Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 28

Kodi pa Webusaiti Yathu Pamapezeka Ciani?

Kodi pa Webusaiti Yathu Pamapezeka Ciani?

Ku France

Ku Poland

Ku Russia

Yesu Kristu anauza otsatila ake kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:16) Kuti ticite zimenezi, timagwilitsila nchito ziwiya zamakono kuphatikizapo Intaneti. Webusaiti ya www.pr418.com, ndiyo adresi yathu yovomelezeka ya pa Intaneti, imene ili ndi nkhani zokhudza zikhulupililo za Mboni za Yehova ndi nchito yao. Kodi pamapezeka ciani?

Mayankho a m’Baibo a mafunso amene anthu ambili amafunsa. Mungapeze mayankho a mafunso ofunika kwambili amene anthu afunsapo. Mwacitsanzo, tumapepa twakuti Kodi Mavuto Adzathadi? ndi Kodi N’zoona kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?, tulipo pa Webusaiti m’zinenelo zoposa 600. Mungapezenso Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenelo zopitilila 130 ndi mabuku ena othandiza kumvetsetsa Baibo, kuphatikizapo buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa m’Ceni-ceni, ndiponso magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mungaŵelenge kapena kumvetsela zofalitsa zimenezi pa Intaneti kapena kuzitenga pamenepo zili mumpagidwe wa MP3, PDF, kapena EPUB. Mungasindikize ngakhale mapeji angapo opatsa munthu wacidwi m’cinenelo cake. Palinso mavidiyo a zofalitsa m’zinenelo za manja zosiyana-zosiyana. Mungatengepo maseŵelo a m’Baibo a mau okha, maseŵelo ena a m’Baibo, ndi nyimbo zosangalatsa zomvetsela nthawi iliyonse imene mufuna.

Cidziŵitso codalilika conena za Mboni za Yehova. Pawebusaiti imeneyi amaikapo cidziŵitso ca posacedwa ca mmene nchito yathu ikuyendela padziko lonse, ca zinthu zimene zicitikila Mboni za Yehova, ndi ca nchito yathu yopeleka thandizo pakagwa tsoka, ndi mavidiyo ake. Mungapezenso cidziŵitso ca misonkhano ikulu-ikulu imene ikubwela ndi ma adresi a maofesi a nthambi.

Mwa kugwilitsila nchito njila imeneyi, tikuwalitsa coonadi kumadela akutali padziko lapansi. Anthu kulikonse, ngakhale ku Antarctica, akupindula. Pemphelo lathu ni lakuti, “mau a Yehova apitilize kufalikila mofulumila” padziko lonse lapansi, kuti Mulungu alemekezeke.—2 Atesalonika 3:1.

  • Kodi webusaiti ya www.pr418.com ikuthandiza bwanji anthu ambili kudziŵa coonadi ca m’Baibo?

  • Kodi muli ndi nkhani iliyonse imene mufuna kuona pawebusaiti yathu?