Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kuti Ndizisangalalako Nthawi Zina?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kuti Ndizisangalalako Nthawi Zina?

Mutu 37

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kuti Ndizisangalalako Nthawi Zina?

Lolemba lililonse likamafika, mtsikana wina wa ku Australia, dzina lake Allison, amachita kudziwiratu kuti zimene anzake azikanena akapita kusukulu akakhumudwa nazo.

Iye ananena kuti: “Aliyense amafotokoza zimene wakhala akuchita Loweruka ndi Lamlungu. Ndimasirira akamafotokoza zinthu ngati kuchuluka kwa mapate amene anapita, kuchuluka kwa anyamata amene akisana nawo komanso mmene amathamangitsirana ndi apolisi pamsewu . . . Zimaoneka zoopsa komanso zosangalatsa. Amatha kufika pakhomo cha m’ma 5 m’mawa ndipo makolo awo samawafunsa chilichonse, pamene ine ndimafunika kugona mwinanso anzangawo asananyamuke n’komwe kupita konjoyako.

“Kenako akamaliza kufotokoza zimene amachitazo amandifunsa zimene nanenso ndimachita. . . . Ineyo ndimakhala kuti ndinangopita kumisonkhano ya mpingo komanso kugwira ntchito yolalikira. Ndimaona kuti sindinachite chilichonse chonjoya ndiye nthawi zambiri ndimangowauza kuti palibe chimene ndinachita. Ndikayankha zimenezi amandifunsa kuti n’chifukwa chiyani sindinapite nawo kumene anapita iwowoko.

“Munthu angaganize kuti zinthu zikhalako bwino Lolemba likadutsa, koma ayi. Likamafika Lachiwiri aliyense amakhala atayamba kufotokoza zimene akufuna kudzachita kumapeto kwa mlungu umenewowo. Nthawi zambiri ndimangokhala phee n’kumawamvetsera. Ndimadzimva kuti ndikutsalira.”

KODI nanunso mumakumana ndi zinthu ngati zimenezi Lolemba lililonse mukapita kusukulu? Mwina mungamaganize kuti anzanu onse amanjoya pamene inuyo makolo anu amakuletsani. Sikuti mumafuna kuchita zonse zimene anzanuwo amachita koma mwina mumangofuna kusangalalako nthawi zina. Mwachitsanzo, ikani chizindikiro pa zosangalatsa zimene inuyo mungakonde kuchita kumapeto kwa mlungu uno.

□ kupita kokavina

□ kupita kokaonera mpira

□ kupita kupate

□ kukaonera filimu

□ zina ․․․․․

N’zoona kuti mumafunika kusangalala, ndipotu Mlengi wanu amafuna kuti muzisangalala ndi chinyamata chanu. (Mlaliki 3:1, 4) Ngakhale kuti nthawi zina n’zovuta kuzikhulupirira, nawonso makolo anu amafuna kuti muzisangalala. Komabe makolo anu angafune kudziwa zinthu ziwiri: (1) kodi mukukachita chiyani komanso (2) mukupita ndi ndani?

Kodi mungatani ngati anzanu atakuitanirani kwinakwake koma inuyo simukudziwa kuti makolo anu ati chiyani mukawapempha? Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene mungasankhe komanso zotsatira zake.

NJIRA 1 KUNGONYAMUKA OSAWAPEMPHA

N’chifukwa chiyani mungaganize zotsatira njira imeneyi? Mwina mungafune kuti anzanuwo aziona kuti muli ndi ufulu wochita zimene mukufuna. Mungasonyezenso kuti inuyo mumadziwa zambiri kuposa makolo anu kapena kuti simulemekeza maganizo awo.​—Miyambo 14:18.

Zotsatira zake: N’zoona kuti anzanuwo angamakugomereni koma adzadziwanso kuti ndinu wachinyengo. Ngati mungachite zinthu zachinyengo kwa makolo anu, mukhoza kuchitanso zachinyengo kwa anzanuwo. Ngati makolo anu atakutulukirani akhoza kukhumudwa ndipo sangamakuloleninso kuyenda ngakhale pang’ono. Choncho, si nzeru kupita kokasangalala osauza makolo anu.​—Miyambo 12:15.

