Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 25

Timamangilanji Nyumba za Ufumu? Nanga Timamanga Bwanji

Timamangilanji Nyumba za Ufumu? Nanga Timamanga Bwanji

Ku Bolivia

Ku Nigeria, yakale ndi yatsopano

Ku Tahiti

Malinga ndi dzinali lakuti Nyumba ya Ufumu, ciphunzitso cacikulu ca m’Baibo cimene timaphunzila kumeneko cimanena za Ufumu wa Mulungu. Imeneyi inali mfundo yaikulu ya ulaliki wa Yesu.—Luka 8:1.

Ni malo olambilila Mulungu. Nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu imacitika kucokela kumalo amenewa. (Mateyu 24:14) Nyumba za Ufumu zimasiyana-siyana ukulu ndi kamangidwe kake, koma sizikhala zazikulu ndi zokongola mopitilila malile. Ndipo zambili zimagwilitsilidwa nchito ndi mipingo ingapo. Pa zaka za posacedwapa, tamanga Nyumba za Ufumu masauzande (pa avaleji Nyumba za Ufumu 5 pa tsiku) kuti tikwanitse kusamalila mipingo imene iculukila-culukila. Kodi zimenezi zatheka bwanji?—Mateyu 19:26.

Ndalama zomangila zimacokela ku thumba limene anakhazikitsa. Zopeleka zimenezi zimatumizidwa ku ofesi ya nthambi kuti izipeleka ndalama ku mipingo imene ifuna kumanga kapena kukonzanso Nyumba ya Ufumu.

Zimamangidwa ndi anchito ongodzipeleka amene salipilidwa ndiponso a zikhalidwe zosiyana-siyana. M’maiko ambili akhazikitsa Magulu Omanga Nyumba za Ufumu. Atumiki a nchito yomanga ndi anchito ongodzipeleka amapita kumipingo yosiyana-siyana ngakhale m’madela a kutali a m’dziko lao, kuti akathandizile mipingo kumanga Nyumba za Ufumu. M’maiko ena, abale oyenelela aikidwa kuti aziyang’anila nchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu m’zigao zimene anapatsidwa. Ngakhale kuti abale amene ali ndi luso amadzipeleka kuthandiza pamalo a cimango alionse, unyinji wa amene amagwila nchito yodzipeleka ni abale ndi alongo a pampingopo. Nchito imeneyi imatheka cifukwa ca mzimu wa Yehova ndi anthu ake amene amadzipeleka ndi mtima wonse.—Salimo 127:1; Akolose 3:23.

  • N’cifukwa ciani malo athu olambilila amachedwa Nyumba za Ufumu?

  • Kodi timakwanitsa bwanji kumanga Nyumba za Ufumu padziko lonse lapansi?