Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino—Rute

Chitsanzo Chabwino—Rute

Chitsanzo Chabwino​—Rute

Rute ndi chitsanzo chabwino cha munthu wokhulupirika. Anasankha kukhala ndi apongozi ake a Naomi omwe anali achikulire, m’malo mobwerera kumzinda wa kwawo kumene akanatha kukakhala ndi moyo wosangalala. Ngakhale kuti zimene anasankhazi zikanachititsa kuti asapeze mwamuna, Rute sankangoganizira zofuna zake zokha. Chikondi chake pa Naomi ndiponso kufunitsitsa kwake kukhala ndi anthu a Yehova ndi zimene zinali zofunika kwambiri pa moyo wake osati kuti akhalenso pa banja mofulumira.​—Rute 1:8-17.

Kodi inuyo mukuganiza zolowa m’banja? Ngati ndi choncho, tsatirani chitsanzo cha Rute. Musamangoganizira zofuna zanu. Mungachite bwino kuganizira za makhalidwe abwino amene muli nawo amene angadzakhale othandiza kwa munthu amene mudzakwatirane nayeyo. Mwachitsanzo, kodi ndinu munthu wokhulupirika komanso wololera kuvutikira ena? Kodi mumayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu ngakhale pamene thupi lanu likulakalaka kuchita zolakwika? Rute sankachita zinthu zosokonekera pofuna kuti apeze mwamuna. Komabe, m’kupita kwa nthawi anapeza mwamuna wabwino yemwe anali ndi makhalidwe ofanana ndi ake, ndipo khalidwe lofunika kwambiri limene ankafanana linali kukonda Mulungu. Nanunso zinthu zikhoza kukuyenderani choncho.