Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Mutu 23

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Pa mwambo wopereka mphoto, anthu akuchita phokoso kwambiri ataona kuti atsikana awiri otchuka ahagana komanso kupatsana kisi mwachikondi. Anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo akuona kuti atsikanawo achita bwino kuchita zimenezi pagulu. Pamene ena akuona kuti atsikanawo angochita zimenezi pofuna kutchuka. Kwa masiku ambiri, vidiyo yosonyeza zimene atsikanawa achita ikhala ikubwerezedwa kambirimbiri mu nkhani za pa TV komanso anthu ambiri akhala akuionera pa intaneti.

ZIMENE zafotokozedwa pamwambazi zikusonyeza kuti nkhani yofotokoza za anthu otchuka amene asonyeza kapena kufotokoza poyera kuti amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo imafalitsidwa kwambiri kuposa nkhani zina. Anthu ena amayamikira anthu otere chifukwa cholimba mtima kunena zimenezi, pamene ena sasangalala nazo chifukwa amaona kuti limeneli ndi khalidwe loipa. Anthu ena ambiri amaona kuti kuchita zimenezi kulibe vuto lina lililonse, moti munthu aliyense ali ndi ufulu wochita zimenezi kapena ayi. Daniel wazaka 21 ananena kuti: “Ndili pa sukulu, ana onse, kuphatikizapo amene tinkawaona kuti ali ndi khalidwe labwino, ankaona kuti munthu amene amadana ndi zoti amuna kapena akazi okhaokha azigonana ndi watsankho komanso amadzitenga ngati iyeyo ndiye wabwino.”

Mmene anthu akuluakulu amaonera nkhani imeneyi zikhoza kusiyana ndi mmene ana amaionera komanso anthu a m’mayiko osiyana amaonanso nkhaniyi mosiyana. Koma Akhristu ‘satengekatengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’ (Aefeso 4:14) M’malomwake amatsatira zimene Baibulo limanena.

Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi? Ndipo ngati mumatsatira zimene Baibulo limanena, kodi mungawayankhe bwanji anthu amene amakunenani kuti ndinu watsankho, wodziona ngati wabwino kapenanso kuti mumadana ndi anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo? Tiyeni tikambirane zimene anthu ena anganene kapena kufunsa ndiponso zomwe mungayankhe.

“Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha?”

“Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu anakonza zoti kugonana kuzichitika pakati pa mwamuna ndi mkazi komanso anthuwo akhale kuti ndi okwatirana. (Genesis 1:27, 28; Levitiko 18:22; Miyambo 5:18, 19) Baibulo likamaletsa dama, kapena kuti chiwerewere, limaphatikiza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha komanso kugonana kulikonse kolakwika ngakhale kutakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi.” *​—Agalatiya 5:19-21.

“Kodi iweyo nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha umaiona bwanji?”

“Si kuti ndimadana ndi anthuwo koma sindisangalala ndi zimene amachitazo.”

Kumbukirani kuti ngati mumatsatira mfundo za m’Baibulo ndiye kuti munasankha moyo umenewo ndipo umenewu ndi ufulu wanu. (Yoswa 24:15) Musamachite manyazi kufotokoza mmene mumaonera nkhaniyi.​—Salimo 119:46.

“M’mesa Akhristu amayenera kulemekeza anthu onse, ngakhale atakhala kuti amachita zotani?”

“Kwambiri. Ndipotu Baibulo limati: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.” (1 Petulo 2:17) Choncho Akhristu samadana ndi anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Amachitira chifundo anthu onse, ngakhale amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo.”​—Mateyu 7:12.

“Kodi maganizo akowo si olimbikitsa zoti anthu ogonana ndi amuna kapena akazi anzawo azisalidwa?”

“Ayi. Ineyo ndimadana ndi khalidwe lawolo, osati anthuwo.”

Mukhoza kuwonjezeranso kuti: “Chinthu chinanso chimene ndimadana nacho ndi kusuta fodya. Moti ndikangomva za fodya, si kuipidwa kwake. Koma tiyerekeze kuti iweyo umasuta ndipo umaona kuti kusuta kulibe vuto. Ngakhale titakhala kuti timasiyana maganizo pa nkhaniyi ndikukhulupirira kuti sungadane nane ndipo nanenso sindingadane nawe chifukwa chakuti tili ndi maganizo osiyana. Ndikunama kapena? Ndi mmenenso zilili pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.”

“M’mesa Yesu anatiphunzitsa kuti tizilolerana? Ndiye kodi si zofunika kuti Akhristu onse aziloleranso maganizo a anthu omwe amafuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo?”

