Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 7

Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?

Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?

New Zealand

Japan

Uganda

Lithuania

Pamisonkhano ya Akhristu oyambirira, ankaimba nyimbo, kupemphera, kuwerenga komanso kukambirana Malemba, ndipo sipankachitika miyambo iliyonse yamakolo. (1 Akorinto 14:26) Masiku ano, misonkhano ya Mboni za Yehova imachitikanso chimodzimodzi.

Timalandira malangizo othandiza ochokera m’Baibulo. Pa mapeto pa mlungu, mpingo uliwonse umasonkhana kuti umvetsere nkhani ya m’Baibulo ya mphindi 30. Nkhaniyi imatithandiza kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito Malemba pa moyo wathu komanso imatithandiza kuona mmene malembawo akugwirizanira ndi zimene zikuchitika panopa. Pa nthawiyi, tonse timayenera kutsegula Baibulo lathu n’kumawerenga limodzi ndi munthu amene akukamba nkhaniyo. Nkhaniyo ikatha, timakhala ndi Phunziro la “Nsanja ya Olonda,” lomwe limachitika kwa ola limodzi. Phunziro limeneli limachitika pogwiritsira ntchito magazini yophunzirira ya Nsanja ya Olonda, ndipo aliyense mu mpingo amakhala ndi mwayi wopereka ndemanga zake. Phunziro limeneli limatithandiza kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pa moyo wathu. Mlungu uliwonse mipingo yonse ya Mboni za Yehova yoposa 110,000 padziko lonse, imaphunzira nkhani yofanana.

Timathandizidwa kuti tikhale aphunzitsi aluso. Tsiku lina mlungu womwewo, timachita msonkhano womwe umakhala ndi mbali zitatu. Msonkhanowu, umadziwika kuti Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Nkhani zomwe zimakambidwa pa msonkhanowu zimachokera mu ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu yomwe imatuluka mwezi ndi mwezi. Mbali yoyamba ya msonkhano umenewu yomwe ili ndi mutu wakuti, Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu, imatithandiza kumvetsa bwino mbali ina ya m’Baibulo imene abale ndi alongo anapemphedwa kuti awerenge mlungu umenewo. Mbali yachiwiri ili ndi mutu wakuti, Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki. Abale ndi alongo amachita zitsanzo zosonyeza zimene tingachite pokambirana ndi munthu mfundo za m’Baibulo. M’bale yemwe ndi mlangizi wa mbali imeneyi amaperekanso malangizo omwe amatithandiza kuti tiziwerenga komanso kufotokoza mfundo momveka bwino. (1 Timoteyo 4:13) Mbali yachitatu, yomwe ndi yomaliza ili ndi mutu wakuti, Moyo Wathu Wachikhristu. Wokamba nkhani imeneyi amakambirana ndi abale ndi alongo mfundo zowathandiza kuti amvetse bwino Baibulo, ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito mafunso amene ali m’nkhaniyi.

Mukadzabwera kumisonkhano yathu, sitikukayikira kuti mudzasangalala ndi maphunziro apamwamba ochokera m’Baibulo.​—Yesaya 54:13.

  • Kodi mungayembekezere kudzaphunzira zotani kumisonkhano ya Mboni za Yehova?

  • Pa misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu, kodi ndi msonkhano uti umene mungakonde kudzapezekapo?