Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 9

Yeremiya Sanaleke Kulankhula za Yehova

Yeremiya Sanaleke Kulankhula za Yehova

N’cifukwa ciani anthu amukalipila Yeremiya?

Yehova anapulumutsa Yeremiya

Nthawi zina anthu amatiseka ndi kutikalipila pamene tiwauzako za Yehova. Zimenezo zingaticititse kuti tileke kukamba za Mulungu. Kodi iwenso zinakucitikilapo?— Baibulo limatiuza za mnyamata wina amene anali kukonda Yehova, koma anatsala pang’ono kuti aleke kukamba za Mulungu. Dzina lake ndi Yeremiya. Tiye tiphunzile zambili za iye.

Pamene Yeremiya anali mwana, Yehova anamuuza kuti akacenjeze anthu kuti aleke kucita zoipa. Izi zinali zovuta kwambili kwa Yeremiya, ndipo zinamucititsa mantha. Iye anauza Yehova kuti: ‘Ndidzakamba ciani ine! Ndine mwana. Koma Yehova anamuuza kuti: Usacite mantha, ndidzakuthandiza.’

Nthawi imeneyo Yeremiya anayamba kucenjeza anthu kuti, adzalangidwa ngati sasintha. Kodi uganiza kuti anthu anamvela zimene Yeremiya anali kukamba?— Iyai sanamvele. M’malo mwake anali kumunyoza kapena kumukalipila kwambili. Ena anafuna kumupha. Kodi uganiza kuti Yeremiya anamva bwanji?— Anacita mantha ndipo anati: ‘Sindidzakambanso za Yehova.’ Koma, kodi zoona analeka kukamba za Mulungu?— Iyai. Sanaleke cifukwa anali kukonda kwambili Yehova. Yehova anamupulumutsa Yeremiya cifukwa cakuti iye sanaleke kukamba za Mulungu.

Mwacitsanzo, panthawi ina anthu oipa anaponya Yeremiya m’citsime cakuya cokhala ndi matope. Analibe cakudya kapena madzi. Amuna amenewo anafuna kuti Yeremiya afele mmenemo. Cifukwa ca thandizo la Yehova, iye anapulumuka.

Kodi uphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yeremiya?— Ngakhale kuti nthawi zina anali kucita mantha, iye sanaleke kulankhula za Yehova. Ngati ulankhula za Yehova, anthu angayambe kukuseka kapena kukukalipila. Ungacite manyazi kapena mantha. Koma suyenela kuleka kulankhula za Yehova. Iye adzakuthandiza nthawi zonse monga mmene anacitila kwa Yeremiya.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Yeremiya 1:4-8; 20:7-9; 26:8-19, 24; 38:6-13