Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?

Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?

Mutu 22

Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?

Kodi mayi kapena bambo anu anachokera dziko lina?

□ Inde □ Ayi

Kodi chinenero kapena chikhalidwe cha anzanu a kusukulu n’chosiyana ndi cha dziko lomwe munachokera?

□ Inde □ Ayi

“Tinachokera ku Italy ndipo tinazolowera kusonyezana chikondi pagulu. Panopa tikukhala ku Britain komwe anthu ake amachita zinthu modzipatsa ulemu kwambiri. Ndikakhala ndi anthu a ku Britain amaona kuti sindimadzipatsa ulemu pamene ndikakhala ndi anthu a ku Italy amaona kuti ndimadzipatsa ulemu kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti ndizidzimva ngati mlendo ndikakhala ku Britain komanso ndikapita kwathu ku Italy.”​—Anatero Giosuè, ku England.

“Kusukulu aphunzitsi anandiuza kuti ndiziwayang’ana akamandilankhula. Koma ndikawayang’ana bambo anga akamandilankhula ankati ndine wamwano. Ndinaona kuti ndinkafunika kutsatira zikhalidwe ziwiri, china cha kunyumba china cha kusukulu.”​—Anatero Patrick yemwe anabadwira ku France koma makolo ake anachokera ku Algeria.

MAKOLO anu atasamukira ku dziko lina ayenera kuti anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Kusamukako kunachititsa kuti ayambe kuchita zinthu ndi anthu osiyana nawo chinenero, chikhalidwe komanso kavalidwe. Mwachidziwikire, zimenezi zinachititsa kuti azinyozedwa komanso kusalidwa.

Kodi nanunso zimenezi zimakuchitikirani? M’munsimu mwalembedwa mavuto amene achinyamata ena omwe akukhala ku dziko lina anakumana nawo. Ikani chizindikiro ichi ✔ pamene pali vuto limene mukuona kuti ndi lovuta kwambiri kuthana nalo.

Kusekedwa. Mtsikana wina dzina lake Noor anasamuka ku Jordan kupita ku North America limodzi ndi makolo ake ali wamng’ono kwambiri. Iye anati: “Zimene tinkavala zinkaoneka zosiyana ndi anthu a m’dzikolo moti anthu ankatiseka kwambiri. Ankatisekanso chifukwa chakuti zinthu zimene ankaona kuti ndi zoseketsa ife sitinkaziona choncho chifukwa chosiyana chikhalidwe.”

Kudzimva mlendo ndi kwanu komwe. Mtsikana wina dzina lake Nadia anati: “Ndinabadwira ku Germany. Popeza makolo anga ndi a ku Italy, ndikamalankhula chinenero cha ku Germany mawu anga ankamveka kuti ndine wa ku Italy moti anthu a kusukulu kwathu ankandinyoza kuti ndine “chitsiru chopanda kwawo.” Koma ndikapita ku Italy, ndikamalankhula chinenero cha ku Italy, mawu anga amamveka ngati ndine wa ku Germany. Ndimaona ngati ndilibe kwathu chifukwa kulikonse komwe ndapita ndimaona ngati ndine mlendo.”

Kusiyana chikhalidwe ndi makolo anu. Mtsikana wina dzina lake Ana anasamukira ku England limodzi ndi makolo ake ali ndi zaka  8. Iye anati: “Ine ndi mchimwene wanga sitinavutike kuzolowera chikhalidwe cha ku London. Koma makolo anga anavutika kwambiri chifukwa anali atazolowera kukhala pachilumba china chaching’ono cha Madeira, ku Portugal.”

Voeun anasamukira ku Australia limodzi ndi makolo ake, ochokera ku Cambodia, ali ndi zaka zitatu. Iye anati: “Makolo anga anavutika kwambiri kuzolowera chikhalidwe cha ku Australia. Moti nthawi zina bambo anga ankakwiya komanso kukhumudwa chifukwa sindinkamvetsa mmene amaganizira.”

Kusiyana chilankhulo ndi makolo anu. Ian anasamuka ku Ecuador, komwe amalankhula Chisipanishi, kupita ku New York limodzi ndi makolo ake ali ndi zaka 8. Atakhala ku United States kwa zaka 6 ananena kuti: “Panopa ndimalankhula kwambiri Chingelezi kusiyana ndi Chisipanishi chifukwa ndikamalankhula ndi mchimwene wanga, aphunzitsi anga komanso anzanga ndimalankhula nawo m’Chingelezi. Chifukwa cha zimenezi mawu ambiri a Chisipanishi ndayamba kuwaiwala.”

