Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 2

Ni Cifukwa Ciani Timachedwa Mboni za Yehova?

Ni Cifukwa Ciani Timachedwa Mboni za Yehova?

Nowa

Abulahamu ndi Sara

Mose

Yesu Khristu

Anthu ambili amaganiza kuti dzina lakuti Mboni za Yehova ni dzina la cipembedzo catsopano. Komabe, zaka zopitilila 2,700 zapita, atumiki a Mulungu yekha woona anachedwa “mboni” zake. (Yesaya 43:10-12) Caka ca 1931 cisanafike, tinali kudziŵika ndi dzina lakuti Ophunzila Baibo. Nanga n’cifukwa ciani tinasankha dzina lakuti Mboni za Yehova?

Dzina limeneli limalengeza dzina la Mulungu wathu. M’mipukutu yakale ya Baibo, dzina la Mulungu lakuti Yehova, limapezeka nthawi masauzande ambili. Mu Mabaibo ambili, dzina limeneli analicotsa ndi kuikamo maina audindo monga Ambuye kapena Mulungu. Komabe, Mulungu woona anauza Mose kuti dzina lake ni Yehova. Iye anati: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kale-kale.” (Ekisodo 3:15) Apa, iye anadzisiyanitsa ndi milungu yonse yabodza. Timanyadila kudziŵika ndi dzina loyela la Mulungu.

Dzina limeneli limafotokoza nchito yathu. Anthu ambili akale, kuyambila ndi munthu wolungama, Abele, anacitila umboni za cikhulupililo cao mwa Yehova. M’kupita kwa nthawi, Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Davide ndi ena, anakhalanso m’gulu lalikulu limeneli la “mtambo wa mboni.” (Aheberi 11:4–12:1) Mwacitsanzo, munthu wina angakhale mboni m’khoti pamlandu wa mnzake amene sanalakwe. Nafenso sitidzasiya kuuza anthu coonadi ponena za Mulungu.

Timatsatila citsanzo ca Yesu. Baibo imanena kuti Yesu ni “mboni yokhulupilika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Yesu iye yekha anakamba kuti ‘anadziŵitsa dzina la Mulungu’ ndipo ‘anacitila umboni coonadi’ conena za Mulungu. (Yohane 17:26; 18:37) Conco, otsatila eni-eni a Kristu ayenela kulengeza dzina la Yehova ndi kulidziŵitsa kwa anthu. Izi n’zimene Mboni za Yehova zimalimbikila kucita.

  • Kodi n’cifukwa ciani Ophunzila Baibo anasankha dzina lakuti Mboni za Yehova?

  • Kodi Yehova wakhala ndi Mboni padziko lapansi kuyambila liti?

  • Kodi Mboni yaikulu ya Yehova ndani?