Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 24

Kodi Ndalama za Nchito Yathu Zimacokela Kuti?

Kodi Ndalama za Nchito Yathu Zimacokela Kuti?

Ku Nepal

Ku Togo

Ku Britain

Caka ciliconse, gulu lathu limasindikiza Mabaibo ndi mabuku mamiliyoni ambili ndi kuwagaŵila popanda kulipilitsa. Timamanga Nyumba za Ufumu ndi maofesi a nthambi ndipo timazisamalila. Timacilikiza abale ndi alongo ambili a pa Beteli ndi amishonale, ndipo timapeleka thandizo pakagwa tsoka. Conco mungafunse kuti: ‘Kodi ndalama zake zimacokela kuti?’

Sitipeleka cakhumi, kulipilitsa mtulo, kapena kuyendetsa mbale ya zopeleka. Nchito yathu yolalikila imafuna ndalama zambili, koma sitipempha ndalama. Zaka zopitilila 100 m’mbuyomu, magazini yaciŵili ya Nsanja ya Olonda inakamba kuti timakhulupilila kuti Yehova ndiye amatithandiza ndi kuti “sitidzapempha thandizo kwa anthu”—ndipo sitinapemphepo!Mateyu 10:8.

Nchito yathu imacilikizidwa ndi zopeleka zaufulu. Anthu ambili amayamikila nchito yathu yophunzitsa Baibo ndipo amapeleka ndalama kuthandiza pa nchito imeneyi. Ndipo Mboni za Yehova mocokela pansi pa mtima zimagwilitsila nchito nthawi yao, mphamvu zao, ndalama zao, ndi zinthu zina kucita cifunilo ca Mulungu padziko lonse. (1 Mbiri 29:9) Pa Nyumba ya Ufumu, pa misonkhano yadela ndi ya cigawo, pamakhala mabokosi a zopeleka, kuti amene afuna aponyemo. Kapena mungacite zopeleka kupitila pa webusaiti yathu ya jw.org. Nthawi zambili, zopeleka zimene timalandila zimacokela kwa anthu amene alibe zambili, monga mkazi wamasiye wosauka uja, amene Yesu anayamikila cifukwa coponya tumakobili tuŵili moponyamo zopeleka. (Luka 21:1-4) Conco, aliyense ‘angaziika kenakake pambali’ kuti apeleke “mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake.”—1 Akorinto 16:2; 2 Akorinto 9:7.

Tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzapitiliza kusonkhezela mitima ya anthu amene amafuna ‘kumulemekeza ndi zinthu zao zamtengo wapatali,’ kuti acilikize nchito ya Ufumu, kotelo kuti cifunilo cake cicitike.—Miyambo 3:9.

  • Kodi gulu lathu limasiyana bwanji ndi zipembedzo zina?

  • Kodi zopeleka zaufulu zimagwila nchito yanji?