Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kugonana Pongofuna Kuthandizana Kuli Ndi Vuto?

Kodi Kugonana Pongofuna Kuthandizana Kuli Ndi Vuto?

Mutu 26

Kodi Kugonana Pongofuna Kuthandizana Kuli Ndi Vuto?

“Achinyamata amagwirizana zoti azigonana ngakhale asali pa chibwenzi pongofuna kuona kuti angagonane ndi anthu angati.”​—Anatero Penny.

“Anyamata amakambirana momasuka nkhani imeneyi pagulu. Amadzichemerera kuti amagonana ndi atsikana ambirimbiri ngakhale kuti ali ndi chibwenzi.”​—Anatero Edward.

ACHINYAMATA ambiri masiku ano amawawalira anzawo kuti amagonana ngakhale kuti sali pa chibwenzi. Ndipo ena ali ndi azinzawo amene amagonana nawo nthawi ndi nthawi ngakhale kuti sali pa chibwenzi.

Choncho musamadabwe ngati mutayamba kulakalaka kuchita zimenezi kapena ngati winawake atakunyengererani kuti mugone naye ngakhale kuti simuli naye pa chibwenzi. (Yeremiya 17:9) Edward, yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Atsikana ambiri ankandinyengerera kuti ndikagone nawo ndipo kukana zimenezi kunali kovuta kwambiri kuposa zina zonse. Kunena kuti sukufuna si chinthu chophweka.” Koma kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati munthu wina atakunyengererani kuti mugone naye?

Dziwani Chifukwa Chake Kuchita Zimenezi Kuli Kulakwa

Dama ndi tchimo lalikulu moti anthu amene amachita dama “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Ndipotu mfundo imeneyi imagwira ntchito pa aliyense wochita dama, kaya ali pa chibwenzi kapena akungofuna kuthandizana. Choncho, kuti mupewe kugonana ndi munthu, kaya amene muli naye pa chibwenzi kapena wina aliyense, muyenera kuona dama ngati mmene Yehova amalionera.

“Ndimakhulupirira zoti kuti zinthu zikuyendere bwino pa moyo wako uyenera kumachita zinthu motsatira zimene Yehova amafuna.”​—Anatero Karen, wa ku Canada.

“Nthawi zonse muzikumbukira kuti ndinu mwana wa enaake, muli ndi anzanu a ku mpingo komanso anzanu ena ambirimbiri omwe amakukondani. Anthu amenewa akhoza kukhumudwa kwambiri ngati mutakopeka n’kugonana ndi munthu amene akukunyengereraniyo.”​—Anatero Peter, wa ku Britain.

Mukamaona dama ngati mmene Yehova amalionera, mudzatha ‘kudana nacho choipa’ ngakhale thupi lanu litakhala kuti likulakalaka kuchita zoipazo.​—Salimo 97:10.

Mavesi amene mungawerenge: Genesis 39:7-9. Onani mmene Yosefe anasonyezera kulimba mtima pokana atanyengereredwa kuti agonane ndi mkazi wa mbuye wake. Onaninso zimene zinamuthandiza kuchita zimenezi.

Muzinyadira Zimene Mumakhulupirira

Nthawi zambiri zimakhala zophweka kwa achinyamata kuchita zinazake molimba mtima komanso monyadira akakhala kuti zinthuzo amazikhulupirira. Muli ndi mwayi wapadera wochita zinthu zosonyeza kuti mumatsatira mfundo za Mulungu. Choncho musamachite manyazi kufotokozera anzanu mmene mumaonera nkhani yogonana musanalowe m’banja.

“Muziwauziratu anzanu pasadakhale kuti muli ndi mfundo zimene mumatsatira pa nkhani zosiyanasiyana.”​—Anatero Allen, wa ku Germany.

“Anyamata amene ndinaphunzira nawo ankandidziwa bwino moti ankadziwiratu kuti kulimbana ndi kundinyengerera kunali kungotaya nthawi.”​—Anatero Vicky, wa ku United States.

Kuyesetsa kutsatira zimene mumakhulupirira ndi umboni wakuti mukukula mwauzimu.​—1 Akorinto 14:20.

Mavesi amene mungawerenge: Miyambo 27:11. Onani mmene kuchita zinthu zoyenera kungasangalatsire Yehova.

Muzichita Zinthu Motsimikiza

Kunena kuti simukufuna n’kofunika kwambiri koma anthu ena akhoza kuona ngati mukuyankha zimenezi pongofuna kuti winayo aoneke ngati wachita kuvutikira kuti mulole.

