Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Inu Mudzayamba Kucita Cifunilo ca Yehova?

Kodi Inu Mudzayamba Kucita Cifunilo ca Yehova?

Tikuyamikilani kwambili kuti munali kupatula nthawi yoŵelenga kabuku kano. Kakuthandizani kutidziŵa bwino ife Mboni za Yehova, kudziŵa nchito yathu, ndi mmene gulu lathu limagwilila nchito. Tikhulupilila kuti kakuthandizaninso kudziŵa kuti ife ndife amene ticita cifunilo ca Yehova masiku ano. Tikulimbikitsani kuti mupitilize kuphunzila za Mulungu, kuuzako acibanja ndi anzanu zimene mukuphunzila, ndi kuti muzibwela kumisonkhano yathu nthawi zonse.—Aheberi 10:23-25.

Mukapitiliza kuphunzila za Yehova, mudzamvetsetsa kuti iye amakukondani kwambili. Ndipo zimenezi zidzakulimbikitsani kucita zonse zimene mungathe kuti inunso muonetse kuti mumam’konda. (1 Yohane 4:8-10, 19) Koma kodi mungaonetse bwanji zimenezi pa umoyo wanu? N’cifukwa ciani kumvela malamulo a Mulungu pa makhalidwe abwino kungakuthandizeni? Ndipo n’ciani cingakusonkhezeleni kuti muzicita cifunilo ca Mulungu pamodzi ndi ife? Mphunzitsi wanu wa Baibo angakuthandizeni kupeza mayankho kuti inu ndi banja lanu mukhale m’cikondi ca Mulungu kuti mukalandile moyo wosatha.—Yuda 21.

Conco, tikulimbikitsani kupita patsogolo panjila ya coonadi mwa kuphunzilanso buku ili . . .“Khalanibe M’chikondi ca Mulungu.”