Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kumwa Mowa Wambiri Kuli Ndi Vuto Lanji?

Kodi Kumwa Mowa Wambiri Kuli Ndi Vuto Lanji?

Mutu 34

Kodi Kumwa Mowa Wambiri Kuli Ndi Vuto Lanji?

Kodi mungayankhe bwanji mafunso otsatirawa? Ikani chizindikiro ichi ✔ pamene pali yankho logwirizana ndi lanu.

Kodi anzanu amamwa mowa kwambiri kapena amamwa mowa ngakhale kuti sanafike pa msinkhu woyenerera?

□ Inde □ Ayi

Kodi anzanu anayamba akunyengereranipo kuti mumwe mowa?

□ Inde □ Ayi

Kodi munayamba mwamwapo mowa wambiri?

□ Inde □ Ayi

KODI tingasiyanitse bwanji kumwa mowa ndi kumwa mowa wambiri? Anthu ena amanena kuti kumwa mowa wambiri ndi kumwa n’cholinga choti uledzere. Lipoti la bungwe lina la ku United States, linachita kutchula nambala ya mabotolo omwe munthu atamwa tinganene kuti wamwa mowa wambiri. (U.S. National Institute on Alcohol Abuse and Alcoholism) Linanena kuti “ngati mwamuna wamwa molumikiza mabotolo 5 kapena kuposa komanso ngati mkazi wamwa mabotolo 4 kapena kuposa,” ndiye kuti wamwa mowa wambiri.

Ngati munayamba mwamwapo mowa wambiri kapena kumwa mowa musanafike msinkhu wovomerezeka ndi boma, dziwani kuti simuli nokha. Achinyamata ambiri amamwa mowa mopitirira muyezo. * Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikudziwa chimene chikundichititsa kuti ndiyambe mowa? Nanga ndikudziwa mavuto amene ndingakumane nawo ngati nditayamba mowa?’ Mwachitsanzo, kodi mungayankhe bwanji mafunso otsatirawa? Ikani chizindikiro ichi ✔ pamene pali yankho logwirizana ndi lanu, kenako ganizirani mayankho olondola omwe ali m’munsi mwakemo.

a. Achinyamata amamwa chifukwa chakuti umawakomera.

□ Zoona □ Zabodza

b. Chifukwa chakuti achinyamata amakhala ndi mphamvu komanso thanzi labwino, sangakumane ndi mavuto ena amene anthu akuluakulu amakumana nawo chifukwa chomwa mowa wambiri.

□ Zoona □ Zabodza

c. Munthu sungafe chifukwa chomwa mowa wambiri.

□ Zoona □ Zabodza

d. Baibulo limaletsa kumwa mowa.

□ Zoona □ Zabodza

e. Vuto lokha limene ungakumane nalo ngati umamwa mowa wambiri ndi kudwaladwala basi.

□ Zoona □ Zabodza

a. Achinyamata amamwa chifukwa chakuti umawakomera. Yankho​—Zabodza. Pa kafukufuku amene anachitika ku Australia, anapeza kuti achinyamata 36 pa 100 alionse amene anafunsidwa, amamwa mowa n’cholinga choti asamaoneke otsalira pa nthawi ya zisangalalo. Pa kafukufuku wina amene anachitika ku United States anapeza kuti achinyamata 66 pa 100 alionse amamwa pongotengera anzawo. Komabe, achinyamata ambiri ananenanso kuti amamwa n’cholinga choti aiwale mavuto.

b. Chifukwa chakuti achinyamata amakhala ndi mphamvu komanso thanzi labwino, sangakumane ndi mavuto ena amene anthu akuluakulu amakumana nawo chifukwa chomwa mowa wambiri. Yankho​—Zabodza. Magazini ina inanena kuti: “Kafukufuku amene wachitika posachedwapa akusonyeza kuti achinyamata amene amamwa mowa akuputa dala mavuto.” Kodi ananena zimenezi chifukwa chiyani? Chifukwa “achinyamata amene amamwa mowa kwambiri ubongo wawo sumagwira ntchito bwino.”​—Discover.

Kumwa mowa kwa nthawi yaitali kumayambitsanso ziphuphu, kukalamba uli mwana, kunenepa kwambiri, kulephera kuchita zinthu ngati sunamwe mowa komanso kuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Kukhozanso kuwononga mitsempha, chiwindi ndiponso mtima.

c. Munthu sungafe chifukwa chomwa mowa wambiri. Yankho​—Zabodza. Kumwa mowa kwambiri kumachititsa kuti muubongo musamafike mpweya wokwanira, zomwe zingachititse kuti ziwalo zina zisiye kugwira ntchito. Zizindikiro zake ndi kusanza, kukomoka ndiponso kuvutika kupuma. Nthawi zina munthu akhoza kufa.

d. Baibulo limaletsa kumwa mowa. Yankho​—Zabodza. Baibulo silimaletsa kumwa mowa komanso silimaletsa achinyamata kusangalala. (Salimo 104:15; Mlaliki 10:19) Komabe, ngati mukufuna kumwa mowa muyenera kudikira mpaka mutafika msinkhu wovomerezeka ndi boma.​—Aroma 13:1.

