Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumadziwa Zotani pa Nkhani ya Fodya?

Kodi Mumadziwa Zotani pa Nkhani ya Fodya?

Mutu 33

Kodi Mumadziwa Zotani pa Nkhani ya Fodya?

Onani zimene zalembedwa kumanjaku ndipo ikani chizindikiro ichi ✔ pa mawu amene akufotokoza zimene zimakuchititsani inuyo kufuna kusuta fodya.

□ Ndimafuna kulawa

□ Ndikufuna ndichepetse nkhawa

□ Ndikufuna kuti anzanga asamandisale

□ Ndikufuna ndichepetse thupi

NGATI mwachonga pa bokosi lililonse patsamba 237, ndiye kuti mukufanana ndi achinyamata ena omwe amasuta fodya kapena amafuna atayamba kusuta. * Mwachitsanzo:

Kufuna kulawa. “Ndinkafuna kudziwa kuti fodya amakoma bwanji ndiye tsiku lina mtsikana wina wa kusukulu kwathu atandigayira ndudu imodzi ndinalandira kenako n’kutuluka panja kukasuta.”​—Anatero Tracy.

Kuchepetsa nkhawa komanso kufuna kuti anthu ena asamakusale. “Ana ambiri a kusukulu kwathu ankanena kuti kusuta kumawathandiza kuti asamakhale ndi nkhawa, ndiye nanenso ndikakhala ndi nkhawa ndinkalakalaka kusuta.”​—Anatero Nikki.

Kuchepetsa thupi. “Atsikana ena amasuta kuti asanenepe. Njira imeneyi imaoneka yophweka poyerekeza ndi kuchepetsa zimene umadya.”​—Anatero Samantha.

Koma musanayatse ndudu yanu, kaya mukuyamba kumene kapena mwakhala mukusuta m’mbuyomu, ndi bwino kuganiza kaye mofatsa. Musakhale ngati nsomba imene ikufuna kudya chinthu choti chili kumbedza. N’zoona kuti nsombayo idyadi chinthu chimene ikufunacho koma pamapeto pake ifa. M’malo mochita zimenezi, tsatirani malangizo a m’Baibulo ndipo muzigwiritsa ntchito “mphamvu zanu zotha kuganiza bwino.” (2 Petulo 3:1) Yankhani mafunso otsatirawa.

Kodi Zimene Mumadziwa pa Nkhani ya Fodya N’zolondola?

Chongani ziganizo zili m’munsizi kuti ndi zoona kapena zabodza.

a. Kusuta kukhoza kuchepetsa nkhawa imene ndimakhala nayo.

□ Zoona □ Zabodza

b. Ndikamasuta palibe utsi umene umatsala m’thupi.

□ Zoona □ Zabodza

c. Panopa kusuta sikungasokoneze thanzi langa mpaka nditakalamba.

□ Zoona □ Zabodza

d. Kusuta kungachititse kuti anyamata kapena atsikana azindigomera.

□ Zoona □ Zabodza

e. Mavuto amene angabwere chifukwa chosuta adzakhudza ine ndekha.

□ Zoona □ Zabodza

f. Mulungu alibe nazo ntchito ngati nditayamba kusuta kapena ayi.

□ Zoona □ Zabodza

Mayankho

a. Zabodza. Ngakhale kuti kusuta kumachepetsa pang’ono nkhawa imene munthu amakhala nayo akangosiya kusuta, asayansi apeza kuti kusuta kumawonjezera nkhawa.

b. Zabodza. Kafukufuku amasonyeza kuti zinthu zambiri zimene zimakhala mu utsi wa fodya zimatsalira m’thupi.

c. Zabodza. Ndi zoona kuti mavuto ambiri amawonjezeka ngati munthu wakhala akusuta kwa nthawi yaitali komabe pali mavuto ena amene amayamba kuonekera nthawi yomweyo. Anthu ena akangosuta ndudu imodzi amakomedwa moti safunanso kusiya. Kusuta kumapangitsanso kuti mapapo azikanika kukoka mpweya wokwanira mukamapuma komanso mukhoza kuyamba kudwala chifuwa chosatha. Khungu lanu likhoza kuyamba makwinya zomwe zingachititse kuti mukalambe msanga. Kusuta kukhoza kuchititsa kuti musamathe kugonana, muzikhala ndi mantha komanso kuti muzivutika maganizo.