NJIRA 2 OSAWAUZA KOMANSO OSAPITA

N’chifukwa chiyani mungaganize zotsatira njira imeneyi? N’kutheka kuti mwaona kuti zimene anzanuwo akufuna kukachita sizikugwirizana ndi mfundo zimene mumatsatira kapena mwaona kuti anthu ena amene aitanidwa si akhalidwe labwino. (1 Akorinto 15:33; Afilipi 4:8) Komanso n’kutheka kuti mukufuna kupita koma mukuopa kuwauza makolo anu.

Zotsatira zake: Ngati mwasankha kusapita chifukwa chakuti mukuona kuti si nzeru kupitako, sizingakuvuteni kuwayankha anzanuwo. Koma ngati mwasankha kusapita chifukwa choopa kupempha makolo anu, mukhoza kumangonyinyirika n’kumaona ngati mukumanidwa zinazake.

NJIRA 3 APEMPHENI KUTI MUMVE ZIMENE ANENE

N’chifukwa chiyani mungaganize zotsatira njira imeneyi? Mungawapemphe chifukwa mukudziwa kuti ali ndi udindo wokuyang’anirani ndiponso mumalemekeza maganizo awo. (Akolose 3:20) Komanso chifukwa chakuti mumawakonda ndipo simukufuna kuwakhumudwitsa pochita zinthu zachinyengo. (Miyambo 10:1) Mungakhalenso ndi mwayi wowafotokozera maganizo anu.

Zotsatira zake: Makolo anu angaone kuti mumawakonda komanso mumawalemekeza. Ndipo ngati ataona kuti palibe vuto akhoza kukulolani.

Zimene Zingachititse Kuti Akukanizeni

Koma bwanji ngati makolo anu atakukanizani? Mukhoza kukhumudwa kwambiri. Komabe kudziwa zifukwa zimene akukanizirani kungakuthandizeni kuti musakhumudwe kwambiri. Mwachitsanzo, mwina makolo anu akhoza kukukanizani pa zifukwa zotsatirazi:

Amadziwa zinthu zambiri. Ngati mutakhala ndi mwayi wosambira m’nyanja, mwina mungasankhe kusambira pamalo amene mukudziwa kuti pali anthu amene akhoza kukupulumutsani ngati mutayamba kumira. Tikutero chifukwa munthu akamasambira amakomedwa ndi kusambirako moti sangaone bwinobwino zinthu zimene zingaike moyo wake pangozi. Koma anthu opulumutsawo amakhala poti amaona zinthu zoopsa ngakhale zili kutali ndipo atha kukuchenjezani.

N’chimodzimodzinso ndi makolo anu. Iwo amadziwa zambiri komanso aona zinthu zambiri pa moyo wawo moti amadziwa zinthu zoopsa zimene inuyo simungazidziwe. Mofanana ndi cholinga cha opulumutsa aja, cholinga cha makolo anu sikukukhomererani kuti musamasangalale koma kukuthandizani kuti musakumane ndi mavuto.

Amakukondani. Makolo anu amafunitsitsa kukutetezani. Chifukwa chakuti amakukondani akhoza kukulolani kuti mupite kokasangalala. Koma ngati akuona kuti mukhoza kukumana ndi mavuto sangakuloleni. Mukawapempha kuti mukufuna kupita kwinakwake, amayamba aganizira kaye za mavuto amene mungakumane nawo ngati atakulolezani. Nthawi zambiri akhoza kukulolezani ngati atatsimikiza kuti simukakumana ndi vuto lililonse.

Zimene Mungachite Kuti Azikulolani Kukasangalala

Muyenera kutsatira mfundo 4 zotsatirazi.

Muzinena zoona: Choyamba, muzidzifunsa moona mtima kuti: ‘Kodi ndikufuna kupita kumeneko chifukwa chiyani? Kodi ndikungofuna kupitako chifukwa chakuti ndikufuna kusangalatsa anzanga kapena ndimasangalala ndi zimene zikukachitikazo? Kapena ndikungofuna kupitako chifukwa chakuti mnyamata kapena mtsikana amene ndimamufuna akakhalako?’ Mukapeza mayankho a mafunso amenewa, mungachite bwino kuuza makolo anuwo zoona zenizeni zimene mukufunira kupita kumeneko. Nawonso makolo anuwo anakhalapo achinyamata komanso akukudziwani bwino moti akhoza kukutulukirani ngakhale mutawanamiza. Kunena zoona kungachititse kuti makolo anu azikukondani ndipo akhoza kukupatsani malangizo othandiza kwambiri. (Miyambo 7:1, 2) Koma ngati simunena zoona, makolo anu sangamakukhulupirireni ndipo nthawi zambiri sangamakuloleni kupita kokasangalala.