Lee, yemwe anabadwira ku Australia koma makolo ake anachokera ku Cambodia, ananena kuti: “Ndikamalankhula ndi makolo anga ndipo ndikufuna kuwafotokozera mmene ndikumvera pa nkhani inayake, ndimaona kuti sindikudziwa mawu oyenera a m’chinenero chawo ofotokozera zimene ndikufunazo.”

Noor, yemwe tamutchula kale uja ananenanso kuti: “Bambo anga ankatikakamiza kuti tizilankhula chinenero chawo tikakhala kunyumba koma ifeyo sitinkafuna zomalankhula Chiarabu. Tinkaona kuti kuphunzira Chiarabu n’kungodzivutitsa pa zinthu zopanda phindu. Anzathu onse ankalankhula Chingelezi, mapulogalamu onse amene tinkaonera pa TV analinso m’Chingelezi, ndiye chodzivutitsira ndi Chiarabu n’chiyani?”

Zimene Mungachite

Zimene zafotokozedwa m’ndime zimenezi zikusonyeza kuti anthu enanso akukumana ndi mavuto ngati anuwo. M’malo molimbana ndi kuthetsa mavutowo mungayese kungoiwala za chikhalidwe chanu n’kuyesetsa kuzolowera chikhalidwe cha anthu a m’dera limene mukukhalalo. Koma kuchita zimenezi kukhoza kukhumudwitsa makolo anu ndipo inuyo simungafune kuti zimenezi zichitike. Choncho ndi bwino kungophunzira kupirira mavuto. Onani mfundo zothandiza zotsatirazi:

Zoyenera kuchita mukamasekedwa. Olo mutachita zotani, sizingatheke kuti muzigwirizana ndi aliyense. Anthu amene amakonda kuseka anzawo nthawi zonse amapeza chifukwa chochitira zimenezi. (Miyambo 18:24) Choncho, kuyesa kuwathandiza kuti asinthe mmene amaganizira n’kosathandiza. Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akum’dzudzula.” (Miyambo 15:12) Zimene anthu okusekaniwo amanena zimangosonyeza maganizo awo olakwika osati zimene inuyo mumalakwitsa.

Zimene mungachite ngati mukudzimva ngati mlendo. Mwachibadwa anthufe timafuna kuti tizikhala ndi gulu linalake lomwe timafanana nalo zochita komanso chikhalidwe. Koma si bwino kuganiza kuti munthu amakhala wofunika chifukwa cha chikhalidwe chake kapena chifukwa cha banja limene akuchokera. Mwina anthu akhoza kumakuonani wofunika chifukwa cha banja limene mukuchokera koma si mmene Mulungu amaonera anthu. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Mukamayesetsa kuchita zinthu zimene Yehova Mulungu amasangalala nazo, iye adzayamba kukuonani ngati mwana wa m’banja lake. (Yesaya 43:10; Maliko 10:29, 30) Palibe chinthu chofunika kwambiri kuposa kukhala m’banja la Mulungu.

Zimene mungachite ngati mumasiyana chikhalidwe ndi makolo anu. M’banja lililonse, ana ndi makolo amaona zinthu zina mosiyana. Kungoti nkhani yanuyi ikuoneka ngati yaikulu chifukwa mukuona kuti makolo anu akufuna kuti muzitsatira chikhalidwe cha dziko limene munachokera pamene inuyo mukufuna kumatsatira chikhalidwe cha m’dziko limene mukukhalalo. Ngakhale zili choncho, ngati mukufuna kuti zinthu zikuyendereni bwino pa moyo wanu, muyenera ‘kulemekeza bambo anu ndi amayi anu.’​—Aefeso 6:2, 3.

M’malo mongofikira kunena kuti simukufuna kutsatira chikhalidwe cha makolo anuwo, mungachite bwino kufufuza kaye chifukwa chake makolo anu amakonda chikhalidwe chimenechocho. (Miyambo 2:10, 11) Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimene zimachitika m’chikhalidwechi n’zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo? Ngati sizotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo, ndi zinthu ziti za m’chikhalidwe chimenechi zimene sizindisangalatsa? Kodi ndingafotokoze bwanji mwaulemu maganizo anga pa nkhaniyi kwa makolo anga?’ (Machitidwe 5:29) Komabe zingakhale zosavuta kuti mumvetse maganizo a makolo anu komanso kufotokoza maganizo anu momveka bwino ngati mutakhala kuti mumalankhula chinenero chawo bwinobwino.

Zimene mungachite ngati mumasiyana chilankhulo ndi makolo anu. Mabanja ena amaona kuti akamakakamiza ana awo kulankhula chinenero cha kwawo chokha akakhala kunyumba, anawo amakhala ndi mwayi wophunzira zinenero ziwiri nthawi imodzi. Nanunso mungachite bwino kuyesa njira imeneyi kunyumba kwanu. Mungawapemphenso makolo anu kuti akuphunzitseni mmene amalembera chinenerocho. Stelios, yemwe anakulira ku Germany koma chinenero cha kwawo ndi Chigiriki, ananena kuti: “Tsiku lililonse makolo anga ankandiwerengera vesi linalake la m’Baibulo kenako ndinkalemba zimene andiwerengerazo. Panopa ndimatha kuwerenga komanso kulemba Chigiriki ndi Chijeremani.”

