Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Bwanji Ndingosiya Sukulu?

Bwanji Ndingosiya Sukulu?

Mutu 19

Bwanji Ndingosiya Sukulu?

Kodi mukuganiza kuti muyenera kusiya sukulu mutafika nayo pati? ․․․․․

Kodi makolo anu akufuna kuti muphunzire mpaka pati? ․․․․․

KODI mayankho a mafunso awiriwa afanana? N’kutheka kuti afanana koma ngati mudakali pa sukulu, mwina nthawi zina mumalakalaka mutangosiyira sukulu panjira. Kodi inuyo munayamba mwakhalapo ndi maganizo ofanana ndi amene alembedwa m’munsiwa?

“Nthawi zina ndimadzuka wotopa kwambiri moti ndimangolakalaka nditapitirizabe kugona. Ndimakhala ndi maganizo akuti, ‘Pali phindu lanji kupita kusukulu n’kukaphunzira zinthu zoti sindidzazigwiritsa ntchito n’komwe?’”​—Anatero Rachel.

“Nthawi zambiri sukulu imafika ponditopetsa kwambiri, moti ndimalakalaka nditangoisiya n’kukayamba ntchito. Ndimaona kuti sukulu ikungonditayitsa nthawi ndipo kuli bwino ndingoyamba ntchito kuti ndizipeza ndalama.”​—Anatero John.

“Ndinkapita kusukulu inayake ya m’tawuni koma ana ake ankandisala. Zomwe tinkaphunzira sizinali zovuta kwenikweni, koma nthawi zonse ndinkangooneka ngati mlendo ndipo nthawi zambiri ndinkangokhala ndekhandekha. Ndipo ngakhale ana ena omwe nawonso ankasalidwa, sankafunanso kumacheza ndi ine. Zimenezi zinkandichititsa kukhala ndi maganizo ofuna kusiya sukulu.”​—Anatero Ryan.

“Usiku uliwonse ndinkakhala ndi zinthu zoti ndilembe zomwe zinkanditengera maola pafupifupi 4. Mahomuweki ankandichulukira kwambiri chifukwa ankangotsatizana. Ndinafika potopa nawo ndipo ndinayamba kuganiza zongosiya sukulu.”​—Anatero Cindy.

“Nthawi ina kunamveka mphekesera yoti wina watchera bomba kusukulu kwathu. Ana atatu ankafuna kudzipha, ndipo mwana wina anadziphadi. Kunalinso magulu a anthu okonda zachiwawa omwe nthawi zambiri ankamenyana. Nthawi zina ndinkaona kuti sindingapitirize kukhala malo oterewa ndipo ndi bwino kungosiya sukulu.”​—Anatero Rose.

Kodi inuyo munakumanapo ndi mavuto ngati amenewa? Ngati ndi choncho, ndi vuto liti kwenikweni lomwe linakuchititsani kuganiza zosiya sukulu?

․․․․․

N’kutheka kuti panopo mwatsimikiza zosiya sukulu, koma kodi mungadziwe bwanji ngati mukusiya pa nthawi yake kapena ngati mukusiya chifukwa chongotopa nayo? Kuti tiyankhe funso limeneli, choyamba tikufunika kudziwa tanthauzo la kusiyira sukulu panjira.

Kusiyana Kwa Kusiya Sukulu Ndi Kusiyira Panjira

Fotokozani kusiyana kwa kusiya sukulu ndi kusiyira sukulu panjira.

․․․․․

Kodi mukudziwa kuti m’mayiko ena mwana amaloledwa kusiya sukulu ngati ataphunzira kwa zaka 5 kapena 8 zokha? Koma m’mayiko ena ana amayenera kuphunzira sukulu kwa zaka zoposa 10. Zimenezi zikusonyeza kuti msinkhu komanso kalasi yomwe munthu akhoza kusiyira sukulu imasiyana potengera dziko lomwe munthu akukhala.

