Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 6

Kuyanjana ndi Akhristu Anzathu Kumatithandiza Pambali Ziti?

Kuyanjana ndi Akhristu Anzathu Kumatithandiza Pambali Ziti?

Ngakhale ngati timadutsa m’nkhalango yoopsa kapena ngati kunja sikunace bwino, sitiphonya misonkhano yathu yacikristu. Mboni za Yehova zimakumana ndi mavuto pa umoyo wao ndipo zimatopa ndi nchito. Koma sizilephela kusonkhana ndi Akristu anzao. Cifukwa ciani?

Misonkhano imatilimbikitsa. Paulo analemba kuti “tiganizilane.” Apa anali kukamba za kuganizila amene timasonkhana nao. (Aheberi 10:24) Mau amenewa amatanthauza “kuganizilana mozama,” m’mau ena, kudziŵana bwino wina ndi mnzake. Conco, mau a mtumwi Paulo amenewa amatilimbikitsa kudela nkhawa anzathu. Tikayamba kudziŵana ndi mabanja a Akristu anzathu, timapeza kuti ena a io apilila mavuto ofanana ndi athu ndi kuti io angatithandize kupilila.

Kumalimbitsa ubwenzi wathu. Amene timasonkhana nao, si anthu amene timadziŵana nao patali-patali iyai, koma ni mabwenzi apamtima. Nthawi zina, timakhalanso ndi maceza abwino. Koma kodi mayanjano amenewa ali ndi ubwino wanji? Mayanjano amenewa amatithandiza kuona kuti tonse ndife ofunika, ndipo zimenezi zimalimbitsa cikondi cathu. Ndiyeno, anzathu akakumana ndi mavuto, timakhala okonzeka kuwathandiza cifukwa ndife mabwenzi ao eni-eni. (Miyambo 17:17) Ngati tiyanjana ndi onse mumpingo, timaonetsa kuti ‘timasamalilana mofanana.’—1 Akorinto 12:25, 26.

Tikulimbikitsani kusankha anthu amene amacita cifunilo ca Mulungu kukhala mabwenzi anu. Mabwenzi ngati amenewa mungawapeze pakati pa Mboni za Yehova. Conde musalole ciliconse kukulepeletsani kuyanjana nafe.

  • Kodi kuyanjana kwathu pamisonkhano kuli ndi ubwino wanji?

  • Kodi ni liti pamene mungafune kusonkhana nafe kuti mutidziŵe bwino?