Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 21

Kodi Beteli n’Ciani?

Kodi Beteli n’Ciani?

Dipatimenti Yojambula Zithunzi, ku U.S.A.

Ku Germany

Ku Kenya

Ku Colombia

Pa Ciheberi, dzina lakuti Beteli limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” (Genesis 28:17, 19) Limeneli ndi dzina loyenelela la malo amene Mboni za Yehova zakhazikitsa padziko lonse. Ku malo amenewa n’kumene amayang’anila nchito yolalikila. Bungwe Lolamulila lili kumalikulu a padziko lonse m’boma la New York, U.S.A., ndipo limayang’anila maofesi a nthambi m’maiko osiyana-siyana. Anthu amene amatumikila kumalo amenewa amachedwa kuti banja la Beteli. Monga banja, amakhalila pamodzi, amagwilila nchito pamodzi, amadyela pamodzi, ndi kuphunzilila Baibo pamodzi.—Salimo 133:1.

Malo apadela kumene onse m’banja ali ndi mzimu wodzimana. Beteli iliyonse ili ndi amuna ndi akazi acikristu odzipeleka kucita cifunilo ca Mulungu ndipo amacilikiza zinthu za Ufumu nthawi zonse. (Mateyu 6:33) Palibe amene amalandila malipilo alionse, koma onse amapatsidwa malo okhala, cakudya, ndi alawansi yowathandiza pa zinthu zaumwini. Aliyense pa Beteli ali ndi nchito yake, kaya ni ya mu ofesi, mu khichini, kapena m’cipinda codyela. Ena amaseŵenzela kosindikizila mabuku kapena koikila zikuto. Ena amayeletsa m’nyumba, amacapa, amagwila nchito yokonza zinthu, kapena nchito zina.

Kumacitika zambili zocilikiza nchito yolalikila Ufumu. Colinga cacikulu ca Beteli ni kufalitsa coonadi ca m’Baibo kwa anthu ambili. Citsanzo cake ni kabuku kano. Bungwe Lolamulila ni limene linayang’anila nchito ya kulemba kabuku kano, kukatumiza pakompyuta kwa otembenuza padziko lonse, kukasindikiza pamakina ofulumila kwambili kunyumba za Beteli zosiyana-siyana, ndi kukatumiza kumipingo yopitila 110,000. Pa zocitika zonse izi, mabanja a Beteli amakhala akucilikiza nchito yofunika kwambili pa zonse—nchito yolalikila uthenga wabwino.—Maliko 13:10.

  • Kodi ndani amene amatumikila pa Beteli, ndipo amawasamalila bwanji?

  • Kodi Beteli iliyonse imacilikiza nchito yofunika kwambili iti?