Komanso mayiko ena amalola ana kumaphunzirira kunyumba maphunziro ena, kapenanso maphunziro onse popanda kupita kusukulu. Ana amene analolezedwa ndi makolo awo kuti azingophunzirira kunyumba kwawo, ndiye kuti sanasiyire sukulu panjira.

Koma ngati mukuganiza zosiya kuphunzira musanamalize maphunziro onse oyenerera, kaya mukuphunzirira kunyumba kapena kusukulu, muyenera kuganizira mafunso otsatirawa:

Kodi malamulo a dzikolo amati chiyani pa nkhaniyi? Monga tanenera kale, dziko lililonse limakhala ndi malamulo akeake onena za nthawi imene mwana amayenera kuphunzira sukulu. Kodi kwanuko boma limafuna kuti mwana aliyense aphunzire mpaka kalasi yanji? Kodi inuyo mwafika kalasi imeneyoyo? Ngati mutanyalanyaza malangizo a m’Baibulo akuti ‘muzimvera olamulira akuluakulu,’ n’kusiya sukulu musanafike kalasi imeneyi ndiye kuti mwasiyira sukulu panjira.​—Aroma 13:1.

Kodi ndakwaniritsa zolinga zanga? Kodi mukuphunzira sukulu kuti mudzachite chiyani? Mukufunika kukhala ndi zolinga zopitira kusukulu. Ngati mulibe zolinga, mungakhale ngati munthu amene wakwera sitima koma asakudziwa kumene akupita. Mungachite bwino kukambirana ndi makolo anu komanso kulemba zimene zili patsamba 139 pa mutu wakuti,  “Zolinga Zanga pa Nkhani ya Maphunziro.” Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti maganizo anu onse azikhala pa maphunziro amene angakuthandizeni kukwaniritsa zolingazo. Kungakuthandizeninso inuyo ndi makolo anu kudziwa pamene muyenera kufika ndi maphunziro anu.​—Miyambo 21:5.

Aphunzitsi anu komanso anthu ena akhoza kukuuzani kuti sukulu yanu mudzafike nayo pati. Komabe makolo anu ndi amene ali ndi mphamvu yokuuzani zoyenera kuchita. (Miyambo 1:8; Akolose 3:20) Ngati mutasiya sukulu musanakwaniritse zolinga zimene inuyo ndi makolo anu munagwirizana ndiye kuti mwasiyira sukulu panjira.

Kodi ndikufuna kusiya sukulu chifukwa chiyani? Musamadzipusitse. (Yeremiya 17:9) Mwachibadwa munthu amapereka zifukwa zooneka ngati zomveka zochitira zimene akufuna.​—Yakobo 1:22.

Lembani zifukwa zomveka zimene zingakuchititseni kuti musiyire sukulu panjira.

․․․․․

Lembani zifukwa zina zosamveka zosiyira sukulu panjira.

․․․․․

Kodi zifukwa zomveka zimene mwalemba ndi zotani? N’kutheka kuti mwalemba zoti mukufuna muzigwira ntchito n’cholinga choti muzithandiza banja lanu kapena kuti muyambe ntchito yongodzipereka yophunzitsa anthu Baibulo. Zifukwa zosamveka zingakhale zoti mwatopa ndi zolemba mayeso kapena homuweki. Koma nkhani ndi yoti, kodi cholinga chanu chenicheni chosiyira sukulu ndi chiyani, ndipo cholingacho ndi chomveka kapena chosamveka?

Onaninso zimene mwalemba pamwambapa ndipo lembani manambala 1 mpaka 5 pa chifukwa chilichonse (mulembe manambalawo potengera chifukwa chachikulu chimene mukufuna kusiyira sukulu. Muike nambala 1 pa chifukwa chosafunika kwenikweni ndipo nambala 5 muike pa chifukwa chofunika kwambiri). Ngati mukufuna kusiya sukulu kuti muthawe mavuto, dziwani kuti mudzakhumudwa kwambiri.

Kodi Kusiyira Sukulu Panjira Kuli Ndi Vuto Lililonse?

