Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?

Mutu 35

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?

KODI mumagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo mukulephera kusiya? N’kutheka kuti mumadziwa zoti mankhwala mukugwiritsa ntchitowo akuwononga thupi lanu komanso maganizo anu. Mwinanso munayesapo kusiya koma kenako munayambiranso. Ngati ndi choncho, musataye mtima. Anthu ena anakwanitsa kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo nanunso mukhoza kukwanitsa. Onani zitsanzo za anthu atatu omwe anakulira m’malo osiyana kwambiri koma anakwanitsa kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

DZINA Marta

MBIRI YANGA Ndinabadwa mayi anga asali pabanja moti ineyo ndi mchemwali wanga tinakula opanda bambo. Nditangokwanitsa zaka 12 ndinayamba kupita ku madansi ndi amayi anga aang’ono omwe ankakonda kuvina. Ndinkakonda zonjoya ndipo ndinayamba kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa. Ndili ndi zaka 13, ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuphatikizapo cocaine. Poyamba, ndinkasangalala ndikamagwiritsa ntchito mankhwalawa koma kenako ndinayamba kumaona zilubwelubwe komanso kuchita mantha ndi zinthu zachabechabe. Mphamvu ya mankhwalawa ikayamba kukungunuka ndinkakhala ndi maganizo ofuna kudzipha. Ndinkafuna kusiya kugwiritsa ntchito mankhwalawa koma ndinkasowa poyambira.

MMENE NDINASIYIRA Ndinayamba kuganizira za Mulungu moti ndinapita kutchalitchi maulendo angapo. Koma ndinkangokhalabe wokhumudwa. Nditakwanitsa zaka 18, ndinapita kukakhala kwa chibwenzi changa ndipo ndinakhala ndi mwana wamwamuna. Kubereka mwanaku kunawonjezera chidwi changa chofuna kusintha khalidwe langa. Munthu wina amene ndinkacheza naye kalekale anasamukira m’nyumba ina pafupi ndi nyumba yathu. Tsiku lina anabwera kudzandichezera ndipo anandifunsa kuti zinthu zikundiyendera bwanji. Atandifunsa zimenezi ndinamuuza zonse zimene zinali kukhosi kwanga. Anandiuza kuti tsopano ndi wa Mboni za Yehova ndipo atandipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo, ndinavomera.

Ndinaphunzira kuti Mulungu amadana ndi zimene ndinkachita pa moyo wanga ndiponso kuti ndiyenera kusiya kusuta komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma ndinali nditazolowera kwambiri kugwiritsa ntchito mankhwalawa moti zinali zovuta kwambiri kuti ndisiye. Tsiku lililonse ndinkapemphera kwa Yehova Mulungu maulendo angapo kuti andithandize kusintha khalidwe langa. Ndinkafunitsitsa kuchita zinthu zimene amasangalala nazo. (Miyambo 27:11) Ndinakwanitsa kusiya pambuyo pophunzira Baibulo ndiponso kusonkhana ndi Mboni za Yehova kwa miyezi 6. Panopa ndimasangalala kwambiri ndi moyo wanga. Zomangokhalira kuvutika maganizo zija zinatha. Ndinakumana ndi mwamuna wina wachikhristu komanso wakhalidwe labwino ndipo tinakwatirana. Ndakhala ndikuphunzitsa mwana wanga mfundo za m’Baibulo ndipo ndimayamikira kwambiri Yehova chifukwa choyankha pemphero langa ndiponso kundithandiza.

DZINA Marcio

MBIRI YANGA Ndinakulira mumzinda wa anthu ambiri wotchedwa Santo André, ku São Paulo, m’dziko la Brazil. Ndinayamba kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuba ndili wamng’ono. Anzanga ambiri ankaba magalimoto komanso kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo. Ndipo mnzanga wina ankapereka mankhwalawa kwaulere kwa achinyamata a m’dera lathu. Koma achinyamatawo akafika pozolowera kugwiritsa ntchito mankhwalawa ankachita kuwagulitsa.

Nthawi zonse apolisi ankalondera dera lathu ndipo ndinamangidwapo maulendo angapo pa milandu yachabechabe. Nthawi ina anandimanga chifukwa chondiganizira kuti ndinkazembetsa mankhwala osokoneza bongo. Maulendo angapo ndinkasunga m’nyumba mwathu mfuti komanso katundu wobedwa.

Anthu ankandiopa kwambiri. Maso anga ankangokhala ofiira komanso sindinkamwetulira. Ndipotu nkhope yanga inkangooneka yoopsa nthawi zonse. Anthu anandipatsa dzina losonyeza kuti ndinali munthu wosokoneza kwambiri. Ndinkamwanso kwambiri mowa komanso ndinali wam’chiuno. Anzanga ambiri anamwalira ndipo ena anamangidwa. Tsiku lina ndinakhumudwa kwambiri moti ndinamangirira chingwe kunthambi ya mtengo kuti ndidziphe.

