Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 15

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupitiriza Kuphunzira za Yehova?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupitiriza Kuphunzira za Yehova?

1. Kodi mungapindule bwanji mukapitiriza kuphunzira Baibulo?

Pofika pano mwaphunzira mfundo zambiri za m’Baibulo ndipo mosakayikira, zakuthandizani kuti muyambe kukonda kwambiri Yehova. Koma nthawi zonse muyenera kuchita zinthu zothandiza kuti chikondicho chizikula. (1 Petulo 2:2) Kuti mudzapeze moyo wosatha zikudalira kuti mupitirize kuyandikira Mulungu mwa kuphunzira Mawu ake.​—Werengani Yohane 17:3; Yuda 21.

Pamene mukupitiriza kudziwa zambiri zokhudza Mulungu, chikhulupiriro chanu chidzalimba kwambiri. Ndiyeno chikhulupirirocho chidzakuthandizani kuti muzichita zinthu zokondweretsa Mulungu. (Aheberi 11:1, 6) Komanso chikhulupiriro chidzakuthandizani kuti mulape n’kusintha moyo wanu.​—Werengani Machitidwe 3:19.

2. Kodi mungatani kuti zimene mukudziwa zokhudza Mulungu zithandizenso anthu ena?

Mungakhale pa ubwenzi wapadera kwambiri ndi Yehova

Mwachibadwa, mudzafuna kuuza anthu ena zimene mwaphunzira, ndipotu tonsefe timasangalala tikamauza anthu ena uthenga wabwino. Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadziwa mmene mungagwiritsire ntchito Baibulo pofotokoza zimene mumakhulupirira zokhudza Yehova ndiponso zokhudza uthenga wabwino.​—Werengani Aroma 10:13-14.

Anthu ambiri akamayamba kuuza ena uthenga wabwino, amayamba ndi kuuza achibale awo kapena anzawo. Koma m’pofunika kuchita zinthu mwanzeru. M’malo mowauza kuti chipembedzo chawo n’cholakwika, auzeni zimene Mulungu walonjeza. Komanso muzikumbukira kuti kawirikawiri anthu amakopeka kwambiri ndi khalidwe lanu la kukoma mtima osati ndi zimene mumalankhula.​—Werengani 2 Timoteyo 2:24, 25.

3. Kodi mungakhale pa ubwenzi wotani ndi Mulungu?

Kuphunzira Mawu a Mulungu kudzakuthandizani kuti mukule mwauzimu. M’kupita kwa nthawi, mungakhale pa ubwenzi wapadera kwambiri ndi Yehova, ndipo mungafike pokhala m’gulu lake, lomwe lili ngati banja.​—Werengani 2 Akorinto 6:18.

4. Kodi mungatani kuti muphunzire zambiri zokhudza Mulungu?

Mukapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu, mungakule kwambiri mwauzimu. (Aheberi 5:13, 14) Choncho, pemphani munthu aliyense wa Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa Mukamaphunzira kwambiri Mawu a Mulungu, mudzaona kuti zinthu zizikuyenderani bwino kwambiri pa moyo wanu.​—Werengani Salimo 1:1-3; 73:27, 28.

Uthenga wabwino ukuchokera kwa Yehova, yemwe ndi Mulungu wachimwemwe. Mungamuyandikire Mulungu ameneyu ngati mungayesetse kugwirizana ndi anthu ake. (Aheberi 10:24, 25) Mukamayesetsa kuchita zonse zimene mungathe kuti musangalatse Yehova, ndiye kuti mukuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kudzapeza moyo weniweni, womwe ndi moyo wosatha. Choncho, chinthu chabwino zedi chomwe mungachite n’kuyandikira Mulungu.​—Werengani 1 Timoteyo 1:11; 6:19.