d. Zabodza. Katswiri wina wofufuza zinthu, dzina lake Lloyd Johnston, anapeza kuti “anyamata ndi atsikana ambiri sakopeka” ndi achinyamata amene amasuta.

e. Zabodza. Chaka chilichonse, anthu ambiri amafa chifukwa cha utsi wochokera kwa munthu yemwe akusuta fodya. Utsiwo ukhoza kupha anthu a m’banja la munthu wosutayo ngakhalenso anzake.

f. Zabodza. Amene amafuna kusangalatsa Mulungu sayenera kuchita “chinthu chilichonse choipitsa thupi.” (2 Akorinto 7:1) Palibe amene angatsutse zoti kusuta kumawononga thupi. Ngati mutasankha kuti muipitse thupi lanu komanso kuvulaza anthu ena chifukwa chosuta fodya, simungakhale bwenzi la Mulungu.​—Mateyu 22:39; Agalatiya 5:19-21.

Zimene Mungayankhe Ngati Wina Atakunyengererani

Ndiye kodi mungatani ngati winawake atakupatsani fodya kuti musute? Kuyankha mwachidule koma motsimikiza kukhoza kuthandiza. Mukhoza kumuyankha kuti “Pepani, sindimasuta.” Ngati munthuyo akukukakamizani kapenanso atayamba kukunenani, kumbukirani kuti kukana kusuta fodya ndi ufulu wanu. Mukhoza kumuuza kuti:

● “Ndimadziwa kuti fodya ndi woipa chifukwa akhoza kuwononga thanzi la munthu ndiye sindimasuta.”

● “Sindikufuna kufa msanga, ndili ndi zambiri zoti ndichite kutsogoloku.”

● “Kodi m’mesa ndili ndi ufulu wosankha zimene ndikufuna?”

Koma mofanana ndi achinyamata amene afotokoza maganizo awo kumayambiriro kwa nkhaniyi, zikhoza kutheka kuti mtima wanu ndi umene ukulakalaka kwambiri kusuta fodya. Ngati zili choncho, kuganizira mafunso otsatirawa kukhoza kukuthandizani kulimbana ndi maganizo amenewa:

● ‘Kodi ndikasuta ndipindula chilichonse? Mwachitsanzo, ngati nditasuta n’cholinga choti anzanga asamandisale, kodi anzangawo angamandikondedi chabe chifukwa chakuti tonse timasuta? Ndipo kodi ndingafune kumagwirizana ndi anthu amene angasangalale kundiona ndikuwononga moyo wanga?’

● ‘Kodi ndingawononge ndalama zambiri bwanji pogula fodya komanso polipirira kuchipatala nditayamba kudwala naye? Komanso kodi ndingalole kuti anthu asiye kundilemekeza chifukwa chakuti ndimasuta?’

● ‘Kodi ndingalole kuwononga ubwenzi wanga ndi Mulungu chifukwa chosuta?’

Koma kodi mungatani ngati munayamba kale kusuta ndipo mukukanika kusiya?

Zimene Zingakuthandizeni Kuti Musiye

1. Tsimikizani. Lembani zifukwa zimene mukusiyira ndipo muziona zimene mwalembazo pafupipafupi. Kukhala ndi cholinga choti Mulungu azikuonani kuti ndinu woyera kungakuthandizeni kwambiri kuti muziyesetsa kupewa kusuta.​—Aroma 12:1; Aefeso 4:17-19.

2. Pemphani thandizo. Ngati mwakhala mukusuta mobisa, panopa ndi nthawi yabwino yoti muwauze ena kuti akuthandizeni. Auzeni anthu amene mwakhala mukuwabisirawo kuti mukufunitsitsa kusiya kusuta ndipo apempheni kuti akuthandizeni. Ngati mukufuna kutumikira Mulungu, m’pempheni kuti akuthandizeni.​—1 Yohane 5:14.

