Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 4

Anakondweletsa Atate Wake ndi Yehova

Anakondweletsa Atate Wake ndi Yehova

Kodi Yefita analonjeza Yehova ciani?

Ngakhale kuti zinali zovuta, mwana wa Yefita anacita zimene atate ake analonjeza

Kodi wamuona mtsikana pacithunzi-thunzi?— Iye ndi mwana wa munthu wina dzina lake Yefita. Dzina lake silinachulidwe m’Baibulo, koma zimene tidziŵa n’zakuti iye anakondweletsa atate wake ndi Yehova. Tiye tiphunzile za mwana ameneyu ndi atate wake, a Yefita.

Yefita anali munthu wabwino ndipo nthawi zambili anali kuphunzitsa mwana wake za Yehova. Analinso munthu wamphamvu komanso mtsogoleli wabwino. Conco, Aisiraeli anamupempha kuti awatsogolele pomenyana ndi adani ao.

Yefita anapempha thandizo la Mulungu kuti apambane. Ndipo iye analonjeza kuti akadzapambana nkhondo, adzapeleka kwa Yehova munthu aliyense woyamba kutuluka m’nyumba yake pamene iye acoka kunkhondo. Munthu ameneyo adzakhala ndi kugwila nchito pa cihema ca Mulungu kwa moyo wake wonse. Cihema cinali malo kumene anthu anali kukumana polambila Mulungu m’nthawi yakale. Yefita anapambanadi nkhondo! Atabwelela kunyumba, kodi udziŵa amene anayambilila kutuluka m’nyumba yake?—

Inde, anali mwana wake wamkazi, ndipo anali mwana mmodzi cabe. Koma tsopano anafunikila kumulola kuti apite kumalo akutali. Yefita anamva cisoni kwambili. Koma kumbukila kuti iye analonjeza. Nthawi imeneyo mwana wake anati: ‘Atate munalonjeza kwa Yehova, conco muyenela kusunga lonjezo.’

Caka ciliconse anzake a mwana wa Yefita anali kupita kukamuona

Mwana wa Yefita nayenso anamva cisoni, cifukwa pa cihema kunalibe kukwatiwa ndi kukhala ndi ana. Koma, iye anafunitsitsa kwambili kukwanilitsa lonjezo la atate wake ndi kukondweletsa Yehova. Zimenezi zinali zofunika kwambili kwa iye kuposa kukwatiwa ndi kukhala ndi ana. Conco, iye anacoka panyumba ndi kukatumikila pa cihema kwa moyo wake wonse.

Uona bwanji, kodi zimene anacita zinakondweletsa atate wake ndi Yehova?— Inde! Ngati umamvela ndi kukonda Yehova, udzakhala ngati mwana wa Yefita. Iwenso udzakondweletsa kwambili makolo ako ndi Yehova.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Deuteronomo 6:4-6

  • Oweruza 11:30-40

  • 1 Akorinto 7:37, 38