Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Cifunilo ca Mulungu n’Ciani?

Kodi Cifunilo ca Mulungu n’Ciani?

Mulungu amafuna kuti tikhale ndi mtendele ndi cimwemwe m’paradaiso padziko lapansi kwamuyaya.

Koma mungafunse kuti, ‘Kodi zimenezi n’zotheka?’ Baibo imakamba kuti zimenezi zidzatheka ndi Ufumu wa Mulungu, ndipo cifunilo ca Mulungu n’cakuti anthu onse aphunzile za Ufumu umenewo ndi colinga cake kwa ife.—Salimo 37:11, 29; Yesaya 9:7.

Mulungu amafuna kuti zinthu zizitiyendela bwino.

Tate wabwino amafuna kuti ana ake azikhala bwino. Nayenso Atate wathu wa Kumwamba amafuna kuti tizikondwela kwamuyaya. (Yesaya 48:17, 18) Iye walonjeza kuti amene ‘acita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.’—1 Yohane 2:17.

Mulungu amafuna kuti tiziyenda m’njila zake.

Baibo imakamba kuti Mlengi wathu amafuna ‘kutiphunzitsa njila zake,’ kuti ‘tiziyenda m’njila zake’ zimenezo. (Yesaya 2:2, 3) Iye wasankha “anthu odziŵika ndi dzina lake” kuti alalikile za cifunilo cake padziko lonse lapansi.—Machitidwe 15:14.

Mulungu amafuna kuti tizimulambila mogwilizana.

Anthu amene amalambila Yehova amakondana kwambili ndipo amagwilizana m’malo mogaŵanikana. (Yohane 13:35) Kodi masiku ano ndani amene amaphunzitsa amuna ndi akazi kuli konse mmene angatumikilile Mulungu mogwilizana? Ŵelengani kabuku kano kuti mudziŵe.