Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 7

Kodi Misonkhano Yathu Imacitika Bwanji?

Kodi Misonkhano Yathu Imacitika Bwanji?

Ku New Zealand

Ku Japan

Ku Uganda

Ku Lithuania

Misonkhano ya Akristu oyambilila inali kuphatikizapo kuimba nyimbo, kupemphela, kuŵelenga ndi kukambitsilana Malemba, ndipo sipanali kukhala mwambo wapadela ngakhale umodzi. (1 Akorinto 14:26) Mudzaona zofanana ndi zimenezi mukabwela pamisonkhano yathu.

Malangizo ake amacokela m’Baibo ndipo ni othandiza. Kumapeto kwa wiki, mpingo ulionse umasonkhana kumvetsela nkhani ya m’Baibo ya mamineti 30. Nkhani imeneyi imafotokoza mmene tingagwilitsile nchito Malemba pa umoyo wathu ndi zimene Malemba amanena za nthawi imene tikukhala. Pamene mkambi aŵelenga Malemba, tonse timatsatila m’Mabaibo athu. Nkhani ikatha, pamakhala Phunzilo la Nsanja ya Olonda” kwa ola limodzi, ndipo onse opezekapo amakhala ndi ufulu woyankhapo pokambitsilana nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yophunzila. Phunzilo limeneli limatithandiza kutsatila malangizo a m’Baibo pa umoyo wathu. Nkhani imeneyi imaphunzilidwa mumipingo yonse yopitilila 110,000 padziko lonse lapansi.

Imatithandiza kuonjezela luso lathu lophunzitsa. Timakhalanso ndi msonkhano wina mkati mwa wiki wa mbali zitatu wochedwa Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhiristu. Pa msonkhanowu, timaphunzila nkhani za mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu. Mbali yoyamba ya msonkhanowu, yakuti Cuma Copezeka m’Mau a Mulungu, imatithandiza kumvetsetsa malemba amene abale ndi alongo anaŵelenga asanabwele kudzasonkhana. Mbali yaciŵili ndi yakuti Citani Khama pa Ulaliki, imene imakhala ndi zitsanzo zotithandiza kudziŵa mmene tingafotokozele mfundo za m’Baibo kwa anthu. Pamakhala mlangizi amene amaona mbali zina zimene tifunika kuongolela kuti tiziŵelenga ndi kulankhula mwaluso. (1 Timoteyo 4:13) Pa mbali yotsiliza yakuti Umoyo Wathu Wacikhiristu, timaphunzila mmene tingaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo pa umoyo wathu. Pamakhalanso nkhani ya mafunso ndi mayankho imene imatithandiza kumvetsetsa Baibo.

Mukabwela kumisonkhano yathu, sitikaikila kuti mudzasangalala ndi maphunzilo apamwamba a m’Baibo amene mudzalandila.—Yesaya 54:13.

  • Kodi mudzaphunzila ciani mukabwela pamisonkhano ya Mboni za Yehova?

  • Kodi ndi msonkhano uti umene mungakonde kupezekapo?