Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 7

Kodi Nthawi Zina Umaona kuti Uli Wekha Ndipo Ukucita Mantha?

Kodi Nthawi Zina Umaona kuti Uli Wekha Ndipo Ukucita Mantha?

Ona kamnyamata pa cithunzi-thunzi. Kaoneka kuti kacita mantha, si conco? Kodi tsiku lina unacitapo mantha?— Nthawi zina ife tonse timacita mantha. Baibulo limakamba za anzake a Yehova amene pa nthawi ina anacita mantha. Mmodzi wa io anali Eliya. Tiye tiphunzile za iye.

Yezebeli anafuna kupha Eliya

Eliya anali kukhala ku Isiraeli kale-kale Yesu asanabadwe padziko lapansi. Ahabu mfumu ya Aisiraeli sanali kulambila Yehova Mulungu woona. Ahabu ndi mkazi wake Yezebeli, anali kulambila mulungu wabodza Baala. Conco, anthu ambili mu Isiraeli naonso anayamba kulambila Baala. Mfumukazi Yezebeli anali woipa mtima ndipo anafuna kupha onse olambila Yehova kuphatikizapo Eliya. Kodi udziŵa zimene Eliya anacita?—

Iye anathaŵa. Anathaŵila kucipululu kutali kwambili ndi kubisala m’phanga. Uganiza n’ciani cinam’cititsa kuti athawe?— Iye anacita mantha. Komabe, Eliya sanafunikile kucita mantha. Cifukwa ciani? Cifukwa anadziŵa kuti Yehova adzamuthandiza. Yehova anali atamusonyezapo kale Eliya mphamvu zake. Panthawi ina, Yehova anayankha pemphelo la Eliya mwa kutumiza moto kucoka kumwamba. Mosakaikila konse, Yehova anali kudzam’thandiza Eliya.

Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Eliya?

Pamene Eliya anali m’phanga, Yehova analankhula naye ndipo anamufunsa kuti: ‘Ufuna ciani kuno Eliya?’ Eliya anayankha kuti: ‘Ndine cabe amene ndikali kukulambilani. Ndatsala ndekha, ndipo ndicita mantha kuti adzandipha.’ Eliya anaganiza kuti olambila onse a Yehova aphedwa. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Iyai, si zoona zimenezo. Pali anthu ena 7,000 amene akali kundilambila. Limba mtima. Pali nchito yambili imene ndifuna kuti ucite.’ Kodi uganiza kuti Eliya anakondwela ndi zimenezo?—

Kodi uphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila Eliya?— Suyenela kuona kuti uli wekha kapena kucita mantha. Uli ndi anzako amene amalambila Yehova ndiponso amene amakukonda. Komanso, Yehova ali ndi mphamvu zambili, adzakuthandiza nthawi zonse. Kodi wakondwela kudziŵa kuti nthawi zonse suli wekha?—

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • 1 Mafumu 19:3-18

  • Salimo 145:18

  • 1 Petulo 5:9