“Yesu sanalimbikitse otsatira ake kuti azingololera maganizo a munthu aliyense. Koma anawaphunzitsa kuti “aliyense wokhulupirira iye” adzapulumuka. (Yohane 3:16) Kukhulupirira Yesu kumaphatikizapo kutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino zomwe zimaletsa makhalidwe ena ngati kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.”​—Aroma 1:26, 27.

“Anthu amene amachita zimenezi anabadwa choncho, moti sangasinthe.”

“Ngakhale kuti Baibulo limafotokoza kuti anthu ena amachita zoipa chifukwa chakuti zinthuzo zinazikika mumtima mwawo, koma silifotokoza mmene anthu amene amagona ndi amuna kapena akazi anzawo anapangidwira. (2 Akorinto 10:4, 5) Ngakhale kuti anthu ena amakopeka ndi amuna kapena akazi anzawo, Baibulo limalangiza Akhristu kuti azipewa khalidwe limeneli.”

Mfundo yothandiza: M’malo momangotsutsana za chimene chimachititsa kuti munthu azifuna kugona ndi mwamuna kapena mkazi mnzake, mungachite bwino kufotokoza kuti Baibulo limaletsa khalidwe limeneli. Kuti amvetse, munganenenso kuti: “Anthu ambiri amaganiza kuti nthawi zina munthu amachita zinthu zankhanza chifukwa chakuti anatengera kwa makolo ake ndipo sangasinthe. (Miyambo 29:22) Koma paja ukudziwa kuti Baibulo limaletsa kupsa mtima. (Salimo 37:8; Aefeso 4:31) Kodi tinganene kuti mfundo imeneyi si yachilungamo chifukwa chakuti anthu ena amachita zinthu zankhanza chifukwa choti anatengera kwa makolo awo?”

“Mulungu angamuuze bwanji munthu yemwe mwachibadwa amafuna kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzake kuti asamachite zimenezi? Si nkhanza zimenezo?”

“Maganizo amenewo amabwera chifukwa anthu amaganiza kuti munthu ayenera kuchita chilichonse chimene thupi lake likufuna pa nkhani ya kugonana. Koma Baibulo limafotokoza kuti anthu ali ndi mwayi wosankha kusachita zinthu zolakwika zimene thupi lawo likufuna.”​—Akolose 3:5.

“Ngakhale kuti iweyo sumachita nawo zimenezo, koma uyenera kusintha mmene umaonera amuna kapena akazi amene amagonana okhaokha.”

“Tiyerekeze kuti ineyo ndimadana ndi zochita juga koma iweyo umaona kuti kuchita juga kulibe vuto. Kodi ingakhale nzeru utandikakamiza kuti ndisinthe maganizo anga pongotengera kuti anthu ambiri amachita juga?”

Kumbukirani kuti nawonso anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo ali ndi mfundo za makhalidwe abwino zimene amatsatira zomwe zimawachititsa kuona kuti zinthu zina ndi zoipa. N’kutheka kuti iwo amaona kuti katangale, kupanda chilungamo, kapena nkhondo ndi zoipa. Baibulo limaletsa zinthu zimenezi komanso limaletsa kugonana kwina, kuphatikizapo kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.​—1 Akorinto 6:9, 10.

Sitinganene kuti Baibulo limangofuna kukhwimitsa zinthu kapena kuti limalimbikitsa tsankho. Limachita zimenezi pofuna kuthandiza anthu omwe amafuna kuti azigonana ndi amuna kapena akazi anzawo kuti azitsatira mfundo yomwe anthu onse amayenera kutsatira, yakuti “thawani dama.”​—1 Akorinto 6:18.

Ndipotu anthu ambiri amene amafuna kutsatira mfundo za m’Bai bulo amayesetsa kudziletsa ngakhale atayesedwa kuti achite dama. Ena mwa anthu amenewa ndi anthu amene sali pabanja ndipo amakayikira zoti adzapeza banja komanso anthu ena ambiri amene mwamuna kapena mkazi wawo ndi wolumala moti sangathe kugonana naye. Komabe anthu amenewa amatha kukhala bwinobwino mosangalala. Anthu amene amafuna atagonana ndi amuna kapena akazi anzawo akhozanso kudziletsa ngati akufunitsitsa kusangalatsa Mulungu.​—Deuteronomo 30:19.

KUTI MUMVE ZAMBIRI PA NKHANI IMENEYI WERENGANI MUTU 28, M’BUKU LACHIWIRI

M’MUTU WOTSATIRA

Atsikana ena amaganiza kuti kugonana ndi chibwenzi chawo kungathandize kuti azikondana kwambiri. Koma zimenezi si zoona. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake tikunena choncho.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Mawu a m’Baibulo akuti “dama” samatanthauza kugonana kokha koma amatanthauzanso kuseweretsa maliseche a munthu wina kapena kugonana m’kamwa kapena kumatako.