3. Sankhani tsiku limene mukufuna kusiya. Mukamasankha tsiku loti mudzasiye kusuta, ndi bwino kusankha tsiku lakutsogolo kutatsala milungu iwiri kapena kucheperapo kuti lifike. Lembani detilo pakalendala yanu ndipo muuze abale anu komanso anzanu zoti mudzasiya kusuta pa tsiku limenelolo.

4. Fufuzani ndi kutaya zinthu zonse zosafunika. Tsiku limene mwasankha kuti mudzasiye kusuta lisanafike, fufuzani mosamala kuchipinda kwanu, m’galimoto komanso m’zovala zanu ngati muli fodya aliyense wotsala. Mukamupeza m’tayeni ndipo tayaninso malaitala komanso zinthu zonse zimene mumagwiritsa ntchito posuta. Mungachite bwinonso kusiya zoyenda ndi machesi.

5. Pezani njira yothetsera mavuto omwe amabwera mukangosiya kumene. Muzimwa madzi ambiri kapena juwisi komanso muzigona mokwanira. Musamaiwale kuti mavuto amene mungakumane nawo chifukwa chosiya kusuta ndi akanthawi chabe, pamene mapindu amene mungapeze adzakhalapo mpaka kalekale.

6. Muzipewa zinthu zimene zingakupangitseni kufuna kusuta. Muzipewa kukhala pamalo kapena zochitika zimene zingakupangitseni kusuta. Zingakhalenso bwino ngati mutasiya kucheza ndi anthu amene amasuta.​—Miyambo 13:20.

Musapusitsike Ndi Anthu Ena

Chaka chilichonse, makampani ogulitsa fodya amawononga ndalama zambiri poitanira malonda awo. Kodi amafuna kukopa ndani kwenikweni? Kalata ina imene anthu ogwira ntchito pa kampani inayake ya fodya analemberana inali ndi mawu akuti: “Achinyamata a masiku ano akhoza kudzakhala makasitomala abwino a fodya. Choncho tikufunika kuyesetsa kuwakopa kuti ayambe kusuta.”

Musalole kuti ndalama zanu zipite kwa anthu opanga fodya. Musakopeke ndi zochita zawo chifukwa iwowo komanso achinyamata anzanu amene amasuta samaganizira za moyo wanu. Choncho m’malo momvera zonena zawo, mungachite bwino kumvera malangizo a m’Baibulo kuti “zinthu zikuyendereni bwino.”​—Yesaya 48:17.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi anzanu amakunyengererani kuti mumwe mowa? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe kufunika kokhala ndi malire a kuchuluka kwa mowa umene mungamwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ngakhale kuti nkhaniyi ikufotokoza za anthu omwe amasuta, mavuto amene atchulidwa angachitikenso kwa munthu amene fodyayo amachita kutafuna.

LEMBA

“Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.”​—2 Akorinto 7:1.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati mwasiya kusuta, musamaganize kuti kusuta ndudu imodzi yokha si nkhani. Maganizo amenewa angachititse kuti muyambirenso.​—Yeremiya 17:9.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Munthu amene amagwiritsa ntchito fodya mosachita kusuta, mwachitsanzo kuchita kutafuna amakhala ndi poizoni wambiri m’thupi mwake wotchedwa nicotine kuposa munthu amene amachita kusuta. Kugwiritsa ntchito fodya mwa njira ngati imeneyi kukhoza kuchititsanso kuti poizoni woyambitsa khansa amene amapezeka mu fodya alowe m’thupi mwake ndipo akhoza kudwala khansa yapakhosi komanso yam’kamwa.

ZOTI NDICHITE

Ngati mnzanga wakusukulu atandinyengerera kuti ndisute fodya ndidzachita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani n’zotheka munthu kulakalaka kuyamba kusuta ngakhale akudziwa kale mavuto ake?

● N’chiyani chikukupangitsani kuona kuti kusuta n’koopsa?

