Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino—Yakobo

Chitsanzo Chabwino—Yakobo

Chitsanzo Chabwino​—Yakobo

Yakobo ndi mchimwene wake Esau anatenga nthawi yaitali asanalankhulane. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Esau ankadana kwambiri ndi Yakobo. Ngakhale kuti Yakobo sanalakwitse chilichonse, anachita zonse zomwe akanatha kuti akhazikitsenso mtendere ndi m’bale wake. Cholinga chake sichinali kuti awine mkanganowo koma kuti agwirizanenso ndi m’bale wake. Ngakhale kuti sanasinthe mfundo zimene ankatsatira pa moyo wake, sanakakamize m’bale wakeyo kuti apepese kaye kenako agwirizanenso.​Genesis 25:27-34; 27:30-41; 32:3-22; 33:1-9.

Kodi inuyo mumatani mukasemphana maganizo ndi m’bale wanu? Nthawi zina mungaone kuti inuyo simunalakwitse chilichonse koma m’bale wanu kapena makolo anu ndi amene alakwitsa. Kodi zimenezi zikachitika mumayembekezera kuti munthu winayo ndi amene akuyenera kuyambitsa zoti mukambirane? Kapena mungatengere chitsanzo cha Yakobo? Ngati nkhaniyo siikukhudza mfundo za m’Baibulo, kodi mudzachita zonse zomwe mungathe kuti mukhazikitsenso mtendere? (1 Petulo 3:8, 9) Yakobo sanalole kuti kunyada kusokoneze banja lawo. Anachita zinthu modzichepetsa ndipo anayambanso kugwirizana ndi m’bale wake. Kodi nanunso mudzayesetsa kukhazikitsa mtendere ndi abale anu?