Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 12

Mwana wa Mlongo wa Paulo Anali Wolimba Mtima

Mwana wa Mlongo wa Paulo Anali Wolimba Mtima

Tiye tiphunzile za mnyamata amene anapulumutsa amalume ake. Amalume a mnyamatayu anali mtumwi Paulo. Dzina la mnyamata ameneyu sitilidziŵa, koma zimene tidziŵa ndi zakuti iye anacita zinthu molimba mtima. Kodi ungakonde kudziŵa zimene iye anacita?—

Paulo anali m’ndende ku Yerusalemu. Iye anaikidwa m’ndende cifukwa anali kulalikila za Yesu. Koma anthu ena oipa anadana naye Paulo, conco anakonza ciwembu. Iwo anati: ‘Tiyeni tipemphe mkulu wa asilikali kuti alamule asilikali ake kuti abweletse Paulo ku khoti. Ndiyeno ife tidzabisala panjila kuti pamene Paulo adutsa timuphe.’

Mwana wa mlongo wa Paulo anauza Paulo ndi mkulu wa asilikali za ciwembu

Mwana wa mlongo wa Paulo anamva za ciwembu cimeneco. Kodi iye anacita ciani? Anapita kundende ndi kukauza Paulo za nkhani imeneyo. Nthawi imeneyo, Paulo anauza mnyamatayo kuti apite kukauza mkulu wa asilikali za ciwembu cimeneco. Kodi uganiza kuti cinali copepuka kwa mnyamatayo kuti akauze mkulu wa asilikali?— Iyai, cifukwa msilikali ameneyo anali wapamwamba kwambili. Koma mwana wa mlongo wa Paulo anali wolimba mtima, ndipo iye sanaope kuuza mkulu wa asilikali za nkhani imeneyo.

Mkulu wa asilikali anadziŵa zocita. Anatumiza asilikali pafupi-fupi 500 kuti ateteze Paulo. Iye anauza asilikaliwo kuti apelekeze Paulo ku Kaisareya usiku umenewo. Kodi Paulo anapulumuka ciwembu cimeneci?— Inde, anthu oipa amenewo analephela kumupha. Ciwembu cao sicinagwile nchito.

Kodi uphunzilapo ciani pankhani imeneyi?— Iwenso ungakhale wolimba mtima monga mwana wa mlongo wa Paulo. Pamene tiuza ena za Yehova, ifenso tiyenela kukhala olimba mtima. Kodi udzakhala wolimba mtima ndi kupitilizabe kulankhula za Yehova?— Ngati ucita zimenezo, udzapulumutsa anthu ena.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO