Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino—Mose

Chitsanzo Chabwino—Mose

Chitsanzo Chabwino​—Mose

Mose anali ndi mwayi wambiri. Anakulira m’banja lachifumu la Farao ndipo anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo. (Machitidwe 7:22) Kodi anagwiritsa ntchito bwanji zomwe anaphunzirazo? Mose akanatha kukhala wotchuka, wolemera komanso akanatha kukhala ndi udindo waukulu m’boma. Komabe, iye sanakopeke ndi zimene anzake ankachita kapena kufuna kutchuka. M’malomwake anasankha ntchito imene anthu ambiri sankayembekezera. Iye “anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu.” (Aheberi 11:25) Koma kodi kuchita zimenezi inali nzeru? Inde, chifukwa kusankha kwake kutumikira Mulungu ndiponso kuthandiza anthu, kunamuthandiza kuti azikhala wosangalala.

Ngati muli ndi mwayi wophunzira kwambiri, kodi mudzachita chiyani pambuyo pomaliza sukulu? Mukhoza kusankha ntchito yabwino komanso kukhala ndi udindo waukulu. Komanso mofanana ndi Mose, muli ndi mwayi wogwiritsa ntchito moyo wanu pa zinthu zaphindu kwambiri. Mukhoza kugwiritsa ntchito maphunziro anu komanso mphamvu zimene muli nazo potumikira Mulungu ndiponso anthu ena. (Mateyu 22:35-40) Palibe ntchito ina yabwino komanso yaphindu kwambiri kuposa imeneyi.