“Chilichonse chimene mumachita, kaya ndi mmene mumavalira, mmene mumalankhulira, anthu amene mumalankhula nawo, mmene mumachitira zinthu ndi anthu ena, ziyenera kusonyeza kuti simukufuna kuchita dama.”​—Anatero Joy, wa ku Nigeria.

“Muzichita zinthu zosonyezeratu kuti olo atachita zotani simungalole. Musamalandire mphatso kuchokera kwa anyamata amene akungofuna kupeza njira yokunyengererani. Akhoza kukukakamizani kuti mugone nawo apo ayi mubweze zimene anakupatsanizo.”​—Anatero Lara, wa ku Britain.

Mukamachita zinthu motsimikiza, Yehova adzakuthandizani. Poganizira zimene zinamuchitikira pa moyo wake, Davide ananena kuti: “Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.”​—Salimo 18:25.

Mavesi amene mungawerenge: 2 Mbiri 16:9. Onani kuti Yehova ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu amene akufuna kumachita zinthu zolondola pa moyo wawo.

Muziona Patali

Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mukutsatira mfundo ya pa lembali? Muzichita zinthu zosonyeza kuti mukuona patali.

“Yesetsani kupewa anthu amene amakonda kukamba nkhani zimenezi.”​—Anatero Naomi, wa ku Japan.

“Musamangouza anthu mwachisawawa zinthu ngati kumene mumakhala kapena nambala yanu ya foni.”​—Anatero Diana, wa ku Britain.

Ganizirani mofatsa za zinthu zimene mumalankhula, khalidwe lanu, anzanu komanso malo amene mumakonda kupita. Kenako dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene ndimachitazi sizingapangitse anthu kukhala ndi maganizo oti andinyengerere kuti ndigone nawo?’

Mavesi amene mungawerenge: Genesis 34:1, 2. Onani mmene kupezeka pamalo olakwika kunachititsira mtsikana wina dzina lake Dina kuti akumane ndi mavuto.

Kumbukirani kuti Yehova Mulungu samaona nkhani imeneyi ngati yaing’ono, choncho nanunso musamaone kugonana ngati masewera chabe. Mukamayesetsa kuchita zinthu zoyenera mungakhale ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndiponso mungadzisungire ulemu. Mtsikana wina, dzina lake Carly, ananena kuti: “Musalole kuti wina angokugwiritsani ntchito pa zimene thupi lake likufuna. Muzikumbukira kuti panapita nthawi kuti mukwanitse kukhala ndi makhalidwe oyera pamaso pa Yehova. Choncho, yesetsani kuteteza makhalidwe amenewa.”

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi anyamata amanena kuti amafuna atsikana otani? Mukawerenga nkhaniyi mudabwa kudziwa zimene mnyamata amafuna mwa mtsikana.

LEMBA

“Chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.”​—2 Petulo 3:14.

MFUNDO YOTHANDIZA

Yesetsani kuti mukhale ndi makhalidwe abwino. (1 Petulo 3:3, 4) Mukakhala ndi makhalidwe abwino, zidzakuthandizani kuti munthu winanso wamakhalidwe abwino akopeke nanu.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Yehova amafuna kuti mudzasangalale pogonana ndi mwamuna kapena mkazi wanu mogwirizana ndi mmene iyeyo ankafunira. Kugonana muli m’banja kudzathandiza kuti muzidzasangalala ndiponso kuti musadzavutike ndi nkhawa komanso kunong’oneza bondo, zomwe anthu amene amachita dama amavutika nazo.

ZOTI NDICHITE

Nthawi zonse ndizichita zotsatirazi kuti ndikhale woyera pamaso pa Mulungu ngati mmene analili Yosefe: ․․․․․

Kuti ndisakumane ndi zimene Dina anakumana nazo ndizichita zotsatirazi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Ngakhale kuti mtima ungafune kuti mugonane ndi munthu pongofuna kuthandizana, n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi sikoyenera?

● Kodi mungatani ngati munthu atakuuzani kuti mukagonane?

[Mawu Otsindika patsamba 185]

“Muziyankha ndi mphamvu. Mnyamata wina ataoneka kuti wayamba kuganiza zopusa ndinamuuza kuti, ‘Iwe, chotsa msanga dzanja lakolo paphewa langa!’ Kenako ndinangochokapo nditakwiya.”​—Anatero Ellen

[Chithunzi patsamba 187]

Ngati mungagonane ndi munthu wina mongothandizana ndiye kuti mukudzitchipitsa