MMENE NDINASIYIRA KUGWIRITSA NTCHITO MANKHWALAWA Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize ndipo m’kupita kwa nthawi ndinakumana ndi a Mboni za Yehova omwe anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Ndinaphunzira kuti Mulungu ali ndi dzina, lomwe ndi Yehova, komanso kuti amadera nkhawa ndiponso kuthandiza anthu amene amayesetsa kutsatira mfundo zake. (Salimo 83:18; 1 Petulo 5:6, 7) Panali zinthu zambiri zimene ndinkafunika kusintha koma chinthu chovuta kwambiri chinali kuphunzira kumwetulira.

Nthawi ndi nthawi ndinkam’pempha Yehova kuti andithandize ndipo ndinkayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, ndinasiya kucheza ndi anzanga akale komanso kupita ku mabala. M’malo mwake ndinayamba kucheza kwambiri ndi anthu omwe amatsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo. Sizinali zophweka kuti ndisinthe koma panopa ndine wosangalala chifukwa ndinasiya kuba komanso kusowetsa anthu mtendere. Ndipo panopa padutsa zaka zoposa 10 nditasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

DZINA Craig

MBIRI YANGA Ndinakulira ku famu ina ya ku South Australia. Bambo anga anali chidakwa ndipo anasiyana ndi mayi ndili ndi zaka 8 zokha. Mayi anga anakwatiwanso ndipo ndinkakhala nawo limodzi mpaka pamene ndinakwanitsa zaka 17. Chaka chimenecho ndinaphunzira kumeta nkhosa ndipo ndinayamba kukhala ndi magulu a anthu ometa nkhosa omwe ankayenda m’madera osiyanasiyana pofufuza ntchito. Ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo a mitundu yosiyanasiyana komanso kumwa mowa kwambiri. Ndinasiya kumeta tsitsi kenako ndinayamba kulithira mankhwala, kulimanga komanso kuikako mikanda. Ndinkachitira anthu nsanje, ndinali wankhanza komanso sindinkachedwa kupsa mtima moti ndinamangidwapo maulendo angapo.

Ndinasamukira ku tauni ina yaing’ono ya ku Western Australia ndipo ndinkakhala ndi chibwenzi changa chomwe chinkagulitsa mowa ku hotelo ya m’deralo. Tonse tinkasuta fodya komanso kumwa mowa ndipo tinkalima tokha chamba.

MMENE NDINASIYIRA KUGWIRITSA NTCHITO MANKHWALAWA Tsiku lina titangomaliza kukolola chamba a Mboni za Yehova anagogoda pachitseko cha nyumba yathu. Poyamba sindinakhulupirire zimene anafotokoza. Koma m’kupita kwa nthawi ndinayamba kuona kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona. Kenako pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kulimbana ndi mavuto anga.

Pasanapite nthawi ndinadziwa kuti ndiyenera kusiya kusuta chamba. Koma kuchita zimenezi sikunali kophweka chifukwa tinali titavutikira kusamalira chamba chathu kuti chikule bwino, moti poyamba tinkaganiza zongochipereka kwa ena. Koma tinaona kuti imeneyi si njira yabwino ndiye tinangochiwononga. Pemphero ndi limene linandithandiza kwambiri kuti ndisiye kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa kwambiri. Ndinapempha Mulungu kuti andipatse mzimu wake kuti undithandize kulimbana ndi zopinga zimene zinalipo. Ndinasiyanso kucheza ndi anthu amene ankandilimbikitsa kuchita makhalidwe oipa. Kuphunzira komanso kuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo kunandithandiza kuti ndisavutike kwambiri polimbana ndi makhalidwe olakwika amene ndinali nawo. Nachonso chibwenzi changa chinayamba kuphunzira Baibulo ndipo anasintha khalidwe lake. Kenako tinakwatirana ndipo takhala ndi thanzi labwino kwa zaka 21 tsopano. Panopa ndife osangalala kulera ana athu awiri. Sindikudziwa kuti moyo wanga ukanakhala wotani zikanakhala kuti Yehova sanandithandize kusintha khalidwe langa.

LEMBA

“Yehova ndiye mphamvu zanga ndi nyonga zanga.”​—Yesaya 12:2.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati n’zotheka muzipewa anthu amene amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso muzipewa malo ndiponso zinthu zimene zingakukumbutseni moyo wanu wakale. Kafukufuku amasonyeza kuti kuona zinthu ngati zimenezi kukhoza kuyambitsanso chibaba.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kukhoza kuwononga ubongo wanu moti sungagwirenso ntchito bwinobwino.

ZOTI NDICHITE

Ngati nditayambiranso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndidzachita zotsatirazi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Ngati munthu akufuna kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, n’chifukwa chiyani ndi bwino kusintha kwambiri zinthu zimene amachita pa moyo wake?

● Kodi kudziwa choonadi chonena za Mulungu n’kothandiza bwanji?

[Mawu Otsindika patsamba 253]

“Panopa ndine wosangalala kwambiri chifukwa choyesetsa kutsatira mfundo zapamwamba za m’Baibulo.”​—Anatero Marta

[Chithunzi patsamba 256]

Kusiya chizolowezi choipa kuli ngati kuthawa m’nyumba yoti ikuyaka. Umasiya zinthu m’mbuyo, komabe umakhala kuti wapulumutsa moyo wako