Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 19

Kodi Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru ndani?

Kodi Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru ndani?

Tonse timapindula ndi chakudya chauzimu

Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa, anakambirana pambali ndi ophunzira ake anayi, omwe anali Petulo, Yakobo, Yohane ndi Andireya. Pamene Yesu ankalosera zinthu zimene zidzakhale chizindikiro choti iye wayamba kulamulira, anafunsa funso lofunika kwambiri. Iye anati: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?” (Mateyu 24:45) Pamenepa Yesu ankatsimikizira ophunzira akewo kuti iye, monga “mbuye” wawo, adzaika anthu oti nthawi zonse azidzapereka chakudya chauzimu kwa otsatira ake onse, m’nthawi ya mapeto. Kodi Yesu anaika ndani kuti akhale kapolo ameneyu?

Ndi gulu laling’ono la Akhristu odzozedwa. “Kapolo” ameneyu amadziwikanso kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndipo akugwira mwakhama ntchito yopereka chakudya chauzimu pa nthawi yake kwa Akhristu anzawo amene akulambira nawo Yehova. Timadalira kapolo wokhulupirikayu kuti azitipatsa “chakudya chokwanira pa nthawi yake.”​—Luka 12:42.

Kapoloyu amasamalira nyumba ya Mulungu. (1 Timoteyo 3:15) Yesu anapatsa kapoloyu udindo waukulu wotsogolera ntchito imene mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova ikuchita. Kapoloyu amatsogolera ntchito yolalikira, amatiphunzitsa kudzera m’mipingo, komanso amayang’anira katundu yense wa gulu la Yehova. Choncho pofuna kutipatsa chakudya chapanthawi yake, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa mabuku omwe timawagwiritsa ntchito polalikira, komanso amatipatsa chakudyachi kudzera m’misonkhano yathu ya mpingo ndiponso ikuluikulu.

Kapoloyu ndi wokhulupirika chifukwa chakuti amatsatira choonadi cha m’Baibulo ndiponso amagwira modzipereka ntchito imene anapatsidwa yolalikira uthenga wabwino. Komanso ndi wanzeru chifukwa chakuti amasamalira mwanzeru zinthu za Khristu padziko lapansi. (Machitidwe 10:42) Yehova akudalitsa ntchito imene kapoloyu akugwira. Iye akuchita zimenezi pokoka anthu ambiri kuti akhale mboni zake, komanso pothandiza kapoloyu pa ntchito yake yopereka chakudya chauzimu chochuluka.​—Yesaya 60:22; 65:13.

  • Kodi Yesu anaika ndani kuti azipereka chakudya chauzimu kwa ophunzira ake?

  • N’chifukwa chiyani tinganene kuti kapoloyu ndi wokhulupirika komanso ndi wanzeru?