LEMBA

“Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.”​—Akolose 3:5.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngakhale kuti nthawi zina zochita za ena zikhoza kukukhumudwitsani, pewani kulankhula mooneka ngati inuyo simumalakwa. Nawonso ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kukhulupirira.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi omwe ankagonana ndi amuna kapena akazi anzawo anasintha khalidwe limeneli ndipo ‘anasambitsidwa kukhala oyera’ m’maso mwa Mulungu.​—1 Akorinto 6:9-11.

ZOTI NDICHITE

Ngati wina atanena kuti zimene Baibulo limafotokoza pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha n’zachikale, ndingamuyankhe kuti: ․․․․․

Pofuna kusonyeza kuti sindimadana ndi anthu amene amachita zimenezi koma khalidwe lawolo, ndinganene kuti: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani timaona kuti Mulungu ali ndi ufulu wopatsa anthu malamulo oti azitsatira?

● Kodi inuyo mumapindula bwanji mukamatsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo?

[Mawu Otsindika patsamba 170]

“Mnyamata wina wa kusukulu kwathu ankandiona ngati munthu woipa kwambiri chifukwa chakuti sindinkagwirizana ndi zochita zake. Koma nditamufotokozera kuti sindinkadana ndi iyeyo kwenikweni koma zochita zake, ndiponso atazindikira kuti sindimangodana ndi zogonana amuna kapena akazi okhaokha koma ndimadananso ndi khalidwe lililonse la chiwerewere, anayamba kundilemekeza ndipo nthawi zina ankandiikira kumbuyo anthu ena akamanditsutsa.”​—Anatero Aubrey

[Bokosi patsamba 168]

Nanga Bwanji za Anthu Amene Amafuna Kumagonana ndi Amuna ndi Akazi Omwe?

Masiku ano pali akazi ambiri amene amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi aliyense, kaya ndi wamwamuna kapena wamkazi. Koma palinso amuna ena omwe amachita zimenezi. Ena amachita zimenezi pongofuna kuona kuti zimakhala bwanji. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 26, dzina lake Lisa, ananena kuti: “Anthu akamaonetsa zinthu zolimbikitsa atsikana kumakisana ndi atsikana anzawo m’mafilimu, pa TV komanso m’nyimbo, achinyamata ambiri amalakalaka atayesa kuti aone kuti zimakhala bwanji, makamaka ngati asakuona kuti kuchita zimenezi n’kulakwa.”

Koma ena zimaoneka kuti amachita zimenezi chifukwa chakuti alidi ndi chilakolako. Mwachitsanzo, Vicky wazaka 13 anati: “Tsiku lina nditapita kuphwando ndinakumana ndi atsikana awiri omwe amagonana ndi aliyense, ngakhale akazi anzawo. Kenako mnzanga anandiuza kuti atsikanawo ankandifuna. Patapita nthawi ndinayamba kutumizirana mameseji ndi mmodzi mwa atsikanawo ndipo nanenso ndinayamba kumufuna.”

Kodi zimene zinam’chitikira Vicky zinakuchitikiranipo? Anthu ena akhoza kukulimbikitsani kuti mungovomereza komanso kubwera poyera kuti muli m’gulu la anthu omwe amagonana ndi aliyense, kaya wamwamuna kapena wamkazi. Komabe muyenera kudziwa kuti kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzanu kumachitika mukafika msinkhu winawake ndipo sikuchedwa kutha. Zimene zinachitika kwa Vicky zinam’pangitsa kutsimikiza mfundo imeneyi. Nayenso Lisette wazaka 16 anaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Iye anati: “Kufotokozera makolo anga mmene ndikumvera kunkandithandiza. Komanso pamene tinkaphunzira Biology kusukulu, anatiuza kuti wachinyamata akafika msinkhu winawake thupi lake limamulamulira mwamphamvu moti nthawi zina amalakalaka zinthu zolakwika. Ndikuona kuti achinyamata atadziwa zimene zimachitika m’thupi mwawo akhoza kuzindikira kuti kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzako kumangochitika kwa nthawi yochepa. Kudziwa zimenezi kungawathandize kuti asamaganize kuti ali m’gulu la anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo.”

Ndipo ngakhale zitakhala kuti chilakolako chimene muli nacho chikuchedwa kutha, dziwani kuti Baibulo likukulimbikitsani kuti musamangochita zimene thupi lanu likufuna, ngakhale zitakhala zolakwika. Zimene Baibulo limanenazi n’zoti mukhoza kukwanitsa.

[Chithunzi patsamba 169]

Akhristu samangotsatira kumene gulu likulowera. Amalimba mtima kutsatira zimene Baibulo likunena ngakhale zitakhala kuti zikusiyana ndi zimene anthu ambiri akufuna