Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 27

Kodi Tingapindule Bwanji Ndi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu?

Kodi Tingapindule Bwanji Ndi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu?

Ku Israel

Ku Czech Republic

Ku Benin

Ku Cayman Islands

Kodi mungakonde kufufuza zinthu zina kuti muonjezele cidziŵitso canu ca m’Baibo? Kodi mufuna kudziŵa lemba lina lake, munthu, malo, kapena kanthu kena kake kochulidwa m’Baibo? Kapena kodi mufuna kudziŵa ngati Mau a Mulungu angakuthandizeni pa vuto lina lake limene muli nalo? Ngati ni conco, pitani ku laibulale ya ku Nyumba ya Ufumu.

Kuli ziwiya zothandiza pofufuza. Inu muyenela kuti mulibe mabuku onse a cinenelo canu ofotokoza Baibo, olembedwa ndi Mboni za Yehova. Koma laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu ili ndi mabuku ambili atsopano. Ingakhalenso ndi Mabaibo osiyana-siyana, dikishonale yabwino, ndi malifalensi ena othandiza pofufuza. Laibulale imeneyi mungaigwilitsile nchito misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake. Ngati pali kompyuta ndiye kuti mwina ili ndi Watchtower Library. Imeneyi ni pulogalamu ya pakompyuta imene ili ndi mabuku ambili ndipo ni yosavuta kuigwilitsila nchito pofufuza nkhani ina yake, liu, kapena lemba.

Imathandiza ophunzila mu Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Mungagwilitsile nchito laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu pokonzekela mbali yanu. Woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki ndiye amayang’anila laibulale. Iye amaonetsetsa kuti mabuku atsopano alimo ndipo aikidwa mwadongosolo. Iye kapena mphunzitsi wanu wa Baibo angakuonetseni mmene mungapezele nkhani imene mufuna. Komabe, mabuku a mu laibulale sayenela kucoka m’Nyumba ya Ufumu. Ndipo tiyenela kuwasamala bwino ndi kusalembamo.

Baibo imakamba kuti, kuti ‘timudziŵedi Mulungu,’ tiyenela kufuna-funa nzelu “ngati cuma cobisika.” (Miyambo 2:1-5) Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu ingakuthandizeni kuyamba nchito yofuna-funa imeneyo.

  • Kodi ziwiya zofufuzila zimene zimapezeka m’laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu ni ziti?

  • Kodi ndani angakuthandizeni kuti muzigwilitsila nchito bwino laibulale?