PHUNZILO 12
Kodi Nchito Yathu Yolalikila Ufumu Imacitika Bwanji?
Yesu anakamba kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” Anakamba zimenezi imfa yake itayandikila. (Mateyu 24:14) Kodi nchito yolalikila padziko lonse lapansi imeneyi ikanatheka bwanji? Ikanatheka mwa kutsatila citsanzo cimene Yesu anasiya pamene anali padziko lapansi.—Luka 8:1.
Timafikila anthu kunyumba zao. Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kulalikila uthenga wabwino nyumba ndi nyumba. (Mateyu 10:11-13; Machitidwe 5:42; 20:20) Alaliki a m’zaka za zana loyamba amenewo anapatsidwa magao olalikilamo. (Mateyu 10:5, 6; 2 Akorinto 10:13) Ngakhale masiku ano, nchito yathu yolalikila imacitika mwadongosolo, ndipo mpingo ulionse umakhala ndi gao. Zimenezi zimatithandiza kumvela lamulo la Yesu lakuti “tilalikile kwa anthu ndi kupeleka umboni wokwanila.”—Machitidwe 10:42.
Timayesetsa kufikila anthu kulikonse kumene angapezeke. Yesu anapelekanso citsanzo mwa kulalikila kwa anthu kumalo osiyana-siyana, monga m’mbali mwa nyanja kapena pacitsime. (Maliko 4:1; Yohane 4:5-15) Nafenso timakambitsilana ndi anthu za m’Baibo kulikonse kumene tingawapeze—m’miseu, m’malo amalonda, m’mapaki, kapena pafoni. Tikakhala ndi mpata wabwino, timalalikilanso anansi athu, anzathu a kunchito, anzathu a kusukulu, ndi acibanja. Njila zonse izi zathandiza kuti mamiliyoni a anthu padziko lonse lapansi amve “uthenga wabwino wa cipulumutso.”—Salimo 96:2.
Kodi ndani amene mungafune kuuzako uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzawacitila mtsogolo? Musawamane uthenga wa ciyembekezo umenewu. Auzeni mwamsanga!
-
Kodi “uthenga wabwino” umene tiyenela kulalikila ni uthenga wanji?
-
Kodi Mboni za Yehova zimatsatila bwanji citsanzo ca Yesu polalikila?