Kusiyira sukulu panjira kuli ngati kudumpha musitima musanafike kumene mukupita. N’kutheka kuti anthu amene akwera m’sitimamo ndi osachezeka komanso mwakhala mopanikizika kwambiri. Koma ngati mutadumpha ndiye kuti simungakafike kumene mukupita komanso mukhoza kuvulala kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi kusiyira sukulu panjira. Simungakwaniritse zolinga zanu komanso mukhoza kukumana ndi mavuto amene angaonekere nthawi yomweyo ndipo ena angadzaonekere m’tsogolo. Ena mwa mavuto amene mungakumane nawo ndi awa:

Mavuto oonekera nthawi yomweyo: Mukhoza kuvutika kuti mupeze ntchito. Ndipo ngati mungaipeze ikhoza kukhala ya malipiro otsika kwambiri poyerekezera ndi imene mukanapeza mukanamaliza sukulu. Kuti mupeze zinthu zofunika pa moyo wanu mungafunike kugwira ntchito maola ambiri komanso pamalo amene si abwino poyerekezera ndi kusukulu kumene muli.

Mavuto odzaonekera m’tsogolo: Kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene amasiyira sukulu panjira nthawi zambiri sakhala ndi thanzi labwino, amachita zinthu zomwe zimachititsa kuti amangidwe komanso amadalira mabungwe kuti aziwathandiza.

Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti ngati munthu wamaliza sukulu ndiye kuti sangakumane ndi mavuto amenewa. Koma si nzeru kusiyira sukulu panjira mukudziwa kuti mudzakumana ndi mavuto amenewa.

Ubwino Wosasiyira Sukulu Panjira

Mukhoza kukhala ndi maganizo osiya sukulu ngati mwalephera mayeso kapena ngati zinthu sizikukuyenderani bwino kusukulu ndipo mukaganizira mavuto amene mungadzakumane nawo m’tsogolo sangaoneke ngati aakulu poyerekeza ndi amene mukukumana nawo panopa. Koma musanaganize zongosiya sukulu, onani zimene ana asukulu amene tawatchula kumayambiriro kwa mutuwu ananena chifukwa chakuti sanasiyire sukulu panjira.

“Ndaphunzira kuti kupirira kumathandiza munthu kukhala woganiza bwino. Ndaphunziranso kuti ngati ukufuna kumasangalala pochita zinazake, uyenera kusintha mmene umaganizira. Chifukwa chosasiyira sukulu panjira ndinaphunzira zinthu zimene zingadzandithandize ndikadzayamba ntchito.”​—Anatero Rachel.

“Panopa ndazindikira kuti ndikamalimbikira sukulu ndikhoza kudzakwaniritsa zolinga zimene ndili nazo. Ndikuphunzira zinthu zimene zidzandithandize kugwira ntchito imene ndikufuna yokonza mashini osindikizira mabuku.”​—Anatero John.

“Chifukwa chakuti sindinasiyire sukulu panjira ndaphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino kwambiri. Sukulu yandithandiza kuphunzira kuti ndisamakhumudwe ena akandiuza mfundo zosiyana ndi mfundo zanga komanso ndaphunzira kufotokoza maganizo anga momveka bwino zomwe zimandithandiza pamene ndikugwira ntchito yolalikira.”​—Anatero Ryan.

“Sukulu yandithandiza kuphunzira njira zabwino zothetsera mavuto, kaya kusukulu kapena kulikonse. Kuphunzira mmene ndingathetsere mavuto akusukulu komanso mavuto ena kwandithandiza kuti ndizichita zinthu mwanzeru.”​—Anatero Cindy.

“Sukulu yandithandiza kuti ndikonzekere kulimbana ndi mavuto a kuntchito. Komanso kusukulu ndinkakumana ndi zinthu zambiri zimene zinkafuna kuti ndifotokoze zimene zimandichititsa kukhulupirira mfundo za m’Baibulo, choncho ndingati sukulu inandithandiza kulimbitsa chikhulupiriro changa.”​—Anatero Rose.

Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake, ndipo munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza.” (Mlaliki 7:8) Choncho, m’malo mosiyira sukulu panjira, yesetsani kupeza njira yabwino yothetsera mavuto amene mukukumana nawo kusukuluko. Kuchita zinthu mosapupuluma kotereku kudzakuthandizani kuti zinthu zikuyendereni bwino pamapeto pake.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani ngati mukufuna kusiya sukulu chifukwa chakuti simumagwirizana ndi aphunzitsi anu?

LEMBA

“Aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”​—Miyambo 21:5.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati zikukuvutani kuzolowera moyo wa kusukulu, funsani makolo anu zimene mungachite kuti musamapanikizike kwambiri. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mudzamalize sukulu yanuyo.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ana amene amakonda kujomba kusukulu nthawi zambiri amasiyiranso sukulu panjira.

ZOTI NDICHITE

Ngati ndikuona kuti phunziro linalake likundivuta, m’malo molisiya ndidzachita zotsatirazi: ․․․․․

Ngati ndikufuna kusiya sukulu chifukwa chongotopa nayo, ndidzachita zotsatirazi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani muyenera kuphunzira kuwerenga, kulemba komanso kuwerengetsera zinthu?

● Kodi kukhala ndi zolinga zing’onozing’ono nthawi imene muli pa sukulu kungakuthandizeni bwanji?

● N’chifukwa chiyani ndi bwino kusankhiratu ntchito imene mukufuna kudzagwira mukadzamaliza sukulu?

[Mawu Otsindika patsamba 140]

“N’zosatheka kupeweratu mavuto onse pa moyo wanu. Moyo wa kusukulu umakuthandizani kuti muzichita zinthu molimba mtima, zomwe n’zothandiza mukadzayamba ntchito komanso kulikonse komwe mungapite.”​—Anatero Ramona

[Bokosi patsamba 139]

 Zoti Muchite

Zolinga Zanga pa Nkhani ya Maphunziro

Cholinga chachikulu cha maphunziro ndi kukuthandizani kuti mudzapeze ntchito yomwe ingadzakuthandizeni kupeza zofunikira pa moyo wanu komanso wa banja lanu. (2 Atesalonika 3:10, 12) Kodi mwasankha kale ntchito imene mukufuna kudzagwira? Ngati mwasankha, kodi mukuchita zotani kuti zimene mukuphunzira kusukulu zidzakuthandizeni mukadzayamba ntchitoyo? Kuti mudziwe ngati maphunziro amene mukuchita adzakuthandizeni, yankhani mafunso otsatirawa:

Kodi ndimachita bwino zinthu ziti? (Mwachitsanzo, kodi mumacheza bwino ndi anthu? Kodi mumakonda kugwira ntchito zamanja ndiponso kukonza zinthu? Kodi muli ndi luso lodziwa chimene chayambitsa mavuto moti simuvutika kuwathetsa?) ․․․․․

Kodi ndi ntchito ziti zimene zingagwirizane ndi luso limene ndili nalo? ․․․․․

Kodi ndi ntchito ziti zimene ndingazipeze kumene ndimakhala kuno? ․․․․․

Kodi panopa ndikuchita maphunziro otani omwe angandithandize kudzapeza ntchito? ․․․․․

Kodi ndingaphunzirenso zinthu ziti zomwe zingadzandithandize kuti ndizidzagwira bwino ntchito imene ndikufunayo? ․․․․․

Muzikumbukira kuti cholinga chanu chopitira kusukulu n’choti muphunzire zinthu zimene zidzakuthandizeni m’tsogolo. Choncho ndi bwino kusiya sukulu pamene cholinga chanu chakwaniritsidwa m’malo momangophunzirabe pofuna kuthawa udindo umene anthu amene amaliza sukulu amakhala nawo. Kuchita zimenezi kungakhale ngati kumangokhalabe musitima koma mutafika kumene mumapita. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 69 Kuti mudziwe zambiri werengani Mutu 38, m’Buku Lachiwiri.

[Chithunzi patsamba 138, 139]

Kusiyira sukulu panjira kuli ngati kudumpha musitima musanafike kumene mukupita