Muzipempha pa nthawi yoyenera: Si bwino kupempha makolo anu kuti mukufuna kuchokapo akangofika kumene kuchokera kuntchito kapena pa nthawi imene atanganidwa ndi zinazake. Apempheni pa nthawi imene akuoneka kuti ali ndi mpata wabwino. Koma musadikirirenso mpaka nthawi itakutherani moti muziwavutitsa kuti akuyankheni mwamsanga. Makolo sasangalala mukawapanikiza kuti achite zinthu mwaphuma. Muzipempha kukadali nthawi yambiri kuti iwonso akhale ndi nthawi yoiganizira nkhaniyo bwinobwino. Mukamachita zimenezi adzaona kuti mumawaganizira.

Muzifotokoza momveka bwino: Mukamapempha makolo anu musamabise zinthu zina zomwe ayenera kudziwa. Muzifotokoza momveka bwino zimene mukufuna kukachita. Nthawi zambiri makolo safuna kumva yankho lakuti “Sindikudziwa,” makamaka akakufunsani kuti: “Kukakhala ndani?” “Kukakhala munthu wamkulu amene azikakuyang’anirani?” kapena akakufunsani kuti “Zochitikazo zikatha nthawi yanji?”

Musamawakayikire: Musamaone makolo anu ngati adani anu koma muziwaona kuti ndi anzanu omwe mukhoza kuchitira nawo zinthu limodzi ndipo ndi mmenedi ziyenera kukhalira. Ngati mumaona makolo anu ngati anzanu simungamatsutsane nawo ndipo mudzayamba kuchita zinthu mogwirizana. Muzipewa kunena mawu ngati akuti “Simundikhulupirira,” “Anzanga onsetu akupita,” kapena “Anzanga onse makolo awo awalola kuti akhoza kupita.” Asonyezeni makolo anu kuti ndinu woganiza bwino ndipo mumalemekeza zosankha zawo. Mukamachita zimenezi, nawonso adzayamba kukulemekezani ndipo ulendo wotsatira angayesetse kuona ngati zili zotheka kukulolani kupita kokasangalala.

KUTI MUMVE ZAMBIRI PA NKHANIYI WERENGANI MUTU 32, M’BUKU LACHIWIRI

LEMBA

“Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.”​—Miyambo 27:11.

MFUNDO YOTHANDIZA

Mukapita kwinakwake kokasangalala muzikhala ndi pulani yochokera ngati zinthu zitayamba kusokonekera. Musanapite muzidziwiratu zimene mungachite kapena kunena kuti muchoke kumaloko muli ndi chikumbumtima choyera.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Makolo achikondi amasankha zinthu zimene akuona kuti sizingaike pangozi moyo wa ana awo. Choncho ngati sakumvetsa zimene inuyo mukufuna kapena ngati akuona kuti popempha mwabisa mfundo zina zofunika, akhoza kukukanizani.

ZOTI NDICHITE

Ngati ndapita kokaonera filimu kapena kwinakwake kokasangalala kenako chikumbumtima changa n’kuyamba kundivutitsa chifukwa cha zimene ndaona kapena kumva, ndidzachita zotsatirazi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani nthawi zina mungaone kuti ndi bwino osawauza makolo anu zinthu zina zofunikira pamene mukupempha chinthu?

● Kodi pangakhale vuto lanji ngati makolo anu atakulolezani kukayenda chifukwa choti mwawabisira zinthu zina zofunika?

[Mawu Otsindika patsamba 268]

“Ndinali mwana wovuta kwambiri. Zinthu zina zimene ndinkachita pofuna kusangalala m’kupita kwa nthawi zinandibweretsera mavuto. Munthu umakolola zimene wafesa moti panopa ndimadandaula kuti sindinkamvera zimene makolo anga ankandiuza.”​—Anatero Brian

[Chithunzi patsamba 269]

Mofanana ndi anthu opulumutsa anthu m’nyanja, makolo anu amaona zinthu zoopsa ngakhale zili kutali