Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 18

Kodi Timacita Ciani Pakagwa Tsoka Kuti Tithandize Abale Athu?

Kodi Timacita Ciani Pakagwa Tsoka Kuti Tithandize Abale Athu?

Ku Dominican Republic

Ku Japan

Ku Haiti

Pakagwa tsoka, Mboni za Yehova mwamsanga zimapeleka cithandizo kwa abale ao. Zimenezi ni umboni wakuti tili ndi cikondi ceni-ceni pakati pathu. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:17, 18) Kodi timawathandiza m’njila ziti?

Timapeleka ndalama. Pamene ku Yudeya kunagwa njala yaikulu, Akristu oyambilila ku Antiokeya anatumiza ndalama kwa abale ao auzimu. (Machitidwe 11:27-30) Ifenso tikamva kuti abale athu kumaiko ena tsoka lawagwela, timatumiza ndalama kupitila m’mipingo yathu kuti zikathandize abale athu amene akuvutika.—2 Akorinto 8:13-15.

Zimene timacita popeleka thandizo. Akulu amene ali kudela limene kwagwa tsoka, amafuna-funa m’bale ndi mlongo aliyense wa mumpingo kuti adziŵe amene alipo ndi kuti ali bwanji. Komiti yoyang’anila za cithandizo imayendetsa nchito yogaŵila zakudya, madzi akumwa, zovala, malo ogona, ndi mankhwala. Mboni zambili zimene zili ndi luso zimadzipeleka mwa kugwilitsila nchito ndalama zao kukapeleka thandizo kapena kukakonza nyumba za abale ndi Nyumba za Ufumu. Gulu lathu n’logwilizana kwambili ndipo taphunzila zambili mwa kugwilila nchito pamodzi. Izi zimatithandiza kucitapo kanthu mwamsanga pakagwa tsoka. Ngakhale kuti timathandiza maka-maka “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo,” timathandizanso anthu a zipembedzo zina mpata ukapezeka.—Agalatiya 6:10.

Timapeleka thandizo lauzimu ndi cilimbikitso. Anthu tsoka likawagwela, amafunika citonthozo cacikulu. Pa nthawi imeneyi, timapeza cilimbikitso kwa Yehova, “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Timauza anthu otaya mtima malonjezo a m’Baibo ndi kuwatsimikizila kuti posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzacotsa masoka onse amene amativutitsa.—Chivumbulutso 21:4.

  • N’cifukwa ciani Mboni zimacitapo kanthu mwamsanga pakagwa tsoka?

  • Kodi anthu amene tsoka lawagwela tingawapatse citonthozo canji cauzimu?