[Mawu Otsindika patsamba 240]

“Munthu wina akamandipatsa fodya, ndimangomwetulira n’kumuuza kuti, ‘Pepani, sindikufuna kudwala khansa.”​—Anatero Alana

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 241]

Kodi N’zoona Kuti Chamba N’choipa?

Ellen, yemwe amakhala ku Ireland, ananena kuti: “Anthu ena amanena kuti kusuta chamba kumathandiza kuti uiwaleko mavuto ndipo chamba sichiyambitsa mavuto alionse.” Kodi munamva anthu ena akunena zofanana ndi zimenezi? M’munsimu muli zinthu zabodza zimene anthu amanena pa nkhaniyi komanso zoona zake.

Zomwe Ena Amanena. Chamba si choopsa.

Zoona Zake. Zinthu zina zimene munthu wosuta chamba amadzavutika nazo mpaka kalekale ndi izi: Amaiwalaiwala, amavutika kuphunzira zinthu, thupi lake limakanika kulimbana ndi matenda komanso amuna ndi akazi omwe sakhala ndi mphamvu kuchipinda. Chamba chimachititsanso munthu kuvutika ndi nkhawa komanso mutu wake sugwira. Ana amene amabadwa kwa mayi amene amasuta chamba nthawi zambiri amakhala ovutitsa, amavutika kwambiri posankha zinthu komanso sakhala ndi chidwi pophunzira.

Zomwe Ena Amanena. Utsi wa chamba si woopsa ngati utsi wa fodya.

Zoona Zake. Tikayerekeza utsi wa fodya ndi utsi wa chamba, utsi wa chamba umawononga kwambiri m’mene mumadutsa mpweya komanso umakhala ndi poizoni wambiri yemwe amalowa m’magazi. Poizoni amene amapezeka mu ndudu 5 za chamba, ndi wochuluka mofanana ndi poizoni amene angapezeke mupaketi yonse ya fodya wamba.

Zomwe Ena Amanena. Chamba sichivuta kusiya.

Zoona Zake. Nthawi zambiri achinyamata amene amavutika maganizo amati akayamba kusuta chamba zimawavuta kuti asiye. Ena amavutika kusiya ngati akhala akusuta kwa nthawi yaitali. Kafukufuku amasonyezanso kuti achinyamata ambiri amene amasuta chamba, m’kupita kwa nthawi amayambanso kugwiritsa ntchito mankhwala ena osokoneza bongo, ngati cocaine, omwe amavuta kusiya.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 244, 245]

Thupi la Munthu Wosuta Fodya

Yerekezerani zithunzi za anthu a thanzi omwe amasonyezedwa potsatsa malonda a fodya ndi zithunzi zomwe zikusonyeza zimene zimachitikadi m’thupi la munthu wosuta fodya.

M’kamwa ndi pakhosi Umatha kudwala khansa

[Chithunzi]

Khansa ya palilime

Mtima Mitsempha yodutsa magazi imayamba kulimba komanso kutsekeka, zomwe zimachititsa kuti mumtima musamafike mpweya wokwanira ndipo munthuyo akhoza kudwala matenda a mtima mosavuta

[Chithunzi]

Mtsempha woti wayamba kutsekeka

Mapapo Fodya amawononga malo osungira mpweya m’mapapo, amatupitsa njira zimene mpweya umadutsa komanso n’zosavuta kuti munthuyo adwale khansa ya m’mapapo

[Chithunzi]

Mapapo a munthu wosuta fodya

Ubongo N’zosavuta kuti munthu wosuta fodya adwale matenda opha ziwalo

Khungu Munthu amakalamba msanga

Mano amasintha mtundu

M’mimba Fodya amayambitsa khansa

Kapamba Fodya amayambitsa khansa

Chikhodzodzo Fodya amayambitsa khansa

Impso Fodya amayambitsa khansa

[Chithunzi patsamba 239]

Mofanana ndi nsomba imene imadya chinthu choti chili kumbedza, munthu amene amasuta amamva bwino kwa kanthawi koma pamapeto pake amakumana ndi mavuto oopsa