Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 1

Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?

Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?

Denmark

Taiwan

Venezuela

India

Kodi ndi anthu angati a Mboni za Yehova amene mumawadziwa? N’kutheka kuti a Mboni ena mwayandikana nawo nyumba, mumagwira nawo ntchito kapenanso muli nawo kalasi imodzi kusukulu. Mwinanso anakambiranapo nanu nkhani za m’Baibulo. Koma kodi a Mbonife, ndife ndani kwenikweni ndipo n’chifukwa chiyani timauza ena zimene timakhulupirira?

Tili ngati anthu ena onse. Ndife anthu ochokera m’madera osiyanasiyana komanso a zikhalidwe zosiyanasiyana. Ena mwa ife poyamba anali m’zipembedzo zina, ndipo ena sankakhulupirira n’komwe Mulungu. Komabe tonsefe tisanakhale Mboni, tinayamba kaye taphunzira mosamala kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. (Machitidwe 17:11) Tinavomereza kuti zimene tinkaphunzirazo n’zoonadi, ndipo aliyense anasankha yekha kuti ayambe kulambira Yehova Mulungu.

Kuphunzira Baibulo kumatithandiza. Mofanana ndi munthu wina aliyense, ifenso timalimbana ndi mavuto komanso zofooka zathu. Koma chifukwa choti tsiku ndi tsiku tikuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu, tikutha kuona kuti moyo wathu ukusintha ndipo zinthu zikutiyendera bwino. (Salimo 128:1, 2) Chimenechi n’chifukwa chimodzi chimene chimatichititsa kuuzako ena mfundo zabwino zimene taphunzira m’Baibulo.

Timatsatira mfundo za Mulungu pa moyo wathu. Kuphunzira mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kuti tizisangalala ndiponso kuti tizilemekeza ena. Komanso timayesetsa kukhala anthu oona mtima ndiponso achifundo. Kutsatira mfundozi kumatithandizanso kuti tikhale ndi thanzi labwinopo ndiponso kuti tikhale anthu odalirika m’dera lomwe tikukhala. Komanso mfundozi zimatithandiza kupewa makhalidwe oipa, monga chiwerewere, ndipo timakhala ndi mabanja ogwirizana. Popeza sitikayikira zoti “Mulungu alibe tsankho,” timaona kuti tili m’banja lauzimu la padziko lonse. Banjali ndi logwirizana chifukwa cha zimene timakhulupirira, ngakhale kuti tili m’mayiko osiyanasiyana komanso ndife osiyana mitundu. Gulu lathu ndi lapadera kwambiri ngakhale kuti aliyense wa ife si wosiyana ndi anthu ena onse.​—Machitidwe 4:13; 10:34, 35.

  • Kodi anthu a Mboni za Yehova ndi ofanana bwanji ndi anthu ena onse?

  • Kodi kuphunzira mfundo za m’Baibulo kwathandiza bwanji anthu a Mboni?