Koma Baibulo limaletsa kumwa mowa kwambiri. Lemba la Miyambo 20:1 limati: “Vinyo ndi wonyoza. Chakumwa choledzeretsa chimasokosera ndipo aliyense wosochera nacho alibe nzeru.” Mowa ukhoza kukupangitsani kuti muzichita zinthu zopanda nzeru. N’zoona kuti mukamayamba kumene kumwa mowa mumamva bwino, koma mukamwa wambiri ‘umaluma ngati njoka’ ndipo umakusiyirani mavuto ambiri.​—Miyambo 23:32.

e. Vuto lokha limene ungakumane nalo ngati umamwa mowa wambiri ndi kudwadwala basi. Yankho​—Zabodza. Munthu ukaledzera n’zosavuta kuti anthu akuchite chipongwe, ngakhale kukugwiririra kumene. Komanso, mukhoza kuchita zinthu zosokoneza zomwe zikhoza kupweteketsa ena ndipo zimakhala zoti simungachite mutakhala kuti muli bwinobwino. Baibulo limachenjezanso kuti kumwa mowa kwambiri kumachititsanso ‘maso kuona zinthu zachilendo, ndipo mtima umalankhula zinthu zokhota.’ (Miyambo 23:33) Mwachidule tingati mungachite zinthu zodzichotsera ulemu. Mavuto ena angaphatikizepo kudana ndi anzanu, kulephera sukulu, kukanika kugwira bwino ntchito, kupalamula milandu yomwe ingakuipitsireni mbiri mpaka kalekale komanso kusauka.​—Miyambo 23:21.

Koma kwenikweni ganizirani mmene kumwa mowa kwambiri kungasokonezere ubwenzi wanu ndi Yehova. Yehova Mulungu amafuna kuti muzimutumikira ndi ‘maganizo anu onse,’ osati kumutumikira maganizo anu atasokonezeka chifukwa chomwa mowa kwambiri. (Mateyu 22:37) Sikuti Mawu a Mulungu amangoletsa “kumwa vinyo mopitirira muyezo” kokha, amaletsanso “kumwa kwa mpikisano.” (1 Petulo 4:3) Choncho, kumwa mowa wambiri n’kosemphana ndi zimene Mlengi wathu amafuna komanso kungapangitse kuti musakhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

Kodi Inuyo Musankha Chiyani?

Kodi inuyo mutengera zochita za anzanu omwe amamwa kwambiri mowa? Baibulo limati: “Kodi simukudziwa kuti ngati mudziperekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvera, mumakhala akapolo ake chifukwa chakuti mumamumvera?” (Aroma 6:16) Kodi mukufuna kukhala kapolo, kaya wa anzanu kapena wa mowa?

Koma bwanji ngati muli kale ndi chizolowezi chomwa mowa wambiri? Uzani makolo anu mwamsanga kapena mnzanu wachikulire kuti akuthandizeni. Pempherani kwa Yehova Mulungu ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni. Ndipotu iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.” (Salimo 46:1) Popeza achinyamata ambiri amayamba kumwa kwambiri mowa chifukwa cha anzawo, mungachite bwino kusintha anthu amene mumacheza nawo. * Kusintha anthu ocheza nawo sikophweka koma Yehova akhoza kukuthandizani.

M’MUTU WOTSATIRA

N’zotheka kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe zingakuthandizeni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Onani bokosi lakuti,  “Ndani Akuchita Zimenezi?” patsamba 249.

^ ndime 32 Kuti mumve zambiri, werengani Mutu 8 ndi 9 m’bukuli komanso Mutu 15, m’Buku Lachiwiri.

LEMBA

‘Chidakwa . . . chidzasauka.’​—Miyambo 23:21.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ganizirani zifukwa zomwe zikukuchititsani kufuna kumwa mowa. Kenako ganizirani za zinthu zina zabwino zimene mungachite kuti musangalale.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kafukufuku wina amene anachitika ku United States anapeza kuti, “mosiyana ndi achinyamata omwe samwa kwambiri mowa, achinyamata omwe amamwa kwambiri mowa sakonda kulowa m’kalasi, amachedwa kumaliza homuweki, amavulala komanso amawononga katundu.”

ZOTI NDICHITE

Ngati anzanga akufuna kuti timwe mowa mopitirira muyezo, ndingawauze kuti ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani anzanu amafuna kuti anthu ena azimwa nawo mowa mopitirira malire?

● Kodi kumwa mowa kwambiri kungapangitse kuti anyamata kapena atsikana azikuonani kukongola? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

[Mawu Otsindika patsamba 250]

“Anzanga akusukulu akamandipatsa mowa, ndimawauza kuti ndimatha kukhala wosangalala popanda mowa.”​—Anatero Mark

[Bokosi patsamba 249]

 Ndani Akuchita Zimenezi?

Mwana mmodzi pa 4 alionse akusekondale azaka 13 kapena 14, omwe anafunsidwa pa kafukufuku wina yemwe anachitika ku England, Scotland, ndi Wales, “ananena kuti anamwapo mabotolo a mowa oposa 5 nthawi imodzi.” Ndipo hafu ya achinyamata onse azaka 15 ndi 16 omwe anafunsidwa, ananena kuti nawonso anamwapo mowa wambiri chonchi. Dipatimenti ya zaumoyo wa anthu ya ku United States inafotokoza kuti, “achinyamata pafupifupi 10.4 miliyoni azaka zoyambira 12 mpaka 20 ananena kuti amamwa mowa. Pa gulu limeneli, achinyamata 5.1 miliyoni amamwa mowa wambiri ndipo 2.3 miliyoni ndi zidakwa chifukwa pa mwezi umodzi amapezeka kuti amwa mowa wambiri maulendo oposa 5.” Kafukufuku wina amene anachitika ku Australia anasonyeza kuti kawirikawiri atsikana ndi amene amamwa mowa wambiri kuposa anyamata chifukwa amamwa mabotolo 13 mpaka 30 nthawi imodzi.

[Chithunzi patsamba 251]

Mowa umatha kuluma ngati njoka