Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 22

Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?

Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?

Ku Solomon Islands

Ku Canada

Ku South Africa

A banja la Beteli amatumikila m’madipatimenti osiyana-siyana, kusamalila nchito yolalikila m’dziko limodzi kapena angapo. Ena amagwila nchito yotembenuza, yosindikiza magazini, yoika zikuto kumabuku, ndipo ena amagwila nchito kosungila mabuku, kopangila ma CD ndi mavidiyo, kapena amasamalila nchito zina zokhudza dela lao.

Komiti ya Nthambi imayang’anila nchito. Bungwe Lolamulila lapeleka udindo wosamalila ofesi ya nthambi iliyonse m’manja mwa Komiti ya Nthambi ya akulu oyenelela atatu kapena oposelapo. Komiti ya Nthambi imadziŵitsa Bungwe Lolamulila za kupita patsogolo kwa nchito ndiponso mavuto amene angabuke m’dela lao. Malipoti amenewa amathandiza Bungwe Lolamulila kuona nkhani zimene angalembe m’zofalitsa zathu ndi mfundo zimene angaphatikize m’nkhani za misonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikulu-ikulu. Oimila Bungwe Lolamulila amatumizidwa nthawi ndi nthawi kukacezela nthambi kuti apeleke malangizo ku Komiti ya Nthambi a mmene ingagwilile nchito zake. (Miyambo 11:14) Pamakhala pulogilamu yapadela ndipo, woimila likulu lathu amakamba nkhani yolimbikitsa onse m’dela la nthambi imeneyo.

Amacilikiza mipingo. Abale audindo ku ofesi ya nthambi amavomeleza kuti mipingo yatsopano ikhazikitsidwe. Amayang’anilanso nchito ya apainiya, amishonale, ndi oyang’anila dela amene ali m’dela la nthambi yao. Amakonza misonkhano ikulu-ikulu, amayang’anila nchito yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano, ndipo amatsimikiza kuti mabuku amene akufunika atumizidwa kumipingo. Nchito zonse zimene zimacitika ku ofesi ya nthambi zimathandiza kuti nchito yolalikila iziyenda mwadongosolo.—1 Akorinto 14:33, 40.

  • Kodi Makomiti a Nthambi amathandiza Bungwe Lolamulila m’njila ziti?

  • Kodi ni nchito ziti zimene ofesi ya nthambi imasamalila?