Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 21

Kodi Beteli N’chiyani?

Kodi Beteli N’chiyani?

Dipatimenti ya Zithunzi, ku United States

Germany

Kenya

Colombia

Mawu akuti Beteli anachokera ku mawu achiheberi otanthauza kuti “Nyumba ya Mulungu.” (Genesis 28:17, 19) A Mboni za Yehova ali ndi maofesi ambiri m’mayiko osiyanasiyana. Maofesiwa amatchedwa Beteli, ndipo dzinali ndi loyenereradi. Anthu omwe amagwira ntchito kumaofesi amenewa amayang’anira ndi kuthandizira ntchito yolalikira m’mayiko awo. Likulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse lili m’dziko la United States, m’dera la New York, ndipo n’kumene kuli Bungwe Lolamulira. Bungweli limayang’anira ntchito zomwe zikuchitika m’maofesi a Mboni za Yehova amene ali m’mayiko ambirimbiri. Gulu lonse la anthu amene amatumikira pamaofesiwa limatchedwa banja la Beteli. Iwo monga banja, amachitira zinthu limodzi monga kugwira ntchito, kuphunzira Baibulo, komanso amadyera limodzi.​—Salimo 133:1.

Beteli ndi malo apadera, ndipo anthu a m’banja la Beteli ali ndi mtima wodzipereka. Paofesi iliyonse ya Mboni za Yehova, pamakhala amuna ndi akazi achikhristu amene nthawi zonse amagwira ntchito yopititsa patsogolo zinthu za Ufumu, komanso amachita chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 6:33) Palibe amene amalandira malipiro alionse komabe aliyense amapatsidwa chipinda chabwino chogona, chakudya komanso ndalama zochepa zoti agulire zinthu zina zofunika. Anthu a pa Beteli amagwira ntchito zosiyanasiyana, monga muofesi, kukhitchini kapena kuchipinda chodyera. Ntchito zina ndi monga kusindikiza mabuku, kukonza kuzipinda zogona, kuchapa zovala ndiponso kukonza zinthu.

Ku Beteli kumachitika zinthu zambiri zothandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu. Cholinga chachikulu cha Beteli iliyonse n’kuthandiza anthu ambirimbiri kuti adziwe choonadi cha m’Baibulo. Kabuku kano ndi chitsanzo cha zimenezi. Bungwe Lolamulira linayang’anira ntchito yolemba kabukuka, kenako kanatumizidwa kwa omasulira osiyanasiyana padziko lonse. Omasulirawo atamaliza ntchito yawo anatumiza kwa osindikiza omwe ali m’maofesi osiyanasiyana a Mboni za Yehova. Iwo amagwiritsa ntchito makina amene amasindikiza mabuku ambiri pa nthawi yochepa, kenako amatumiza mabukuwo kumipingo yoposa 110,000. Pogwira ntchito zonsezi, mabanja a Beteli amakhala akuthandiza ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino imene ikufunika kuchitika mwamsanga.​—Maliko 13:10.

  • Kodi ndi anthu otani omwe amatumikira pa Beteli, ndipo amasamaliridwa bwanji?

  • Kodi Beteli iliyonse imathandizira pa ntchito iti yofunika kwambiri, imene ikufunika kuchitika mwamsanga?