Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 9

Yeremiya Sanasiye Kulankhula za Yehova

Yeremiya Sanasiye Kulankhula za Yehova

N’chifukwa chiyani anthuwa akwiyira Yeremiya?

Yehova anapulumutsa Yeremiya

Nthawi zina anthu amatiseka kapena kutikwiyira tikamawauza za Yehova. Zimenezi zikhoza kutichititsa kuti tisiye kulalikira za Mulungu. Kodi iweyo unayamba waganizapo choncho?— Baibulo limatiuza za mnyamata wina yemwe ankakonda Yehova koma nthawi ina anangotsala pang’ono kusiya kulankhula za Yehova. Dzina lake anali Yeremiya. Tiye tikambirane za mnyamata ameneyu.

Yeremiya ali mnyamata, Yehova anamuuza kuti achenjeze anthu kuti asiye kuchita zoipa. Yeremiya anaona kuti ntchito imeneyi ndi yovuta ndipo ankachita mantha. Iye anauza Yehova kuti: ‘Sindingathe kuchita zimenezi chifukwa ndine mwana.’ Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Usachite mantha. Ndikuthandiza.’

Ndiyeno Yeremiya anayamba kuchenjeza anthu kuti adzalangidwa ngati sasintha. Kodi ukuganiza kuti anthuwo anamvera zimene Yeremiya ankawauza?— Ayi, chifukwa anayamba kumuseka komanso kumukwiyira kwambiri. Ndipo ena ankafuna kumupha. Kodi ukuganiza kuti Yeremiya anamva bwanji?— Anachita mantha ndipo ananena kuti: ‘Sindidzauzanso anthu za Yehova.’ Koma kodi anasiyadi kuuza anthu za Yehova?— Ayi, sanasiye. Iye ankakonda Yehova kwambiri moti sakanatha kusiya kulankhula za Yehovayo. Ndipo Yehova anamuteteza chifukwa anapitiriza kulankhula za Iye.

Mwachitsanzo, pa nthawi ina anthu oipa anaponyera Yeremiya m’dzenje momwe munali matope ambiri. Iye analibe chakudya kapena madzi. Anthuwo ankafuna kuti Yeremiya afere m’dzenjemo. Koma Yehova anamupulumutsa.

Kodi ukuphunzirapo chiyani pa zimene zinamuchitikira Yeremiya?— Ngakhale kuti nthawi zina ankachita mantha, sanasiye kulankhula za Yehova. Iwenso ukamalankhula za Yehova, anthu akhoza kukuseka kapena kukukwiyira. Zimenezi zikhoza kukuchititsa mantha kapena manyazi. Koma usadzasiye kulankhula za Yehova. Iye adzakuthandiza ngati mmene anathandizira Yeremiya.