choyamba: Dziwani vuto lenileni. Kodi ndi nthawi iti imene inuyo mungafune kuchita zinthu panokha?

․․․․․

Chachiwiri: Yesani kumvetsa mmene makolo anu akuganizira. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimapangitsa kuti makolo anu azikuderani nkhawa mopitirira malire?

․․․․․

Chachitatu: Pezani njira yothetsera vutolo. Kodi mukuganiza kuti pali zinazake zomwe mukuchita zomwe zikuwonjezera vutolo? Ngati mwayankha kuti inde, kodi mungatani kuti musinthe? Kodi mungafune kuti makolo anu akuthandizeni bwanji pa mavuto anuwo?

․․․․․

Chachinayi: Kambiranani. Lembani zimene mungachite kuti mukambirane ndi makolo anu pa nkhani ya kuchita zinthu panokha.

․․․․․

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira ngati mayi kapena bambo anu anamwalira?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri, werengani Mutu 6.

LEMBA

“Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi.”​—2 Timoteyo 2:15.

MFUNDO YOTHANDIZA

Mukamakambirana ndi makolo anu nkhani yokhudza kufuna kuchita zinthu zina panokha, muzipewa kunena zinthu zimene mukuona kuti makolo anu amalakwitsa. Koma muzinena zinthu zomwe zingathandize kuti mupeze njira yothetsera vutolo.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngati simubisira makolo anu chilichonse, iwo sangamakukayikireni.

ZOTI NDICHITE

Kuti makolo anga azindikhulupirira (kapena kuti ayambirenso kundikhulupirira) ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani makolo ayenera kudziwa zimene zikuchitika pa moyo wanu?

● Kodi mukamayesetsa kulankhula bwino ndi makolo anu panopa, zingadzakuthandizeni bwanji m’tsogolo?

[Mawu Otsindika patsamba 108]

“Makolo anu safuna kuti mukumane ndi mavuto ndipo nthawi zina angaoneke ngati akulowelera kwambiri nkhani zanu. Zimenezi sizisangalatsa koma zoona zake n’zakuti, ndikanakhala kuti inenso ndili ndi mwana ndikanachita zomwezo.”​—Anatero Alana

[Chithunzi patsamba 109]

Munthu amalandira malipiro chifukwa cha ntchito imene wagwira. Nanunso pali zimene muyenera kuchita kuti makolo anu azikukhulupirirani