Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 13

Kodi Mpainiya Amachita Chiyani?

Kodi Mpainiya Amachita Chiyani?

Canada

Kulalikira kunyumba ndi nyumba

Phunziro la Baibulo

Akuphunzira Baibulo payekha

Mawu akuti “mpainiya” kawirikawiri amatanthauza munthu amene amayambitsa zinthu zinazake zimene ena sanachitepo ndipo amapereka chitsanzo kwa ena kuti atsanzire. Yesu anali ngati mpainiya, chifukwa chakuti anatumizidwa padziko lapansi kuti adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake n’cholinga choti anthuwo adzapulumuke. (Mateyu 20:28) Masiku ano, otsatira ake akumutsanzira pogwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri pa ntchito ‘yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.’ (Mateyu 28:19, 20) Pofuna kugwira ntchito imeneyi mokwanira, ena anayamba utumiki umene umadziwika ndi dzina lakuti upainiya.

Mpainiya ndi munthu amene amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Aliyense wa Mboni za Yehova amalalikira uthenga wabwino. Komabe, ena anasintha zina ndi zina pa moyo wawo kuti akhale apainiya okhazikika, ndipo amathera maola 70 mwezi uliwonse pa ntchito yolalikira. Kuti akwanitse kuchita utumiki umenewu, ambiri amayesetsa kupeza ntchito imene ingawapatse mpata. Ena amasankhidwa kuti akatumikire monga apainiya apadera, kudera limene kukufunika anthu ambiri olalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Mwezi uliwonse apainiyawa amatha maola 130 kapena kuposa akulalikira ndi kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Apainiya amakhala moyo wosalira zambiri chifukwa amadziwa kuti Yehova adzawapatsa zinthu zonse zofunika pa moyo wawo. (Mateyu 6:31-33; 1 Timoteyo 6:6-8) Amene sangakwanitse kuchita upainiya wokhazikika amachita upainiya wothandiza pa nthawi imene apeza mpata. Zimenezi zimawapatsa mwayi wowonjezera ntchito yawo yolalikira, ndipo amatha maola 30 kapena 50 pa mwezi akugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu.

Mpainiya amagwira ntchito yakeyi chifukwa chokonda Mulungu ndi anthu. Mofanana ndi Yesu, ifenso timaona kuti masiku ano pali anthu ambiri amene akufunikira kuphunzitsidwa za Mulungu ndi zolinga zake. (Maliko 6:34) Choncho popeza kuti ifeyo tikudziwa zinthu zambiri zimene zingawathandize panopa, timawaphunzitsa kuti aziyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Chifukwa chokonda anthu, mpainiya amagwiritsa ntchito nthawi yake komanso mphamvu zake pothandiza ena kuti amve uthenga wabwino. (Mateyu 22:39; 1 Atesalonika 2:8) Zimenezi zimachititsa kuti chikhulupiriro cha mpainiyayo chilimbe, amayandikira kwambiri Mulungu ndiponso amakhala wosangalala kwambiri.​—Machitidwe 20:35.

  • Kodi mpainiya amachita chiyani?

  • N’chifukwa chiyani ena amadzipereka kuchita upainiya nthawi zonse?