Kodi ubwino wina wophunzira chinenero cha makolo anu ndi wotani? Giosuè, yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndinaphunzira chinenero cha makolo anga chifukwa ndinkafuna kuti ndizitha kucheza nawo momasuka nkhani za kukhosi kwanga, makamaka nkhani zauzimu. Kuphunzira chinenero chawo kwandithandiza kuti ndizitha kumvetsa mmene akumvera pa nkhani inayake komanso kuti ndizitha kufotokoza zinthu m’njira imene iwowo angamvetse mmene ndikumvera.”

Muziuona Kukhala Mwayi

Kusiyana chikhalidwe kungakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi anthu ena m’malo mokuchititsani kukhala ngati mlendo. Achinyamata ambiri achikhristu aona kuti akufunika kuyesetsa kugwirizana ndi anthu n’cholinga choti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu enanso ochokera m’mayiko ena. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Salomão, yemwe anasamukira ku London ali ndi zaka 5, anati: “Ndi chinthu chapadera kukwanitsa kufotokoza mfundo za m’Malemba m’zinenero ziwiri. Ndinatsala pang’ono kuiwaliratu chinenero changa choyamba chomwe ndi Chipwitikizi. Koma panopa ndili mumpingo wa Chipwitikizi moti ndimatha kulankhula bwinobwino Chingelezi ndi Chipwitikizi.”

Noor, yemwe tamutchula kale uja, anaona kuti m’dzikolo mukufunika anthu olengeza za Ufumu omwe amatha kulankhula Chiarabu. Iye anati: “Ndayambiranso kuphunzira Chiarabu kuti ndikumbutsire zimene ndinaiwala. Panopa ndikamalankhula ndimafuna kuti anthu azindiuza ndikatchula mawu molakwika. Ndimachita zimenezi chifukwa ndikufunitsitsa kuphunzira Chiarabu.”

Nanunso muli ndi mwayi ngati mukudziwa bwino zikhalidwe zingapo za anthu komanso ngati mumatha kulankhula zinenero ziwiri kapena kuposa. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzimvetsa mosavuta mmene anthu akumvera komanso muzitha kuwayankha bwino mafunso omwe ali nawo onena za Mulungu. (Miyambo 15:23) Preeti, yemwe anabadwira ku England koma makolo ake anachokera ku India, anati: “Sindimavutika ndikakhala mu utumiki chifukwa ndimadziwa bwino zikhalidwe zonse ziwiri. Ndimadziwa zimene anthu azikhalidwe zonsezi amakhulupirira komanso mmene amaganizira.”

Nanunso mungachite bwino kuona kuti kukhala kwanu m’dziko lina ndi mwayi. Musaiwale kuti Yehova amakukondani mosatengera kuti inuyo kapena banja lanu munachokera kuti. Mofanana ndi zimene achinyamata otchulidwa m’nkhaniyi anachita, inunso mungagwiritse ntchito zimene mukudziwa komanso zimene mwakumana nazo pothandiza anthu a chikhalidwe chanu kuphunzira za Mulungu wathu wachikondi Yehova, yemwe ndi wopanda tsankho. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muzikhala wosangalala kwambiri.​—Machitidwe 20:35.

LEMBA

“Mulungu alibe tsankho.”​—Machitidwe 10:34.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati anzanu amakusekani chifukwa cha kumene mukuchokera, muzingowanyalanyaza ndipo muzipitirizabe kuoneka wosangalala. Mukamachita zimenezi, adzatopa okha n’kusiya zokusekanizo.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngati mutakhala kuti mumadziwa bwino zinenero ziwiri mukhoza kupeza ntchito mosavuta.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndidziwe bwino chilankhulo cha makolo anga ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kudziwa kumene makolo anu anachokera kungakuthandizeni bwanji kudzidziwa nokha?

● Kodi inuyo muli ndi mwayi uti umene anzanu amene anabadwa ndi kukulira dera limodzi alibe?

[Mawu Otsindika patsamba 160]

“Ndimasangalala ndikamathandiza anthu ena. Ndimatha kufotokoza mfundo za m’Baibulo kwa anthu amene amalankhula Chirasha, Chifulenchi komanso Chimodova.”​—Anatero Oleg

[Chithunzi patsamba 161]

Muziona kusiyana chikhalidwe ngati buliji imene ingakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi anthu ena